2 Mbiri 7 – CCL & HTB

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Mbiri 7:1-22

Mwambo Wopereka Nyumba kwa Yehova

1Solomoni atamaliza kupemphera, moto unatsika kuchokera kumwamba ndi kutentha nsembe zopsereza ndi nsembe zina, ndipo ulemerero wa Yehova unadzaza Nyumba ya Mulunguyo. 2Ansembe sanathe kulowa mʼNyumba ya Mulungu chifukwa munadzaza ulemerero wa Yehova. 3Aisraeli onse ataona moto ukuchokera kumwamba ndi ulemerero wa Yehova pamwamba pa Nyumba ya Mulungu, anagwada poyalidwa miyalapo ndipo anagunditsa nkhope zawo pansi, ndi kulambira ndi kutamanda Yehova, ponena kuti,

“Iye ndi wabwino;

chikondi chake chikhala chikhalire”

4Tsono mfumu ndi anthu onse anapereka nsembe pamaso pa Yehova. 5Ndipo mfumu Solomoni anapereka nsembe ngʼombe 22,000, nkhosa ndi mbuzi 120,000. Kotero mfumu ndi anthu onse anachita mwambo wopereka Nyumba kwa Mulungu. 6Ansembe anayimirira mʼmalo mwawo, monganso anachitira Alevi ndi zida zoyimbira za Yehova, zimene Davide anapanga zotamandira Yehova ndipo zimagwiritsidwa ntchito pamene amatamanda, ponena kuti, “Chikondi chake chikhale chikhalire.” Moyangʼanizana ndi Alevi, ansembe amaliza malipenga, ndipo Aisraeli onse anali atayimirira.

7Solomoni anapatula malo a pakati pa bwalo kutsogolo kwa Nyumba ya Yehova ndipo pamenepo anapereka nsembe zopsereza ndi mafuta, zopereka za chiyanjano, chifukwa guwa lansembe lamkuwa limene anapanga panalibe malo woti nʼkuperekerapo nsembe zopsereza, nsembe za ufa ndi mafuta.

8Choncho nthawi imeneyi, Solomoni anachita chikondwerero kwa masiku asanu ndi awiri pamodzi ndi Aisraeli onse. Unali msonkhano waukulu, kuyambira ku Lebo Hamati mpaka ku chigwa cha ku Igupto. 9Pa tsiku lachisanu ndi chitatu panali msonkhano, pakuti anachita mwambo wopereka guwa lansembe kwa masiku asanu ndi awiri ndi masiku enanso asanu ndi awiri achikondwerero. 10Pa tsiku la 23 la mwezi wachisanu ndi chiwiri, Solomoni anawuza anthu aja kuti apite kwawo. Anthu anali achimwemwe ndi okondwa mʼmitima mwawo chifukwa cha zinthu zabwino zimene Yehova anachitira Davide ndi Solomoni ndiponso anthu ake Aisraeli.

Yehova Aonekera Solomoni

11Solomoni atatsiriza kumanga Nyumba ya Yehova ndi nyumba yaufumu ndi kukwaniritsa kuchita zonse zimene zinali mu mtima mwake pa Nyumba ya Yehova ndi nyumba yake yaufumu, 12Yehova anamuonekera usiku ndipo anati:

“Ine ndamva pemphero lako ndipo ndadzisankhira malo ano kukhala Nyumba yanga yoperekeramo nsembe.

13“Ine ndikatseka kumwamba kuti mvula isagwe, kapena kulamulira dzombe kuti liwononge dziko, kapena kutumiza mliri pakati pa anthu, 14ngati anthu anga, amene amatchedwa ndi dzina langa adzichepetsa ndi kupemphera ndi kufunafuna nkhope yanga, nasiya njira zawo zoyipa, pamenepo Ine ndidzamva kumwamba ndipo ndidzakhululuka tchimo lawo ndi kuchiritsa dziko lawo. 15Ndipo maso anga adzatsekuka ndi makutu anga adzakhala tcheru kumva mapemphero a pamalo pano. 16Ine ndasankha ndipo ndapatula Nyumba yangayi kotero kuti ndidzakhala mʼmenemo kwamuyaya. Maso ndi mtima wanga zidzakhala pano nthawi zonse.

17“Kunena za iwe, ukayenda pamaso panga mokhulupirika monga momwe anachitira abambo ako Davide, ndi kuchita zonse zimene ndakulamula, ndi kusamalitsa malangizo ndi malamulo anga, 18Ine ndidzakhazikitsa mpando wako waufumu, monga ndinachitira pangano ndi abambo ako Davide pamene ndinati, ‘Sipadzasowa munthu wolamulira Israeli.’

19“Koma ngati iwe udzapatuka ndi kutaya malangizo ndi malamulo amene ndakupatsa ndi kupita kukatumikira milungu ina ndi kuyipembedza, 20pamenepo Ine ndidzazula Aisraeli mʼdziko langa limene ndinawapatsa, ndiponso ndidzayikana Nyumba ino imene ndadzipatulira. Ndipo udzakhala ngati mwambi ndi chinthu chonyozedwa pakati pa anthu onse. 21Ndipo ngakhale kuti tsopano Nyumba ya Mulunguyi ndi yokongola kwambiri, onse amene adzadutsa pano adzadabwa kwambiri ndipo adzati, ‘Nʼchifukwa chiyani Yehova wachita chinthu chotere mʼdziko muno ndi pa Nyumba ya Mulunguyi?’ 22Anthu adzayankha kuti, ‘Nʼchifukwa chakuti asiya Yehova, Mulungu wa makolo awo, amene anawatulutsa mʼdziko la Igupto ndipo akangamira milungu ina ndi kumayipembedza ndi kuyitumikira. Choncho Iye wabweretsa zovuta zonsezi.’ ”

Het Boek

2 Kronieken 7:1-22

De Heerlijkheid van de Here vult de tempel

1-2 Nadat Salomo zijn gebed had beëindigd, flitste vuur vanuit de hemel naar beneden dat de offers verteerde. En de Heerlijkheid van de Here vulde de tempel, zodat de priesters niet naar binnen konden. 3Alle mensen hadden het zien gebeuren en knielden met gebogen hoofd om de Here te aanbidden en te danken. Zij riepen uit: ‘Hij is goed en zijn goedheid en liefde duren tot in eeuwigheid!’

4-5 Daarna wijdden de koning en zijn onderdanen de tempel in door brandoffers aan de Here te offeren. Koning Salomoʼs bijdrage daaraan bedroeg tweeëntwintigduizend ossen en honderdtwintigduizend schapen. 6De priesters stonden op hun normale posten en de Levieten speelden een lied om de Here te danken voor zijn eeuwigdurende goedheid. Daarvoor gebruikten zij de muziekinstrumenten die koning David zelf had gemaakt en had gebruikt om de Here te loven. Toen de priesters op de trompetten bliezen, bleef iedereen staan. 7Salomo heiligde de binnenhof van de tempel, zodat deze die dag kon worden gebruikt als offerplaats, want het koperen altaar kon de vele offers niet verwerken. 8De zeven dagen die volgden, werden gebruikt voor de viering van het loofhuttenfeest. Vanuit heel Israël kwamen grote groepen mensen en onder hen waren er zelfs uit Hamath in het uiterste noorden en uit de buurt van de grens met Egypte in het uiterste zuiden. 9Zeven dagen lang werd dit feest van de inwijding van de tempel gevierd, op de achtste dag werd een plechtige bijeenkomst gehouden en vervolgens vierden ze zeven dagen lang het loofhuttenfeest. 10Op de drieëntwintigste dag van de zevende maand stuurde Salomo de mensen terug naar huis. Iedereen was blij en opgewekt, omdat de Here zo goed was geweest voor David, Salomo en zijn volk Israël.

11Toen Salomo de bouw van de tempel en van zijn eigen paleis voltooid had en alles had gedaan wat hij zich had voorgenomen, 12verscheen de Here hem in de nacht en zei: ‘Ik heb uw gebed gehoord en deze tempel gekozen als de plaats waar u Mij uw offers mag brengen. 13Als Ik de hemel sluit zodat er geen regen valt of als Ik de sprinkhanenzwermen beveel dat zij al uw oogsten moeten opeten of als Ik de pest onder u laat uitbreken 14en mijn volk zich vernedert en bidt, Mij weer zoekt en breekt met zijn zondige praktijken, dan zal Ik vanuit de hemel luisteren, zijn zonden vergeven en het land weer gezond maken. 15-16 Ik zal aandachtig luisteren naar elk gebed dat wordt uitgesproken op deze plaats die Ik heb uitgekozen en afgezonderd als mijn eeuwige woonplaats, mijn ogen en mijn hart zullen daar voor altijd zijn. 17En wat uzelf betreft: als u Mij volgt zoals uw vader David deed, 18zal Ik ervoor zorgen dat u en uw nakomelingen voor altijd koningen van Israël blijven. 19Maar als u Mij niet volgt en de wetten die Ik u gaf, niet naleeft en afgoden aanbidt, 20zal Ik mijn volk wegjagen uit dit land dat Ik het gaf en zal deze tempel worden verwoest, ook al heb Ik hem voor mijzelf geheiligd. Ik zal er dan een afschrikwekkend voorbeeld van maken, een plaats die het onderwerp wordt van spot en kwaadsprekerij. 21Dan zal die plaats niet langer beroemd zijn. Nee, de mensen die er voorbijkomen, zullen zich vol verbazing afvragen: “Waarom heeft de Here zoiets vreselijks gedaan met dit land en deze tempel?” 22En het antwoord zal dan luiden: “Omdat de Israëlieten de Here, de God van hun voorouders de rug toekeerden—de God die hen uit het land Egypte bevrijdde—en zij in plaats van Hem andere goden vereerden. Daarom heeft Hij deze vreselijke ramp over hen gebracht.” ’