2 Mbiri 32 – CCL & CARS

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Mbiri 32:1-33

Senakeribu Aopseza Yerusalemu

1Zitatha zonse zimene Hezekiya anachita mokhulupirika, Senakeribu mfumu ya ku Asiriya anabwera ndi kuthira nkhondo dziko la Yuda. Iye anazinga mizinda yotetezedwa ya Yuda, kuganiza kuti ayigonjetsa. 2Pamene Hezekiya anaona kuti Senakeribu wabwera ndipo wakonzeka kuchita nkhondo ndi Yerusalemu, 3iye anakambirana ndi akuluakulu ake pamodzi ndi atsogoleri a gulu lankhondo za kutseka akasupe ochoka ku kasupe amene anali kunja kwa mzinda, ndipo iwo anamuthandiza. 4Gulu lalikulu la anthu linasonkhana, ndipo anatseka akasupe onse pamodzi ndi mtsinje umene umayenda mʼkati mwa nthakamo. Iwo ankanena kuti, “Nʼchifukwa chiyani mafumu a Asiriya akabwera kuno adzapeze madzi ambiri?” 5Kenaka iye anagwira ntchito molimbika kukonza madera ogumuka a khoma ndi kumangapo msanja. Anamanganso mpanda wina kunja kwa mpanda winawo ndipo anamanga zolimbitsa Milo ku mzinda wa Davide.

6Iye anasankha atsogoleri a ankhondo olamulira anthu ndipo anawasonkhanitsa pamaso pake pa bwalo la chipata cha mzinda ndi kuwalimbikitsa ndi mawu awa: 7“Khalani amphamvu ndi olimba mtima. Musachite mantha kapena kutaya mtima chifukwa cha mfumu ya ku Asiriya ndi gulu lalikulu lankhondo limene ali nalo, pakuti ife tili ndi mphamvu yayikulu kuposa imene ili ndi iye. 8Iye ali ndi mphamvu ya anthu basi, koma ife tili ndi Yehova Mulungu wathu kutithandiza ndi kuchita nkhondo zathu.” Ndipo anthu anapeza chilimbikitso kuchokera pa zimene Hezekiya mfumu ya Yuda ananena.

9Nthawi ina, pamene Senakeribu mfumu ya ku Asiriya ndi gulu lake lonse lankhondo anali atazinga Lakisi, iye anatumiza atsogoleri ake ankhondo ku Yerusalemu ndi uthenga uwu kwa Hezekiya mfumu ya Yuda ndi anthu onse a ku Yuda amene anali kumeneko:

10“Senakeribu mfumu ya ku Asiriya akuti: Kodi inu mukukhulupirira chiyani, kuti mukukhalabe mu Yerusalemu mutazingidwa? 11Pamene Hezekiya akunena kuti ‘Yehova Mulungu wathu adzatipulumutsa kuchoka mʼdzanja la mfumu ya ku Asiriya,’ iye akukusocheretsani, kuti mufe ndi njala ndi ludzu. 12Kodi si Hezekiya amene anachotsa malo opembedzerapo Mulungu ameneyu ndi maguwa ansembe ndi kunena kwa anthu a ku Yuda ndi Yerusalemu kuti, ‘Muzipembedza pa guwa lansembe limodzi ndi kupserezapo nsembe?’

13“Kodi inu simukudziwa zimene ine ndi makolo anga tachita kwa anthu a mitundu ina? Kodi milungu ya mitundu imeneyi inatha kupulumutsa dziko lawo kuchoka mʼdzanja langa? 14Kodi ndi milungu iti mwa milungu ya mitundu ina ya anthuwo, imene makolo anga anayiwononga kotheratu, inatha kupulumutsa anthu ake mʼdzanja langa? Nanga tsono Mulungu wanuyo adzakupulumutsani mʼdzanja langa motani? 15Choncho inu musalole kuti Hezekiya akunamizeni ndi kukusocheretsani motere. Musamukhulupirire, pakuti palibe mulungu wa mtundu wina uliwonse kapena ufumu wina uliwonse umene unatha kupulumutsa anthu ake kuchoka mʼdzanja langa kapena mʼdzanja la makolo anga. Nanga bwanji Mulungu wanuyo, sadzatha kukupulumutsani kuchoka mʼdzanja langa!”

16Atsogoleri a ankhondo a Senakeribu anapitiriza kuyankhula zotsutsana ndi Yehova Mulungu ndi mtumiki wake Hezekiya. 17Mfumunso inalemba makalata onyoza Yehova, Mulungu wa Israeli, ndipo inanena zotsutsana naye izi: “Monga momwe milungu ya anthu a mayiko ena sinathe kuwapulumutsa kuchoka mʼdzanja langa, chonchonso Mulungu wa Hezekiya sadzapulumutsa anthu ake kuchoka mʼdzanja langa.” 18Kenaka iwo anafuwula mu Chihebri kwa anthu a mu Yerusalemu amene anali pa khoma, kuwaopseza ndi kuwachititsa mantha ndi cholinga choti alande mzindawo. 19Iwo anayankhula za Mulungu wa Yerusalemu monga anayankhulira za milungu ya anthu ena a pa dziko lapansi, ntchito ya manja a anthu.

20Mfumu Hezekiya ndi mneneri Yesaya mwana wa Amozi anafuwulira kumwamba mʼpemphero chifukwa cha zimenezi. 21Ndipo Yehova anatumiza mngelo amene anadzapha anthu onse odziwa nkhondo ndi atsogoleri ndiponso oyangʼanira misasa ya mfumu ya ku Asiriya. Choncho Senakeribu anabwerera kwawo wamanyazi. Ndipo atalowa mʼnyumba ya mulungu wake, ena mwa ana ake anamupha ndi lupanga.

22Kotero Yehova anapulumutsa Hezekiya ndi anthu a ku Yerusalemu kuchoka mʼdzanja la Senakeribu mfumu ya ku Asiriya ndi mʼdzanja la anthu ena. Yehova anawateteza ku mbali zonse. 23Anthu ambiri anabweretsa zopereka kwa Yehova ku Yerusalemu ndi mphatso zamtengowapatali kwa Hezekiya mfumu ya Yuda. Kuyambira nthawi imeneyo Hezekiya ankalemekezedwa kwambiri ndi mitundu ina yonse.

Kunyada, Kupambana ndi Imfa ya Hezekiya

24Pa nthawi imeneyo Hezekiya anadwala ndipo anali pafupi kufa. Iye anapemphera kwa Yehova, amene anamuyankha ndi kumupatsa chizindikiro chodabwitsa. 25Koma Hezekiya anali ndi mtima wonyada ndipo sanachite molingana ndi kukoma mtima kumene Mulungu anamuonetsera. Choncho mkwiyo wa Yehova unali pa iye ndi pa Yuda ndi Yerusalemu. 26Koma kenaka Hezekiya analapa za kunyada kwakeko, monga anachitanso anthu a mu Yerusalemu. Choncho mkwiyo wa Yehova sunafike pa iwo pa nthawi ya Hezekiya.

27Hezekiya anali ndi chuma ndi ulemu wambiri ndipo anamanga nyumba zosungiramo chuma cha siliva wake ndi golide ndi za miyala yokongola, zokometsera zakudya, zishango ndi mtundu uliwonse wa zinthu zamtengowapatali. 28Iye anamanganso nyumba zosungiramo tirigu, vinyo watsopano ndi mafuta a olivi, ndiponso anamanga nyumba zodyeramo ngʼombe zosiyanasiyana, ndi makola a nkhosa. 29Iyeyo anamanga midzi ndipo anali ndi nkhosa ndi ngʼombe zambiri, pakuti Mulungu anamupatsa chuma chambiri.

30Ndi Hezekiya amene anatseka ku mtunda kwa kasupe wa Gihoni, ndi kumuwongolera kuti madzi ake apite mbali ya kumadzulo kwa Mzinda wa Davide. Iye ankachita bwino pa ntchito iliyonse imene ankagwira. 31Koma pamene nthumwi zotumizidwa ndi atsogoleri a ku Babuloni zinabwera kudzamufunsa za chizindikiro chozizwitsa chimene chinachitika mʼdzikomo, Mulungu anamusiya yekha, kumuyesa kuti adziwe zonse zimene zinali mu mtima mwake.

32Zina ndi zina zokhudza ulamuliro wa Hezekiya ndi ntchito za kudzipereka kwake zalembedwa mʼmasomphenya a Yesaya mwana wa Amozi, mʼbuku la mafumu a Yuda ndi Israeli. 33Hezekiya anamwalira ndipo anayikidwa mʼmanda pa phiri pamene pali manda a zidzukulu za Davide. Ayuda onse ndi anthu a mu Yerusalemu anamulemekeza atamwalira. Ndipo Manase mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake.

Священное Писание

2 Летопись 32:1-33

Синаххериб угрожает Иерусалиму

(4 Цар. 18:13-37; 19:35-37; Ис. 36:1-22; 37:36-38)

1После всего, что с такой верностью совершил Езекия, пришёл Синаххериб32:1 Синаххериб был сыном и преемником Саргона II. Он правил с 705 по 681 гг. до н. э., царь Ассирии, и вторгся в Иудею. Он взял в осаду укреплённые города, думая отобрать их. 2Когда Езекия увидел, что Синаххериб пришёл и хочет воевать с Иерусалимом, 3он решил на совете со своими приближёнными и военачальниками засыпать источники воды за пределами города, и те помогли ему. 4Собралось множество народа и засыпали источники воды и реку, которая протекала по стране. «К чему оставлять эту воду царям Ассирии?» – говорили они. 5Езекия много трудился, восстанавливая все разрушенные участки стены и воздвигая на ней башни. Он сложил ещё одну стену за пределами прежней и улучшил Милло32:5 Милло – с языка оригинала переводится как «насыпь». Возможно, что это были какие-то городские укрепления. Города Давуда. Ещё он изготовил много оружия и щитов. 6Он поставил над народом военачальников, собрал их к себе на площади у городских ворот и ободрил их, сказав:

7– Будьте тверды и мужественны! Не бойтесь, не падайте духом из-за царя Ассирии и его огромного войска, потому что с нами сила большая, чем с ним. 8С ним – сила людская, а с нами – Вечный, наш Бог, Который поможет нам и будет за нас сражаться.

И народ ободрился словами Езекии, царя Иудеи.

9После этого, когда Синаххериб, царь Ассирии, и все его войска осаждали город Лахиш, он послал своих слуг в Иерусалим, чтобы передать Езекии, царю Иудеи, и всему собравшемуся там народу Иудеи:

10– Так говорит Синаххериб, царь Ассирии: «На что вы так надеетесь, что остаётесь в осаждённом Иерусалиме? 11Когда Езекия говорит: „Вечный, наш Бог, спасёт нас от руки царя Ассирии“, он сбивает вас с пути, чтобы вы умерли от голода и жажды. 12Разве не сам Езекия убрал святилища на возвышенностях и жертвенники этого Бога, говоря Иудее и Иерусалиму: „Поклоняйтесь перед одним жертвенником и на нём сжигайте жертвы“?32:12 Слуги Синаххериба ложно предполагали, что Езекия оскорбил Вечного, разрушив святилища и тем самым лишив Его всех жертвенников, кроме одного, который находился в Иерусалиме (см. 4 Цар. 18:4; 2 Лет. 31:1). 13Разве вы не знаете, что я и мои предки сделали со всеми народами других земель? Разве в силах были боги этих народов избавить свою землю от моей руки? 14Кто из богов всех этих народов, которые были погублены моими предками, смог избавить от меня свой народ? Как же ваш Бог сможет избавить вас от моей руки? 15Не давайте же Езекии обманывать вас этим и сбивать с пути. Не верьте ему, потому что никакой бог ни у одного из народов или царств не мог избавить свой народ от моей руки или от рук моих предков. И куда уж вашему Богу избавить вас от моей руки!»

16Слуги царя Синаххериба говорили ещё больше против Вечного Бога и против Его раба Езекии. 17Синаххериб также написал письма, осыпая бранью Вечного, Бога Исраила, и говоря против Него: «Как боги народов других земель не избавили своих народов от моей руки, так и Бог Езекии не избавит Своего народа от моей руки». 18Они кричали по-еврейски жителям Иерусалима, которые были на стене, чтобы устрашить и запугать их и захватить город. 19Они говорили о Боге Иерусалима, как о богах других народов земли, – творениях человеческих рук.

20Царь Езекия и пророк Исаия, сын Амоца, воззвали в молитве к небесам, 21и Вечный послал Ангела32:21 Ангел – этот особенный ангел отождествляется с Самим Вечным. Многие толкователи видят в Нём явления Исы Масиха до Его воплощения., Который истребил всех храбрых воинов, вождей и полководцев в лагере ассирийского царя, и Синаххериб с позором удалился в свою землю. Однажды, когда он пошёл в храм своего бога, его сыновья поразили его мечом.

22Так Вечный спас Езекию и жителей Иерусалима от руки Синаххериба, царя Ассирии, и от рук всех остальных. Он оберегал их со всех сторон. 23И многие принесли в Иерусалим приношения Вечному и дорогие подарки Езекии, царю Иудеи. С тех пор он был в большом почёте у всех народов.

Конец правления Езекии

(4 Цар. 20:1-19; Ис. 38:1-8; 39:1-8)

24В те дни Езекия заболел и был при смерти. Он помолился Вечному, и Тот ответил ему и дал ему знамение. 25Но сердце Езекии возгордилось, и он не отозвался на оказанную ему милость. За это на нём и на Иудее с Иерусалимом был гнев Вечного. 26Тогда Езекия раскаялся в гордыне своего сердца, как и жители Иерусалима. За это гнев Вечного не обрушился на них в дни Езекии.

27Езекия был очень богат и прославлен. Он сделал сокровищницы для своего серебра и золота, для своих драгоценных камней, благовоний, щитов и всякого рода дорогих вещей. 28Ещё он построил кладовые для урожаев зерна, для молодого вина и оливкового масла и сделал стойла и загоны для различного скота. 29Он строил поселения и приобретал многочисленные отары и стада, потому что Всевышний даровал ему огромное богатство. 30Это Езекия засыпал верхний проток источника Гихон и отвёл воду вниз к западной стороне Города Давуда. Он преуспевал во всём, что делал.

31Однажды, когда правители Вавилона отправили послов, чтобы спросить Езекию о знамении, которое совершилось в стране, Всевышний оставил его наедине с самим собой, чтобы испытать его и узнать всё, что у него на сердце.

Смерть Езекии

(4 Цар. 20:20-21)

32Прочие события царствования Езекии и его добрые дела записаны в «Видениях пророка Исаии, сына Амоца», которые включены в «Книгу царей Иудеи и Исраила». 33Езекия упокоился со своими предками и был похоронен на возвышенности, там, где могилы потомков Давуда. Вся Иудея и все жители Иерусалима почтили его, когда он умер. И царём вместо него стал его сын Манасса.