2 Mbiri 35 – CCL & CCBT

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Mbiri 35:1-27

Yosiya Achita Chikondwerero cha Paska

1Yosiya anachita chikondwerero cha Paska wa Yehova mu Yerusalemu, ndipo mwana wankhosa wa Paska anaphedwa pa tsiku la khumi ndi chinayi la mwezi woyamba. 2Iye anasankha ansembe pa maudindo awo ndipo anawalimbikitsa pa ntchito ya mʼnyumba ya Yehova. 3Iye anati kwa Alevi amene amalangiza Aisraeli onse omwe anadzipatula kwa Yehova: Ikani bokosi lopatulika mʼNyumba ya Mulungu amene Solomoni mwana wa Davide mfumu ya Israeli anamanga. Lisamanyamulidwe pa mapewa anu. Tsopano tumikirani Yehova Mulungu wanu ndi anthu ake Aisraeli. 4Mukhale mʼmagulu anu molingana ndi mabanja anu, molingana ndi momwe analembera Davide mfumu ya Israeli ndiponso mwana wake Solomoni.

5“Muziyima ku malo opatulika pamodzi ndi gulu la Alevi oyimira gulu lililonse lalingʼono la mabanja a abale anu amene ndi anthu wamba. 6Muzipha ana ankhosa a Paska, muzidzipatula nokha ndi kuwakonzera abale anu ana ankhosa awo, kuchita zimene Yehova analamulira mwa Mose.”

7Yosiya anapereka kwa anthu wamba onse ana ankhosa ndi ana ambuzi okwanira 30,000 ndi ngʼombe zazimuna 3,000, zopereka za Paska zonse zochokera pa chuma chake cha mfumu.

8Akuluakulu akenso anapereka mwaufulu kwa anthu ndi kwa ansembe ndi Alevi. Hilikiya, Zekariya ndi Yehieli oyangʼanira ntchito ya mʼNyumba ya Mulungu anapereka kwa ansembe zopereka za Paska 2,600 ndi ngʼombe 300. 9Konaniya nayenso pamodzi ndi Semaya ndi Netaneli, abale ake ndi Hasabiya, Yeiyeli ndi Yozabadi, atsogoleri a Alevi, anapereka nsembe za Paska 5,000 ndi ngʼombe 500 kwa Alevi.

10Mwambo unakonzedwa ndipo ansembe anayima pamalo pawo pamodzi ndi Alevi mʼmagulu awo monga mfumu inalamulira. 11Ana ankhosa a Paska anaphedwa ndipo ansembe anawaza magazi amene anaperekedwa kwa iwo pamene Alevi anali kusenda nyamazo. 12Iwo anayika padera nsembe zopsereza kuti azipereke kwa magulu angʼonoangʼono a mabanja a anthu kuti apereke kwa Yehova monga zinalembedwa mʼbuku la Mose. Ndipo anachita chimodzimodzi ndi ngʼombe. 13Anawotcha nyama za Paska monga momwe zinalembedwera ndi kuwiritsa zopereka zopatulika mʼmiphika, mʼmitsuko ndi mʼziwaya ndipo anazipereka mofulumira kwa anthu onse. 14Izi zitatha, anakonza zawo ndi za ansembe chifukwa ansembe, zidzukulu za Aaroni, anali otanganidwa kupereka nsembe zopsereza ndi mafuta a nyama mpaka madzulo. Choncho Alevi amakonza zawo ndi za ansembe, ana a Aaroni.

15Anthu oyimba nyimbo, zidzukulu za Asafu, anali pa malo awo potsata zomwe analemba Davide, Asafu, Hemani ndi Yedutuni mlosi wa mfumu. Alonda apazipata anali pa chipata chilichonse ndipo kunali kosafunika kuti achoke pa ntchito yawo, poti abale awo Alevi ankawakonzera zonse.

16Kotero pa nthawi imeneyi ntchito yonse ya Yehova ya chikondwerero cha Paska ndi nsembe zopsereza pa guwa la Yehova inachitika monga analamulira mfumu Yosiya. 17Aisraeli amene analipo anachita chikondwerero cha Paska pa nthawi imeneyi ndi kuchita mwambo wa chikondwerero cha Buledi Wopanda Yisiti, kwa masiku asanu ndi awiri. 18Paska yofanana ndi iyi sinachitikepo ku Israeli kuyambira nthawi ya Samueli ndipo palibe mmodzi mwa mafumu a Israeli anachitapo chikondwerero cha Paska ngati anachitira Yosiya pamodzi ndi ansembe, Alevi ndi Ayuda onse ndi Aisraeli amene anali pamodzi ndi anthu a mu Yerusalemu. 19Chikondwerero cha Paska ichi chinachitika mʼchaka cha 18 cha ulamuliro wa Yosiya.

Imfa ya Yosiya

20Zimenezi zitachitika, pamene Yosiya anakonzanso Nyumba ya Mulungu, Neko mfumu ya Igupto inapita kukachita nkhondo ku Karikemesi ku mtsinje wa Yufurate, ndipo Yosiya anapita kukamenyana naye. 21Koma Neko anatumiza amithenga kwa iye kunena kuti, “Kodi pali mkangano wanji pakati pa iwe ndi ine, iwe mfumu ya Yuda? Ine sindikuthira nkhondo iwe pa nthawi ino, koma nyumba imene ndili nayo pa nkhondo. Mulungu wandiwuza kuti ndifulumize choncho leka kutsutsana ndi Mulungu amene ali ndi ine, mwina adzakuwononga.”

22Komabe Yosiya sanatembenuke kumusiya iyeyo, koma anadzizimbayitsa ndi kukalowa mʼnkhondo. Iye sanamvere zimene Neko ananena molamulidwa ndi Mulungu koma anapita kukamenyana naye ku chigwa ku Megido.

23Anthu oponya mivi analasa mfumu Yosiya, ndipo iye anawuza akuluakulu ake, “Chotseni. Ndavulazidwa kwambiri.” 24Choncho anamuchotsa iye mʼgaleta lake, ndipo anamuyika mʼgaleta lina limene anali nalo ndipo anabwera naye ku Yerusalemu kumene anamwalirira. Iye anayikidwa mʼmanda a makolo ake. Ndipo Ayuda ndi Yerusalemu yense anamulira.

25Yeremiya anapeka nyimbo za maliro chifukwa cha Yosiya, ndipo mpaka lero lino amuna ndi akazi onse oyimba amakumbukira Yosiya pa nyimbo zawo za maliro. Izi zinakhala mwambo mu Israeli ndipo zinalembedwa mʼNyimbo za Maliro.

26Zochitika zina za ulamuliro wa Yosiya ndi ntchito za kudzipereka kwake, monga zinalembedwa mʼMalamulo a Yehova, 27zochitika zonse, kuyambira pachiyambi mpaka pa mapeto, zalembedwa mʼbuku la mafumu a Israeli ndi Yuda.

Chinese Contemporary Bible (Traditional)

歷代志下 35:1-27

約西亞守逾越節

1約西亞耶路撒冷為耶和華守逾越節。一月十四日,眾人宰殺逾越節的祭牲。 2他指派祭司各盡其職,鼓勵他們在耶和華的殿裡事奉, 3又對將自己獻給耶和華、負責教導以色列人的利未人說:「你們把聖約櫃放在以色列大衛的兒子所羅門建的殿裡,不用再扛在肩上。現在你們去事奉你們的上帝耶和華和祂的以色列子民吧。 4你們要按宗族和班次,依照以色列大衛和他兒子所羅門所寫的指示,預備自己。 5你們要按你們弟兄所在宗族的班次,侍立在聖所,每個班次中要有幾個利未宗族的人。 6你們要宰殺逾越節的羊羔,潔淨自己,為你們的弟兄做好準備,依照耶和華藉摩西所吩咐的去行。」

7約西亞從自己的產業中,捐出三萬隻綿羊羔和山羊羔,以及三千頭公牛,賜給所有在場的人做逾越節的祭牲。 8他的眾官員也自願為民眾、祭司和利未人捐獻。管理上帝殿的希勒迦撒迦利亞耶歇獻出兩千六百隻羊羔和三百頭牛,給祭司做逾越節的祭牲。 9利未人的首領歌楠雅和他的兩個兄弟示瑪雅拿坦業,及哈沙比雅耶利約撒拔獻出五千隻羊羔和五百頭牛,給利未人做逾越節的祭牲。

10一切都準備好後,依照王的吩咐,祭司站在自己的地方,利未人按照班次侍立。 11利未人宰殺逾越節的羊羔,祭司從他們手中接過血,灑在壇上,又剝去祭牲的皮。 12他們按照宗族把燔祭分給眾人,好使他們按照摩西書上所寫的,把祭物獻給耶和華。獻牛也是這樣。 13他們按規定用火烤逾越節的羊羔,在鍋裡、罐裡和盆裡煮聖物,然後迅速分給民眾。 14之後,利未人為自己和祭司預備祭物,因為做祭司的亞倫子孫要繼續獻燔祭和脂肪一直到晚上。 15負責歌樂的亞薩子孫依照大衛亞薩希幔和王的先見耶杜頓的吩咐,站在自己的崗位上;殿門守衛都看守各門,不必離開工作崗位,因為他們的弟兄利未人為他們預備了祭物。

16當天,一切事奉的事都辦好了,他們就按約西亞王的命令守逾越節,又在耶和華的壇上獻燔祭。 17所有在場的以色列人都在那時守逾越節,又守除酵節七天。 18撒母耳先知以來,在以色列從來沒有守過這樣的逾越節,以色列從沒有君王像約西亞、祭司、利未人、所有在場的猶大人和以色列人,以及耶路撒冷的居民這樣守過逾越節。 19這次逾越節是在約西亞執政第十八年慶祝的。

約西亞逝世

20約西亞辦理完殿裡的事後,埃及尼哥上來,要攻打幼發拉底河附近的迦基米施約西亞出兵攔阻。 21尼哥派使者對約西亞說:「猶大王啊,我與你沒有恩怨。我今天來不是要攻擊你,乃是要攻擊與我作戰的那一家。上帝吩咐我要速速完成,你不要與上帝作對,免得祂毀滅你,因為上帝與我同在。」 22約西亞卻不聽上帝藉尼哥說的話。他沒有退兵,反而喬裝上陣,與尼哥會戰於米吉多平原。 23約西亞王在戰場上中箭受傷,就對僕人說:「我受了重傷,帶我離開吧。」 24他的僕人就扶他下戰車,上另一輛戰車,送到耶路撒冷約西亞死在那裡,葬在他祖先的墳墓裡。所有猶大耶路撒冷的人都為他哀悼。 25耶利米約西亞作了哀歌,所有的男女歌樂手至今仍用這些哀歌紀念約西亞,成了以色列的傳統。這些哀歌都記在《哀歌書》上。

26約西亞其他的事蹟和他怎樣忠心地遵行耶和華的律法, 27自始至終都記在《以色列和猶大的列王史》上。