2 Mbiri 8 – CCL & NRT

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Mbiri 8:1-18

Ntchito Zina za Solomoni

1Patatha zaka makumi awiri, ndiye nthawi imene Solomoni anamanga Nyumba ya Mulungu ndi nyumba yake yaufumu, 2Solomoni anamanganso midzi imene anapatsidwa ndi Hiramu, ndipo anakhazikamo Aisraeli. 3Kenaka Solomoni anapita kukalanda Hamati-zoba. 4Iye anamanganso Tadimori ku chipululu ndi mizinda yonse yosungiramo chuma, imene anayimanga ku Hamati. 5Anamanganso Beti-Horoni Wakumtunda ndi Beti-Horoni Wakumunsi, mizinda yotetezedwa yokhala ndi makoma, zitseko ndi zitsulo zotchingira, 6pamodzinso ndi Baalati ndi mizinda yake yonse yosungira chuma, ndiponso mizinda yonse yosungiramo magaleta ake ndi akavalo ndi chilichonse anafuna kumanga ku Yerusalemu, ku Lebanoni ndi ku madera onse amene iye ankalamulira.

7Panali anthu amene anatsala pakati pa mitundu ya Ahiti, Aamori, Aperezi, Ahivi ndi Ayebusi (anthu awa sanali Aisraeli). 8Zimenezi ndiye zinali zidzukulu zawo zotsalira mʼdzikoli, anthu amene Aisraeli sanathe kuwawononga kotheratu. Solomoni anawatenga ndi kukhala akapolo ake ogwira ntchito yathangata, monga zilili mpaka lero lino. 9Koma Solomoni sanagwiritse ntchito ya ukapolo Aisraeli; Iwo anali anthu ake ankhondo, atsogoleri a ankhondo, olamulira magaleta ndi oyendetsa magaleta ake. 10Amenewa ndiwo anali akuluakulu oyangʼanira ntchito za mfumu Solomoni. Onse amene ankayangʼanira anthu analipo 250.

11Solomoni anabweretsa mwana wamkazi wa Farao mu mzinda wa Davide ku nyumba yaufumu yomwe anamumangira, pakuti iye anati, “Mkazi wanga asakhale mʼnyumba yaufumu ya Davide mfumu ya Israeli, chifukwa malo amene Bokosi la Chipangano la Yehova lafikira ndi opatulika.”

12Solomoni anapereka nsembe zopsereza pa guwa lansembe la Yehova limene anamanga patsogolo pa khonde la polowera, 13monga momwe zinkafunikira pa tsiku lililonse. Ankapereka nsembezo potsata malamulo a Mose okhudza chikondwerero cha Masabata, chikondwerero cha Mwezi Watsopano ndi zikondwerero zitatu za pa chaka: Chikondwerero cha Buledi Wopanda yisiti, Chikondwerero cha Masabata ndi Chikondwerero cha Misasa. 14Potsata malangizo a Davide abambo ake, iye anayika ansembe mʼmagulumagulu monga mwa ntchito zawo ndipo anayika Alevi kukhala otsogolera matamando ndi kuthandiza ansembe pa zofunika pa tsiku lililonse. Iye anasankhanso magulumagulu a alonda a pa zipata zosiyanasiyana, chifukwa izi ndi zimene munthu wa Mulungu, Davide analamula. 15Anthu sanapatukepo pa zimene mfumu inalamula ansembe kapena Alevi pa china chilichonse, kuphatikiza za chuma.

16Ntchito yonse ya Solomoni inachitika kuyambira tsiku limene maziko a Nyumba ya Mulungu anakhazikitsidwa mpaka kumaliza. Kotero Nyumba ya Yehova inamalizidwa.

17Kenaka Solomoni anapita ku Ezioni-Geberi ndi Eloti, mʼmbali mwa nyanja ku Edomu. 18Ndipo Hiramu anatumiza sitima zapamadzi zoyendetsedwa ndi antchito ake, antchito amene ankayidziwa bwino nyanja. Awa pamodzi ndi anthu a Solomoni, anayenda pa madzi kupita ku Ofiri ndipo anakatengako golide olemera makilogalamu 18,000 amene anabwera naye kwa mfumu Solomoni.

New Russian Translation

2 Паралипоменон 8:1-18

Другие дела Соломона

(3 Цар. 9:10-28)

1По истечении двадцати лет, в которые Соломон строил Господень дом и свой дворец, 2Соломон отстроил города, которые дал ему Хирам, и поселил в них израильтян. 3Затем Соломон пошел к Хамат-Цове и захватил его. 4Еще он построил Тадмор в пустыне и все города для хранения запасов, которые он основал в Хамате. 5Он отстроил Верхний Бет-Хорон и Нижний Бет-Хорон, сделав их городами-крепостями со стенами и воротами на засовах. 6Он также отстроил Баалаф, все другие города для хранения запасов и все города для своих колесниц и коней8:6 Или: «колесничих»; или: «всадников».. Соломон построил все, что ему хотелось построить в Иерусалиме, на Ливане и во всех землях, которыми он правил.

7Весь народ, оставшийся от хеттов, аморреев, ферезеев, хиввеев и иевусеев (все они не были израильтянами), 8то есть их потомков, оставшихся в стране, которых израильтяне не искоренили, Соломон использовал подневольными рабочими, как это есть и до сегодняшнего дня. 9Но израильтян Соломон не обращал в рабов, выполняющих его работы; они были его воинами, военачальниками и начальниками его колесниц и колесничих. 10Еще они были у него главными распорядителями – двести пятьдесят надсмотрщиков над людьми.

11Соломон переселил дочь фараона из Города Давида во дворец, который он построил для нее, так как он сказал: «Моя жена не должна жить во дворце Давида, царя Израиля, потому что святы места, куда вносили ковчег Господа».

12На жертвеннике Господа, который он построил напротив притвора храма, Соломон возносил Господу всесожжения 13по установлениям каждого дня о приношениях, данным Моисеем по субботам, в праздник Новолуния и в три ежегодных праздника – в праздник Пресных хлебов, в праздник Недель и в праздник Шалашей. 14По приказу своего отца Давида он назначил отделения священников для несения службы и левитов, чтобы они возносили хвалу и помогали священникам выполнять то, что требовалось по установлениям каждого дня. Еще он поставил привратников по отделениям у каждых ворот, потому что так повелел Божий человек Давид. 15Повеления царя священникам и левитам о чем бы то ни было, включая указания о хранении сокровищ, были исполнены в точности.

16Вся работа Соломона со дня закладки основания Господнего дома до дня его завершения была выполнена. Итак, дом Господа был завершен.

17Тогда Соломон отправился в Эцион-Гевер и в Элат на морском побережье, что в земле Эдома. 18Хирам прислал ему корабли, которые вели его слуги, знавшие море. Вместе с людьми Соломона они отплыли в Офир и привезли оттуда четыреста пятьдесят талантов8:18 Около 16 т. золота, которое и доставили царю Соломону.