2 Petro 1 – CCL & CCBT

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Petro 1:1-21

1Ndine Simoni Petro, mtumiki ndi mtumwi wa Yesu Khristu.

Kwa anthu amene analandira chikhulupiriro cha mtengowapatali chomwe ifenso tinalandira chifukwa cha chilungamo cha Mulungu ndi Mpulumutsi wathu Yesu Khristu.

2Chisomo ndi mtendere zochuluka zikhale nanu pomudziwa Mulungu ndi Yesu Ambuye athu.

Kudziwa za Mayitanidwe ndi za Kusankhidwa Kwathu

3Mulungu mwa mphamvu zake anatipatsa zonse zofunika kukhala moyo opembedza, potidziwitsa za Iyeyo amene anatiyitana ku ulemerero wake ndi ubwino wake. 4Mwa ulemerero ndi ubwino wakewo, anatipatsa malonjezo opambana kwambiri ndi a mtengowapatali. Amenewa ndi malonjezo amene amakuthandizani kulandira nawo moyo wa Mulungu, titapulumuka ku chiwonongeko chimene chili mʼdziko lapansi chifukwa cha zilakolako zoyipa.

5Choncho, chitani khama kuwonjezera moyo wabwino pa chikhulupiriro chanu, ndipo pa moyo wabwino muwonjezerepo nzeru. 6Pa nzeru muwonjezerepo kudziretsa, pa kudziretsa muwonjezerepo chipiriro, ndipo pa chipiriro muwonjezerepo khalidwe lolemekeza Mulungu. 7Pa khalidwe lolemekeza Mulungu muwonjezerepo chifundo cha ubale, pa chifundo cha ubale muwonjezerepo chikondi. 8Ngati zonsezi zikhala mwa inu nʼkumachuluka, zidzakuthandizani kuti musakhale aulesi ndi osapindula ndi chidziwitso chanu cha Ambuye athu Yesu Khristu. 9Koma ngati wina alibe zimenezi, ndi wakhungu sangathe kuona patali, ndipo wayiwala kuti anayeretsedwa machimo ake akale.

10Nʼchifukwa chake abale anga, funitsitsani kuti mayitanidwe ndi masankhidwe anu akhale otsimikizika. Pakuti ngati muchita zinthu izi, simudzagwa konse. 11Mudzalandiridwa bwino kwambiri mu ufumu wosatha wa Ambuye ndi Mpulumutsi wathu Yesu Khristu.

Kukhala Oyera Mtima

12Tsono ine ndidzakukumbutsani nthawi zonse za zinthu zimenezi, ngakhale kuti mumazidziwa ndipo kuti munakhazikika mʼchoonadi chimene muli nacho tsopano. 13Ndikuganiza kuti nʼkoyenera ndikanali mu msasa uno, kuti ndikutsitsimutseni ndi kukukumbutsani, 14chifukwa ndikudziwa kuti posachedwapa ndikuchoka mu msasa uno, monga Ambuye athu Yesu Khristu anandidziwitsiratu. 15Ndipo ndidzayesetsa kuti nditachoka, mudzakumbukire nthawi zonse.

16Ife sitinatsate nkhani zongopeka titakuwuzani za mphamvu zake ndi zakubweranso kwa Ambuye athu Yesu Khristu, koma tinaona ndi maso athu za ukulu wake. 17Pakuti Iye analandira ulemu ndi ulemerero kuchokera kwa Mulungu Atate atamufikira mawu ochokera ku ulemerero wa ukulu akuti, “Uyu ndi mwana wanga amene Ine ndimukonda, amene ndimakondwera naye kwambiri.” 18Ifeyo tinamva mawuwa akuchokera kumwamba pamene tinali naye pamodzi pa phiri lopatulika lija.

19Tsono ifenso tili ndi mawu a uneneri amene ndi odalirika kwambiri ndipo inu mudzachita bwino mukawasamalira mawuwa, monga kuwunika kumene kukuwala mu mdima, mpaka tsiku lidzayambe kucha, pamene nthanda idzayambe kuwala mʼmitima mwanu. 20Kuposa zonse, inu muyenera kuzindikira kuti palibe mawu a uneneri amene amatanthauzidwa pa okha. 21Pakuti mawu a uneneri sanadze mwa kufuna kwa anthu, koma anthu anayankhula zochokera kwa Mulungu, Mzimu Woyera atawayankhulitsa.

Chinese Contemporary Bible (Traditional)

彼得後書 1:1-21

1我是耶穌基督的奴僕和使徒西門·彼得,寫信給藉著我們的上帝和救主耶穌基督的義,與我們得到同樣寶貴信心的人。

2願你們因認識上帝和我們主耶穌而得到豐富的恩典和平安!

追求長進

3因為我們認識了用自己的榮耀和美德呼召我們的上帝,上帝以祂神聖的能力將生命與敬虔所需要的一切賜給了我們。 4藉此,祂已將既寶貴又偉大的應許賞給了我們,使我們脫離世上私慾帶來的敗壞,能夠有份於上帝的性情。

5正因如此,你們要加倍努力,不僅要有信心,還要有好的德行;不僅要有好的德行,還要有知識; 6不僅要有知識,還要有節制;不僅要有節制,還要有忍耐;不僅要有忍耐,還要有敬虔; 7不僅要有敬虔,還要有愛弟兄姊妹的心;不僅要有愛弟兄姊妹的心,還要有愛眾人的心。 8如果充分具備了這些品德,你們對我們主耶穌基督的認識就不會停滯不前,毫無收穫。 9缺乏上述品德的人不是瞎眼就是目光短淺,忘記他從前的罪已經得到潔淨。

10所以,弟兄姊妹,你們要更加努力,以確定自己蒙了呼召和揀選。這樣,你們就絕不會失足犯罪, 11進入我們的主和救主耶穌基督永恆國度的大門必為你們敞開。

12雖然你們已經知道這些事,並且在所領受的真道上也很堅固,但我還是要常常提醒你們。 13我覺得應當趁著我還在世的時候1·13 還在世的時候」希臘文是「還在這帳篷裡的時候」,作者用帳篷代表自己的身體。提醒你們,激勵你們, 14因我知道自己離世的日子已經不遠了,正如我們的主耶穌基督指示我的。 15我要盡力使你們在我離世以後仍然常常記得這些事。

見證基督的榮耀

16我們從前告訴你們有關主耶穌基督的大能和祂降臨的事,並非根據巧妙虛構的神話,而是我們親眼見過祂的威榮。 17祂從父上帝那裡得到了尊貴和榮耀,那時從極大的榮光中有聲音對祂說:「這是我的愛子,我甚喜悅祂。」 18當時我們和祂一同在聖山上,親耳聽見了這來自天上的聲音。

19這使我們更加確信先知的預言。你們要留意這些預言,把這些預言看作照耀在黑暗中的明燈,一直到天破曉、晨星在你們心中升起。 20你們首先該知道:聖經上的一切預言都不可隨人的私意解釋, 21因為預言絕非出於人的意思,都是人受了聖靈的感動,講出上帝的信息。