2 Samueli 17 – CCL & CCBT

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Samueli 17:1-29

1Ahitofele anati kwa Abisalomu, “Mundilole ndisankhe asilikali 12,000, ndinyamuke usiku womwe uno kuti ndithamangire Davide. 2Ndipo ndikamuthira nkhondo atatopa ndiponso atataya mtima. Ndikamuchititsa mantha ndipo anthu onse amene ali naye akathawa. Ine ndikakantha mfumu yokhayo, 3ndipo anthu onse ndidzabwera nawo kwa inu, ngati mkwati amene akubwerera kwa mwamuna wake. Imfa ya munthu mmodzi yekha idzakhalitsa anthu onse pa mtendere.” 4Malangizo awa anaoneka abwino kwa Abisalomu ndi kwa akuluakulu onse a Israeli.

5Koma Abisalomu anati, “Muyitanenso Husai Mwariki kuti timve zimene iye adzanena.” 6Husai atabwera kwa iye, Abisalomu anati, “Ahitofele wapereka malangizo ake. Kodi tichite zimene wanena? Ngati sichoncho, tiwuze maganizo ako.”

7Husai anayankha Abisalomu kuti, “Malangizo amene Ahitofele wapereka si abwino pa nthawi ino. 8Inu mukudziwa bwino abambo anu ali ndi ankhondo awo. Iwo ndi anthu ankhondo komanso ndi woopsa ngati chimbalangondo chimene chalandidwa ana ake. Kuwonjezera apa abambo anu ndi katswiri wa nkhondo. Iwo sanagone pamodzi ndi asilikali awo. 9Onani, ngakhale tsopano lino abisala mʼphanga lina ku malo ena ake. Ngati iwo atayamba kuthira nkhondo asilikali anu, aliyense amene adzamve zimenezi adzati, ‘Gulu lalikulu lankhondo lotsatira Abisalomu laphedwa.’ 10Tsono ngakhale msilikali wolimba mtima kwambiri, amene mtima wake uli ngati wa mkango, adzagwidwa ndi mantha aakulu pakuti Aisraeli akudziwa kuti abambo anu ndi ankhondo ndipo kuti iwo amene ali nawo ndi anthu olimba mtima.

11“Kotero ine ndikukulangizani kuti: Aisraeli onse, kuchokera ku Dani mpaka ku Beeriseba; ochuluka ngati mchenga wa mʼmbali mwa nyanja, asonkhane kwa inu ndipo muwatsogolera kupita ku nkhondo. 12Ndipo ife tidzapita kukamuthira nkhondo kulikonse kumene tikamupeze, ndipo ife tikamuthira nkhondo ngati mame pa nthaka. Palibe amene adzakhale wamoyo kaya iye kapena ankhondo ake. 13Iye akakathawira mu mzinda, Aisraeli onse adzabweretsa zingwe ku mzindawo, ndipo ife tidzawugwetsera ku chigwa mpaka sipadzapezeka ngakhale kachidutswa.”

14Abisalomu ndi ankhondo ena onse a Israeli anati, “Malangizo a Husai Mwariki ndi abwino kuposa a Ahitofele.” Pakuti Yehova anatsimikiza kutsutsa malangizo onse abwino a Ahitofele ndi cholinga choti zimuvute Abisalomu.

15Husai anawuza ansembe Zadoki ndi Abiatara kuti, “Ahitofele analangiza Abisalomu ndi akuluakulu a Israeli zakuti, koma ine ndawalangiza kuchita zakutizakuti. 16Tsopano tumizani wamthenga msangamsanga kuti akamuwuze Davide kuti, ‘Musakagone powolokera Yorodani ku chipululu koma mukawoloke. Mukapanda kutero, mfumu ndi anthu onse amene ali naye adzaphedwa.’ ”

17Yonatani ndi Ahimaazi amakhala ku Eni Rogeli. Tsono wantchito wamkazi ndiye amapita kukawawuza ndipo iwo amayenera kupita kukamuwuza mfumu Davide, pakuti iwowo sankayenera kuonekera polowa mu mzinda. 18Koma mnyamata wina anawaona ndipo anakawuza Abisalomu. Kotero anthu awiriwo anachoka mofulumira ndipo anapita ku nyumba ya munthu wina ku Bahurimu. Iye anali ndi chitsime ku mpanda kwake ndipo iwo analowamo. 19Mkazi wake anatenga chophimba ndipo anachiyika pamwamba pa chitsimecho nawazapo tirigu. Palibe amene anadziwa chilichonse za izi.

20Anthu a Abisalomu atafika kwa mkaziyo pa nyumbapo anafunsa kuti, “Kodi Ahimaazi ndi Yonatani ali kuti?”

Mkaziyo anawayankha kuti, “Awoloka mtsinje.” Anthuwo anafunafuna koma sanapeze munthu, kotero anabwerera ku Yerusalemu.

21Anthu aja atapita, awiriwo anatuluka mʼchitsimemo ndipo anapita kukawuza mfumu Davide nati kwa iye, “Nyamukani, muwoloke mtsinje msangamsanga. Ahitofele wapereka malangizo akutiakuti kutsutsana nanu.” 22Kotero Davide ndi anthu onse amene anali nawo ananyamuka ndi kuwoloka Yorodani. Pofika mmamawa, panalibe munthu amene anatsala asanawoloke Yorodani!

23Ahitofele ataona kuti malangizo ake sanatsatidwe, iye anakwera bulu wake napita ku mzinda wa kwawo ku nyumba yake. Iye anakonza mʼnyumba mwakemo ndi kudzimangirira. Kotero anafa nayikidwa mʼmanda a abambo ake.

24Davide anapita ku Mahanaimu, ndipo Abisalomu anawoloka Yorodani pamodzi ndi ankhondo ena onse a Israeli. 25Abisalomu anasankha Amasa kukhala mkulu wa ankhondo mʼmalo mwa Yowabu. Amasa anali mwana wa munthu wotchedwa Itira Mwisraeli amene anakwatira Abigayeli mwana wa Nahasi mlongo wake wa Zeruya, amayi ake a Yowabu. 26Aisraeli ndi Abisalomu anamanga zithando mʼdziko la Giliyadi.

27Davide atafika ku Mahanaimu, Sobi mwana wa Nahasi wochokera ku Raba ku dziko la Amoni ndi Makiri mwana wa Amieli wochokera ku Lodebara, ndi Barizilai Mgiliyadi wochokera ku Rogelimu 28anabweretsa zofunda, mabeseni ndi miphika. Iwo anabweretsanso kwa Davide ndi anthu ake zakudya izi: tirigu ndi barele, ufa ndi tirigu wokazinga, nyemba ndi mphodza, 29uchi ndi chambiko, nkhosa ndi mafuta olimba a mkaka wangʼombe. Pakuti anati, “Anthuwa ali ndi njala ndipo atopa, alinso ndi ludzu muno mʼchipululu.”

Chinese Contemporary Bible (Traditional)

撒母耳記下 17:1-29

亞希多弗計謀落空

1亞希多弗押沙龍說:「讓我挑選一萬二千人,今夜啟程追趕大衛2趁他疲憊無力的時候襲擊他,使他驚慌失措,他的部下必逃命。我只把王一個人殺掉, 3把他的部下全都帶來歸順你。你尋索的人既然死了,跟隨他的人必然會歸順你。這樣,大家就平安無事了。」 4押沙龍以色列的長老都贊成這個提議。

5押沙龍說:「召亞基戶篩進來,我們也聽聽他的意見。」 6戶篩來了,押沙龍就把亞希多弗的建議告訴他,問他:「我們應該照亞希多弗的提議去做嗎?如果不可行,說說你的看法吧。」 7戶篩答道:「亞希多弗這次的主意不好! 8你知道你父親和他的部下,他們都是勇士,現在他們就像丟了熊崽的母熊一樣兇猛。況且你父親是個身經百戰的人,他一定不會跟部下睡在一處。 9他現在可能藏在山洞或某個地方。要是他襲擊我們的人馬,聽見的人會說押沙龍的軍隊慘敗了。 10那時候,你手下的人再膽量過人,也會膽戰心驚。因為全以色列都知道你父親是英雄,他的部下都是勇士。 11因此,我認為你應該把從別示巴的那多如海沙的以色列人都聚集起來,然後你親自率領他們出征。 12這樣不管在哪裡找到大衛,我們就像露水一樣鋪天蓋地襲擊他,讓他全軍覆沒。 13如果大衛退進一座城裡,我們以色列全軍就拿繩索把那城拉到河谷,連一塊石頭都不留。」

14押沙龍以色列眾人都說:「亞基戶篩的主意比亞希多弗的好!」其實是耶和華決定破壞亞希多弗的巧計,好把災禍降在押沙龍身上。

15戶篩亞希多弗和自己為押沙龍以色列長老所提的建議告訴祭司撒督亞比亞他16並說:「你們現在快派人去通知大衛,告訴他今晚不可在曠野的渡口過夜,務必要渡過約旦河,免得他和部下全軍覆沒。」

17當時,約拿單亞希瑪斯躲在隱·羅結,不敢進城,怕被人看見。有一個婢女從城中出來給他們報信,他們便去通知大衛王。 18不料,有一個少年發現了他們,就去告訴押沙龍。他們二人急忙逃走,來到巴戶琳的一戶人家,藏到那家院子裡的一口井內, 19那家的婦人用蓋子蓋上井口,然後在上面撒了一些麥子,沒有人知道這件事。 20押沙龍的部下來到婦人家查問約拿單亞希瑪斯的下落,婦人說他們已經過河了。押沙龍的部下就去搜索,結果一無所獲,就返回耶路撒冷21押沙龍的部下離開後,約拿單亞希瑪斯便從井裡爬出來,去向大衛王報信,把亞希多弗的計謀告訴他,請他趕快渡過約旦河。 22大衛王和部下就動身過約旦河,在黎明之前,所有的人都過去了。

23亞希多弗見自己的提議不被接納,便備上驢,啟程回鄉,安頓好家事以後,就自縊身亡了。他被安葬在他父親的墓穴裡。

24大衛來到瑪哈念押沙龍也率領以色列全軍渡過了約旦河。 25押沙龍任命亞瑪撒為元帥,代替約押的位置。亞瑪撒以實瑪利以特拉的兒子,母親是拿轄的女兒亞比該亞比該約押的母親洗魯雅是姊妹。 26押沙龍以色列人在基列地區安營。

27大衛來到瑪哈念,受到亞捫拉巴拿轄的兒子朔比羅·底巴亞米利的兒子瑪吉基列羅基琳巴西萊的熱情招待。 28他們帶來被褥、碗盆、瓦器、小麥、大麥、麵粉、炒麥、豆子、扁豆、 29蜂蜜、奶油、綿羊和乳酪,送給大衛和跟隨他的人,因為他們想:「眾人在曠野跋涉,一定饑渴疲乏了。」