2 Mbiri 33 – CCL & NRT

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Mbiri 33:1-25

Manase Mfumu ya Yuda

1Manase anali wa zaka khumi ndi ziwiri pamene anakhala mfumu, ndipo analamulira mu Yerusalemu kwa zaka 55. 2Iye anachita zoyipa pamaso pa Yehova, potsatira machitidwe a mitundu imene Yehova anayithamangitsa pamaso pa Aisraeli. 3Iyeyo anamanganso malo opembedzerapo mafano amene Hezekiya abambo ake anawaphwasula; anamanganso maguwa ansembe a Baala ndi kupanga mafano a Asera. Iye amagwadira zolengedwa zonse zamlengalenga ndi kumazipembedza. 4Manase anamanga maguwa mʼNyumba ya Yehova, mʼmene Yehova ananena kuti, “Ine ndidzakhala mu Yerusalemu mpaka muyaya.” 5Mʼmabwalo onse awiri a Nyumba ya Yehova anamangamo maguwa ansembe a zolengedwa zonse zamlengalenga. 6Iye ankakapereka ana ake aamuna ngati nsembe yopsereza ku chigwa cha Hinomu, ankachita zamatsenga, kuwombeza ndi ufiti, ankakafunsira kwa woyankhula ndi mizimu ya anthu akufa. Iye anachita zoyipa zambiri pamaso pa Yehova, kumukwiyitsa Iyeyo.

7Manase anatenga fano losema limene anapanga ndi kuliyika mʼNyumba ya Mulungu, zimene Mulungu ananena kwa Davide ndi kwa mwana wake Solomoni kuti, “Mʼnyumba ya Mulungu muno, mu Yerusalemu muno, malo amene ndawasankha pakati pa mafuko onse a Israeli, ndidzakhalamo mpaka muyaya. 8Ine sindidzachotsanso phazi la Aisraeli kuchoka mʼdziko limene ndawapatsa makolo ako, ngatitu iwowa adzasamalira kuchita chilichonse chimene ndinawalamulira za malamulo onse, malangizo ndi miyambo imene inapatsidwa kudzera mwa Mose.” 9Koma Manase anasocheretsa anthu a ku Yuda ndi Yerusalemu, kotero anachita zoyipa zambiri kupambana mitundu imene Yehova anayiwononga pamaso pa Aisraeli.

10Yehova anayankhula kwa Manase ndi anthu ake, koma iwo sanasamaleko. 11Kotero Yehova anawatumizira atsogoleri a ankhondo a ku Asiriya amene anagwira Manase ukapolo, anayika ngowe mʼmphuno mwake, namumanga ndi zingwe zamkuwa ndi kupita naye ku Babuloni. 12Ali pa mavuto akewo anafunafuna kuti Yehova Mulungu wake amukomere mtima ndipo anadzichepetsa kwakukulu pamaso pa Mulungu wa makolo ake. 13Ndipo atapemphera, Yehova anakhudzidwa ndi kupempha kwakeko ndipo anamvera madandawulo ake. Kotero anamubweretsanso ku Yerusalemu ndi ku ufumu wake. Ndipo Manase anadziwa kuti Yehova ndi Mulungu.

14Zitapita izi iye anamanga khoma la kunja kwa Mzinda wa Davide kumadzulo kwa kasupe wa Gihoni ku chigwa mpaka polowera ku Chipata cha Nsomba kuzungulira phiri la Ofeli. Iyeyo anakweza kwambiri khomalo. Anayikanso atsogoleri a nkhondo ku mizinda yonse yotetezedwa ya Yuda.

15Iye anachotsa milungu yonse yachilendo ndi fano mʼNyumba ya Yehova komanso maguwa ansembe onse amene anamanga pa phiri la Nyumba ya Mulungu ndi mu Yerusalemu, nazitayira kunja kwa mzinda. 16Kenaka anabwezeretsa guwa lansembe la Yehova ndi kupereka zopereka zachiyanjano ndiponso zopereka zamatamando ndipo anawuza Yuda kuti atumikire Yehova Mulungu wa Israeli. 17Komabe anthu anapitiriza kupereka nsembe ku malo achipembedzo, koma kwa Yehova, Mulungu wawo yekha.

18Zina ndi zina zokhudza ulamuliro wa Manase, kuphatikiza mapemphero ake kwa Mulungu wake ndi mawu amene alosi anayankhula kwa iye mʼdzina la Yehova Mulungu wa Israeli, zalembedwa mʼmabuku a mafumu a Israeli. 19Pemphero lake ndi momwe Mulungu anakhudzidwira ndi kupempha kwakeko, pamodzinso ndi machimo ake onse ndi kusakhulupirika kwake, ndiponso malo onse amene anamanga, malo azipembedzo ndi mafano a Asera ndi mafano asanadzichepetse, zonse zalembedwa mʼmbiri ya alosi. 20Manase anamwalira ndipo anayikidwa mʼmanda mʼnyumba yake yaufumu. Ndipo Amoni mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake.

Amoni Mfumu ya Yuda

21Amoni anali wa zaka 22 pamene anakhala mfumu ndipo analamulira mu Yerusalemu kwa zaka ziwiri. 22Iye anachita zoyipa pamaso pa Yehova, monga anachitira Manase abambo ake. Amoni analambira ndi kupereka nsembe kwa mafano onse amene anapanga Manase. 23Koma kusiyana ndi abambo ake Manase, iye sanadzichepetse pamaso pa Yehova. Amoni anawonjeza kulakwa kwake.

24Akuluakulu a Amoni anamuchita chiwembu ndipo anamupha mʼnyumba yake yaufumu. 25Koma anthu a mʼdzikomo anapha onse amene anakonzera chiwembu mfumu Amoni, ndipo anayika mwana wake Yosiya kukhala mfumu mʼmalo mwake.

New Russian Translation

2 Паралипоменон 33:1-25

Манассия – царь Иудеи

(4 Цар. 21:1-10, 17-18)

1Манассии было двенадцать лет, когда он стал царем, и правил он в Иерусалиме пятьдесят пять лет. 2Он делал зло в глазах Господа, следуя омерзительным обычаям народов, которых Господь прогнал от израильтян. 3Он отстроил святилища на возвышенностях, которые разрушил его отец Езекия, он воздвиг жертвенники Баалам и сделал столбы Ашеры. Он поклонялся всему небесному воинству и служил ему, 4построил жертвенники в доме Господа, о котором Господь сказал: «Мое имя пребудет в Иерусалиме вовеки». 5В обоих дворах дома Господа он построил жертвенники всему небесному воинству. 6Он приносил своих сыновей в огненную жертву в долине Бен-Гинном, гадал и ворожил, и занимался волшебством. Он общался с вызывателями умерших и чародеями. Он сделал много зла в глазах Господа, вызывая Его гнев.

7Он взял резного идола, которого сделал, и поставил его в Божьем доме, о котором Бог говорил Давиду и его сыну Соломону: «В этом доме и в Иерусалиме, который Я избрал среди всех родов Израиля, Я помещу Мое имя навеки. 8Я не дам впредь ногам израильтян оставить землю, которой Я наделил их отцов, если только они будут исполнять все, что Я повелел им в отношении Закона, правил и установлений, данных через Моисея».

9Но Манассия сбил Иудею и жителей Иерусалима с пути, и они стали делать больше зла, чем те народы, которых Господь истребил перед израильтянами.

10Господь предостерегал Манассию и его народ, но они не слушали. 11И Господь навел на них военачальников царя Ассирии, которые взяли Манассию в плен, продели в его нос крюк, заковали в бронзовые кандалы и увели его в Вавилон. 12Попав в беду, он искал милости у Господа, своего Бога, и глубоко смирился перед Богом своих отцов. 13Когда он молился, Господь смилостивился над ним и внял его мольбе. Он возвратил его в Иерусалим, на его трон. Так Манассия познал, что Господь есть Бог.

14После этого он отстроил внешнюю стену Города Давида к западу от источника Гихон в долине до самого прохода Рыбных ворот и вокруг холма Офел, притом он сделал ее гораздо выше. Он разместил военачальников во всех укрепленных городах Иудеи. 15Он убрал чужеземных богов и идола из Господнего дома вместе с жертвенниками, которые построил на храмовой горе и в Иерусалиме; он выбросил их из города. 16Он восстановил жертвенник Господа, принес на нем жертвы примирения и благодарственные жертвы и велел Иудее служить Господу, Богу Израиля. 17Народ же продолжал приносить жертвы в святилищах на возвышенностях, но только Господу, Богу своему.

18Прочие события правления Манассии, его молитва своему Богу и слова провидцев, сказанные ему во имя Господа, Бога Израиля, записаны в летописях царей Израиля. 19Его молитва и то, как Бог смилостивился над ним, все его грехи, неверность и места, где он строил святилища на возвышенностях и ставил столбы Ашеры и идолов, прежде чем смирил себя, – все это записано в «Летописях провидцев»33:19 Так в одной из рукописей еврейского текста и в одном из древних переводов; в нормативном еврейском тексте: «Хозая».. 20Манассия упокоился со своими предками и был похоронен у себя во дворце. Амон, его сын, стал царем вместо него.

Амон – царь Иудеи

(4 Цар. 21:19-24)

21Амону было двадцать два года, когда он стал царем, и правил он в Иерусалиме два года. 22Он делал зло в глазах Господа, как и его отец Манассия. Амон поклонялся и приносил жертвы всем идолам, которых сделал Манассия. 23Но, в отличие от своего отца Манассии, он не смирил себя перед Господом – этот Амон лишь умножал свою вину.

24Приближенные Амона составили против него заговор и убили его в его же дворце. 25Но народ страны перебил всех, кто был в заговоре против царя Амона, и сделал царем вместо него его сына Иосию.