2 Mbiri 36 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Mbiri 36:1-23

1Tsono anthu a mʼdzikomo anatenga Yehowahazi mwana wa Yosiya namuyika kukhala mfumu mu Yerusalemu mʼmalo mwa abambo ake.

Yehowahazi Mfumu ya Yuda

2Yowahazi anali wa zaka 23 pamene anakhala mfumu ndipo analamulira mu Yerusalemu kwa miyezi itatu. 3Mfumu ya Igupto inamuchotsa pa udindo wa ufumu mu Yerusalemu ndipo inakhometsa msonkho dziko la Yuda wa makilogalamu 3,400 asiliva ndi agolide. 4Mfumu ya Igupto inakhazika Eliyakimu, mʼbale wake wa Yehowahazi kukhala mfumu ya Yuda ndi Yerusalemu ndipo anasintha dzina la Eliyakimu kukhala Yehoyakimu. Koma Neko anatenga Yowahazi mʼbale wake wa Eliyakimu ndi kupita naye ku Igupto.

Yehoyakimu Mfumu ya Yuda

5Yehoyakimu anali wa zaka 25 pamene anakhala mfumu, ndipo analamulira mu Yerusalemu zaka 11. Iye anachita zoyipa pamaso pa Yehova Mulungu wake. 6Nebukadinezara, mfumu ya ku Babuloni anachita naye nkhondo ndipo anamumanga ndi zingwe zamkuwa ndi kumutenga kupita naye ku Babuloni. 7Nebukadinezara anatenganso zipangizo za ku Nyumba ya Yehova kupita nazo ku Babuloni ndipo anaziyika mʼnyumba ya Mulungu wake kumeneko.

8Zochitika zina za pa ulamuliro wa Yehoyakimu, zinthu zonyansa zimene anachita ndi zonse zinapezeka kuti zinali zomutsutsa zalembedwa mʼbuku la mafumu a Israeli ndi Yuda. Ndipo Yehoyakini mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake.

Yehoyakini Mfumu ya Yuda

9Yehoyakini anali ndi zaka 21 pamene anakhala mfumu ndipo analamulira mu Yerusalemu kwa miyezi itatu ndi masiku khumi. Iye anachita zoyipa pamaso pa Yehova. 10Nthawi ya mphukira, mfumu Nebukadinezara inayitanitsa Yehoyakini ndipo inapita naye ku Babuloni, pamodzi ndi ziwiya zamtengowapatali za mʼNyumba ya Mulungu wa Yehova, ndipo anayika Zedekiya malume wake kukhala mfumu ya Yuda ndi Yerusalemu.

Zedekiya Mfumu ya Yuda

11Zedekiya anali ndi zaka 21 pamene ankakhala mfumu, ndipo analamulira mu Yerusalemu zaka 11. 12Iye anachita zoyipa pamaso pa Yehova Mulungu wake ndipo sanadzichepetse yekha pamaso pa mneneri Yeremiya amene ankayankhula mawu a Yehova. 13Iye anawukiranso mfumu Nebukadinezara amene anamulumbiritsa mʼdzina la Mulungu. Iyeyo anali wosamva ndipo anawumitsa mtima wake. Sanatembenukire kwa Yehova Mulungu wa Israeli. 14Kuwonjezera apo, atsogoleri onse a ansembe ndi anthu ena anapitirapitira kukhala osakhulupirika, kutsatira machitidwe onse onyansa a mitundu ina ndi kudetsa Nyumba ya Yehova Mulungu wawo, imene anayipatula mu Yerusalemu.

Kugwetsedwa kwa Yerusalemu

15Yehova, Mulungu wa makolo awo, ankatumiza mawu kwa iwo kudzera kwa amithenga ake kawirikawiri, chifukwa ankawamvera chisoni anthu ake ndi malo ake okhalapo. 16Koma iwo ananyoza amithenga a Mulungu, anapeputsa mawu awo ndipo ankaseka aneneri ake mpaka anawutsa mkwiyo wa Yehova pa anthu ake ndipo panalibenso mankhwala owachiritsa. 17Yehova anabweretsa mfumu ya anthu a ku Babuloni, imene inapha anyamata awo ndi lupanga ku malo opatulika, ndipo sanasiye kaya mnyamata kapena mtsikana, wamkulu kapena wokalamba. Mulungu anapereka onsewo kwa Nebukadinezara. 18Iye ananyamula kupita nazo ku Babuloni zipangizo zonse za mʼNyumba ya Yehova Mulungu wawo, zazikulu ndi zazingʼono zomwe, ndi chuma cha mʼNyumba ya Yehova ndiponso chuma cha mfumu ndi akuluakulu ake. 19Iwo anayatsa moto Nyumba ya Mulungu, ndipo anagwetsa makoma a Yerusalemu. Anatentha moto nyumba zonse zaufumu ndipo anawononga chilichonse chimene chinali chofunika.

20Iye anagwira ukapolo anthu otsala amene anapulumuka ku lupanga ndi kupita nawo ku Babuloni, ndipo anakhala antchito ake ndi ana ake mpaka pamene ufumu wa Peresiya unakhazikitsidwa. 21Dziko linakondwera ndi masabata ake. Pa nthawi yonse ya chipasuko chake nthaka inapuma, mpaka zaka 70 zinakwana pokwaniritsa mawu a Yehova amene anayankhula kudzera mwa Yeremiya.

22Mʼchaka choyamba cha Koresi mfumu ya Peresiya, pofuna kukwaniritsa mawu a Yehova amene anayankhula kudzera mwa Yeremiya, Yehova anakhudza mtima wa mfumu ya Peresiya kuti alengeze mu ufumu wake wonse ndipo anazilemba:

23Chimene mfumu Koresi ya Peresiya ikunena ndi ichi:

“Yehova, Mulungu wakumwamba wandipatsa ine mafumu onse a dziko lapansi ndipo wandisankha kuti ndimumangire Nyumba ya Mulungu ku Yerusalemu ku Yuda. Aliyense wa anthu ake pakati panu, Yehova Mulungu wake akhale naye, ndipo apite.”