2 Samueli 16 – CCL & NVI

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Samueli 16:1-23

Davide ndi Ziba

1Davide atapitirira pangʼono pamwamba pa phiri, anakumana ndi Ziba mtumiki wa Mefiboseti akudikira kuti akumane naye. Iye anali ndi abulu a chishalo pa msana ndipo ananyamula malofu a buledi 200, ntchintchi 100 za mphesa zowuma, zipatso za pa nthawi yachilimwe 100 ndi thumba la vinyo.

2Mfumu inafunsa Ziba kuti, “Nʼchifukwa chiyani wabweretsa izi?”

Ziba anayankha kuti, “Abuluwa ndi oti anthu a mʼbanja mwanu akwerepo, buledi ndi zipatso ndi za anthu anu kuti adye, ndipo vinyoyo ndi woti atsitsimutse anthu amene atope mʼchipululu.”

3Kenaka mfumu inafunsa kuti, “Kodi chidzukulu cha mbuye wako chili kuti?”

Ziba anati kwa iye, “Watsalira ku Yerusalemu chifukwa akuganiza kuti, ‘Lero Aisraeli andibwezera ufumu wa agogo anga.’ ”

4Ndipo mfumu inati kwa Ziba, “Zonse zimene zinali za Mefiboseti ndi zako tsopano.”

Ziba anati, “Ine modzichepetsa ndikukugwandirani, mbuye wanga mfumu, kuti ndipeze chisomo pamaso panu.”

Simei Atukwana Davide

5Mfumu Davide itayandikira Bahurimu, munthu wochokera ku fuko limodzi ndi banja la Sauli anabwera kuchokera mʼmenemo. Dzina lake linali Simei, mwana wa Gera ndipo amatukwana pamene amabwera. 6Iye amagenda Davide miyala ndi akuluakulu onse a mfumu, ngakhale kuti ankhondo onse ndi oteteza Davide anali ali kumanzere ndi kumanja kwake. 7Potukwana, Simeiyo amati, “Choka iwe, choka iwe, munthu wopha anthu, munthu wachabechabe iwe! 8Yehova wakubwezera chifukwa cha magazi onse amene unakhetsa pa nyumba ya Sauli, yemwe iwe ukulamulira mʼmalo mwake. Yehova wapereka ufumu kwa mwana wako Abisalomu. Ndipo ona mathero ako ndi amenewa chifukwa ndiwe munthu wopha anthu!”

9Ndipo Abisai mwana wa Zeruya anati kwa mfumu, “Nʼchifukwa chiyani galu wakufa uyu akutukwana mbuye wanga mfumu? Ndiloleni ndipite kuti ndikadule mutu wake.”

10Koma mfumu inati, “Inu ana a Zeruya, kodi ndikuchitireni chiyani? Ngati iye akutukwana chifukwa Yehova wamuwuza kuti, ‘Tukwana Davide,’ angafunse ndani kuti, ‘Nʼchifukwa chiyani ukuchita zimenezi?’ ”

11Tsono Davide anati kwa Abisai ndi akuluakulu ake onse, “Mwana wanga wobereka ndekha akufuna kundipha. Nanji tsono munthu wa fuko la Benjamini uyu! Musiyeni; mulekeni atukwane pakuti Yehova wachita kumuwuza kuti atero. 12Mwina Yehova adzaona mazunzo anga ndipo adzandibwezera zabwino chifukwa cha kutukwanidwa kumene ndikulandira lero.”

13Kotero Davide ndi anthu ake anapitirira kuyenda mu msewu pamene Simei amayenda mʼmbali mwa phiri moyangʼanana naye akutukwana ndi kuponya miyala pamene amayenda nʼkumamutsiranso dothi. 14Mfumu ndi anthu ake onse anafika kumene amapita atatopa kwambiri. Ndipo kumeneko anapumula.

Malangizo a Husai ndi Ahitofele

15Pa nthawi imeneyi Abisalomu ndi Aisraeli ena onse anabwera ku Yerusalemu, Ahitofele anali naye. 16Tsono Husai Mwariki bwenzi la Davide anapita kwa Abisalomu ndipo anati kwa iye, “Ikhale ndi moyo wautali mfumu! Ikhale ndi moyo wautali mfumu!”

17Abisalomu anafunsa Husai, “Kodi ichi ndi chikondi chimene ukumuonetsa bwenzi lako? Nʼchifukwa chiyani sunapite ndi bwenzi lako?”

18Husai anati kwa Abisalomu, “Ayi, ndidzakhala wake wa amene Yehova wamusankha, wosankhidwa ndi anthu awa ndi anthu onse a Israeli, ndipo ndidzakhala wake nthawi zonse. 19Kodi ndidzatumikiranso yani? Kodi sinditumikira mwana wa mfumu? Monga momwe ndinatumikira abambo anu, kotero ndidzatumikiranso inu.”

20Abisalomu anati kwa Ahitofele, “Tiwuze malangizo ako. Kodi tichite chiyani?”

21Ahitofele anayankha kuti, “Mugone ndi azikazi a abambo anu amene awasiya kuti asamalire nyumba yaufumu. Aisraeli onse adzamva kuti mwachitira abambo anu chinthu chonyansa kotheratu ndipo anthu onse amene ali ndi iwe adzalimbikitsidwa.” 22Choncho anamangira tenti Abisalomu pa denga la nyumba ndipo iye anagona ndi azikazi a abambo ake Aisraeli onse akuona.

23Tsono masiku amenewo malangizo amene Ahitofele amapereka anali ngati mawu ochokera kwa Mulungu. Umu ndi mmene Davide ndi Abisalomu amalandirira malangizo onse a Ahitofele.

Nueva Versión Internacional

2 Samuel 16:1-23

David y Siba

1Un poco más allá de la cumbre del monte, David se encontró con Siba, el criado de Mefiboset, que llevaba un par de asnos aparejados y cargados con doscientos panes, cien tortas de uvas pasas, cien tortas de higos y un odre de vino.

2—¿Qué vas a hacer con todo esto? —preguntó el rey.

Siba respondió:

—Los asnos son para que monte la familia de Su Majestad, el pan y la fruta son para que coman los soldados, y el vino es para que beban los que desfallezcan en el desierto.

3Entonces el rey preguntó:

—¿Dónde está el nieto de tu amo?

—Se quedó en Jerusalén —respondió Siba—. Él se imagina que ahora la nación de Israel le va a devolver el reino de su abuelo.

4—Bueno —respondió el rey—, todo lo que antes fue de Mefiboset ahora es tuyo.

—¡Humildemente me postro ante usted! —exclamó Siba—. ¡Que cuente yo siempre con el favor de mi señor y rey!

Simí maldice a David

5Cuando el rey David llegó a Bajurín, salía de allí un hombre de la familia de Saúl, llamado Simí, hijo de Guerá. Este se puso a maldecir 6y a tirarles piedras a David y a todos sus oficiales, a pesar de que las tropas y la guardia real rodeaban al rey. 7En sus insultos, Simí decía al rey:

—¡Largo de aquí! ¡Asesino! ¡Canalla! 8El Señor te está dando tu merecido por haber masacrado a la familia de Saúl para reinar en su lugar. Por eso el Señor ha entregado el reino a tu hijo Absalón. Has caído en desgracia, porque eres un asesino.

9Abisay, hijo de Sarvia, dijo al rey:

—¿Cómo se atreve este perro muerto a maldecir a mi señor el rey? ¡Déjeme que vaya y le corte la cabeza!

10Pero el rey respondió:

—Esto no es asunto mío ni de ustedes, hijos de Sarvia. A lo mejor el Señor le ha ordenado que me maldiga. Y si es así, ¿quién se lo puede reclamar?

11Dirigiéndose a Abisay y a todos sus oficiales, David añadió:

—Si el hijo de mis entrañas intenta quitarme la vida, ¡qué no puedo esperar de este benjamita! Déjenlo que me maldiga, pues el Señor se lo ha mandado. 12A lo mejor el Señor toma en cuenta mi aflicción y me paga con bendiciones las maldiciones que estoy recibiendo hoy.

13David y sus hombres reanudaron el viaje. Simí, por su parte, los seguía por la ladera del monte, maldiciendo a David, tirándole piedras y levantando polvo. 14El rey y quienes lo acompañaban llegaron agotados a su destino, así que descansaron allí.

El consejo de Husay y Ajitofel

15Mientras tanto, Absalón y todos los israelitas que lo seguían habían entrado en Jerusalén; también Ajitofel lo acompañaba. 16Entonces Husay, el arquita amigo de David, fue a ver a Absalón y exclamó:

—¡Viva el rey! ¡Viva el rey!

17Absalón preguntó:

—¿Así muestras tu lealtad a tu amigo? ¿Cómo es que no te fuiste con él?

18—De ningún modo —respondió Husay—. Soy más bien amigo del elegido del Señor, elegido también por este pueblo y por todos los israelitas. Así que yo me quedo con usted. 19Además, ¿a quién voy a servir? Serviré al hijo, como antes serví al padre.

20Luego dijo Absalón a Ajitofel:

—Danos tu consejo. ¿Qué debemos hacer?

21Ajitofel respondió:

—Acuéstese usted con las concubinas16:21 Véase nota en Gn 22:24. que su padre dejó al cuidado del palacio. De ese modo, todos los israelitas se darán cuenta de que usted se ha hecho odioso ante su padre, y quienes lo apoyan a usted se fortalecerán en el poder.

22Entonces instalaron una tienda de campaña en la azotea para que Absalón se acostara con las concubinas de su padre a la vista de todos los israelitas.

23En aquella época, recibir el consejo de Ajitofel era como oír la palabra misma de Dios y esto era así tanto para David como para Absalón.