2 Mbiri 29 – CCL & CARSA

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Mbiri 29:1-36

Mfumu Hezekiya Ayeretsa Nyumba ya Mulungu

1Hezekiya anali wa zaka 25 pamene anakhala mfumu ndipo analamulira mu Yerusalemu kwa zaka 29. Dzina la amayi ake linali Abiya mwana wa Zekariya. 2Iye anachita zolungama pamaso pa Yehova, monga momwe anachitira Davide abambo ake.

3Pa chaka choyamba cha ulamuliro wake, iye anatsekula zitseko za Nyumba ya Yehova ndipo anazikonza. 4Iye analowetsamo ansembe ndi Alevi ndipo anawasonkhanitsa ku bwalo lakummawa 5ndipo anati: “Mverani, inu Alevi! Dziyeretseni tsopano ndiponso muyeretse Nyumba ya Yehova Mulungu wa makolo anu. Muchotse zodetsa zonse ku malo opatulika. 6Makolo athu anali osakhulupirika ndipo anachita zoyipa pa maso pa Yehova Mulungu wathu ndi kumusiya Yehovayo. Iwo anatembenuka ndi kusiya malo okhalako Yehova ndi kumufulatira. 7Iwowo anatsekanso zitseko zapakhonde ndi kuzimitsa nyale. Sanafukize lubani kapena kupereka nsembe zopsereza ku malo opatulika a Mulungu wa Israeli. 8Kotero, Yehova anakwiyira Yuda ndi Yerusalemu. Iye anawasandutsa chinthu chochititsa mantha, choopsa ndiponso chonyozedwa monga momwe mukuonera ndi maso anuwa lero lino. 9Ichi nʼchifukwa chake makolo athu anaperekedwa ku lupanga ndipo nʼchifukwa chake ana athu aamuna ndi aakazi ndi akazi athu ali ku ukapolo. 10Tsono ine ndikuganiza zochita pangano ndi Yehova Mulungu wa Israeli, kuti mkwiyo wake woopsawu utichokere. 11Ana anga, musanyalanyaze tsopano, pakuti Yehova wakusankhani kuti muziyima pamaso pake ndi kumutumikira Iye, kugwira ntchito pamaso pake ndi kufukiza lubani.”

12Ndipo Alevi awa anakonzeka kugwira ntchito:

Kuchokera ku banja la Kohati,

Mahati mwana wa Amasai ndi Yoweli mwana wa Azariya;

kuchokera ku banja la Merari,

Kisi mwana wa Abidi ndi Azariya mwana wa Yehaleleli;

kuchokera ku banja la Geresoni,

Yowa mwana wa Zima ndi Edeni mwana wa Yowa;

13kuchokera kwa zidzukulu za Elizafani,

Simiri ndi Yeiyeli;

kuchokera kwa zidzukulu za Asafu,

Zekariya ndi Mataniya;

14kuchokera kwa zidzukulu za Hemani,

Yehieli ndi Simei;

kuchokera kwa zidzukulu za Yedutuni,

Semaya ndi Uzieli.

15Atasonkhanitsa abale awo ndi kudziyeretsa, iwo anapita kukayeretsa Nyumba ya Yehova, monga inalamulira mfumu, potsatira mawu a Yehova. 16Ansembe analowa ku malo opatulika a Yehova kukayeretsako. Anatulutsira ku bwalo la Nyumba ya Yehova chilichonse chodetsedwa chimene anachipeza mʼNyumba ya Yehova. Alevi anatenga zimenezo ndi kupita nazo ku chigwa cha Kidroni. 17Iwo anayamba mwambo woyeretsawu tsiku loyamba la mwezi woyamba ndipo pa tsiku lachisanu ndi chitatu la mweziwo anafika pa khonde la nyumba ya Yehova. Tsono anachita mwambo woyeretsa Nyumba ya Yehova ija masiku asanu ndi atatu, ndipo anamaliza pa tsiku la 16 mwezi woyamba.

18Ndipo anapita kwa mfumu Hezekiya ndi kukafotokoza kuti, “Ife tayeretsa Nyumba ya Mulungu yonse, guwa lansembe zopsereza ndi ziwiya zake zonse, ndiponso tebulo limene timayikapo buledi wopatulika pamodzi ndi zinthu zake zonse. 19Takonza ndi kuyeretsa zinthu zonse zimene mfumu Ahazi anazichotsa mwa kusakhulupirika kwake pamene anali mfumu. Taziyika kutsogolo kwa guwa la Yehova.”

20Mmamawa tsiku linalo, mfumu Hezekiya inasonkhanitsa pamodzi akuluakulu a mu mzindawo ndipo inapita ku Nyumba ya Yehova. 21Iwo anabweretsa ngʼombe zazimuna zisanu ndi ziwiri ndi nkhosa zazimuna zisanu ndi ziwiri, ana ankhosa aamuna asanu ndi awiri, mbuzi zazimuna zisanu ndi ziwiri monga nsembe zoperekedwa chifukwa cha tchimo la ufumu, la malo opatulika ndi Yuda. Tsono mfumu inalamula ansembe, zidzukulu za Aaroni, kuti apereke zimenezi pa guwa lansembe la Yehova. 22Choncho anthuwo anapha ngʼombe zazimunazo ndipo ansembe anatenga magazi ake ndi kuwawaza pa guwa lansembe, kenaka anapha nkhosa zazimuna zija ndipo anawaza magazi ake pa guwa lansembe; anaphanso ana ankhosa aja ndipo anawaza magazi ake pa guwa lansembe. 23Mbuzi zoperekedwa chifukwa cha tchimo zija zinabweretsedwa pamaso pa mfumu ndi anthu onse, ndipo anasanjika manja awo pa izo. 24Kenaka ansembe anapha mbuzizo ndipo anapereka magazi ake pa guwa, kuti ukhale mwambo wofafanizira machimo a Aisraeli onse, pakuti mfumu inalamula kuti nsembe yopsereza ndi yopepesera machimo zichitike chifukwa cha Aisraeli onse.

25Iye anayika Alevi mʼNyumba ya Yehova ali ndi ziwaya za malipenga, azeze ndi apangwe potsata lamulo la Davide, Gadi mlosi wa mfumu ndi mneneri Natani. Pakuti Yehova ndiye analamula zimenezi kudzera mwa aneneri. 26Kotero Alevi anayima okonzekera atanyamula zoyimbira za Davide ndiponso ansembe atanyamula malipenga awo.

27Hezekiya analamulira kuti apereke nsembe zopsereza pa guwa. Pamene amayamba kupereka nsembezo, kuyimbira Yehova kunayambikanso, pamodzi ndi malipenga ndi zipangizo zoyimbira za Davide mfumu ya Israeli. 28Anthu onse anawerama pansi ndi kulambira, pamene oyimba amayimba ndi malipenga. Izi zonse zinapitirira mpaka pa mapeto pa nsembe zopsereza.

29Zopereka zitatha, mfumu ndi wina aliyense amene anali naye anagwada pansi ndi kulambira. 30Mfumu Hezekiya ndi akuluakulu ake analamulira Alevi kuti atamande Yehova potsata mawu a Davide ndi mlosi Asafu. Kotero anayimba nyimbo zamatamando mokondwera ndipo anaweramitsa mitu yawo ndi kulambira.

31Kenaka Hezekiya anati, “Inu mwadzipereka tsopano kwa Yehova. Bwerani ndipo mufike ndi nsembe ndi zopereka zachiyamiko ku Nyumba ya Yehova.” Choncho anthu onse anabweretsa nsembe ndi zopereka zachiyamiko, ndipo anthu onse amene anali ofuna mu mtima mwawo anabweretsa nsembe zopsereza.

32Chiwerengero cha nsembe zopsereza chimene anthu onse anabweretsa chinali ngʼombe zazimuna makumi asanu ndi awiri, nkhosa zazimuna 100, ana ankhosa aamuna 200 ndipo zonsezi zinali za nsembe yopsereza kwa Yehova. 33Ziweto zimene zinapatulidwa kukhala nsembe zinalipo ngʼombe zazimuna 600, nkhosa ndi mbuzi 3,000. 34Koma ansembe anali ochepa kuti asende zonse zopsereza. Choncho abale awo Alevi anawathandiza mpaka ntchito yonse inatha ndipo mpaka ansembe ena atadziyeretsa, pakuti Alevi anachita changu kudziyeretsa kulekana ndi momwe anachitira ansembe. 35Panali nsembe zopsereza zochuluka, pamodzi ndi mafuta a nsembe yachiyanjano ndi nsembe yachakumwa imene imachitika pamodzi ndi nsembe yopsereza.

Kotero ntchito ya mʼNyumba ya Mulungu inakhazikitsidwanso. 36Hezekiya ndi anthu onse anakondwera pa zimene Mulungu anachitira anthu ake, chifukwa zinachita mwamsangamsanga.

Священное Писание (Восточный перевод), версия с «Аллахом»

2 Летопись 29:1-36

Езекия – царь Иудеи

(4 Цар. 18:1-3)

1Езекии было двадцать пять лет, когда он стал царём, и правил он в Иерусалиме двадцать девять лет. Его мать звали Авия, она была дочерью Закарии. 2Он делал то, что было правильным в глазах Вечного, как и его предок Давуд.

Езекия очищает храм

3В первый месяц (ранней весной), на первом году своего правления, он открыл двери храма Вечного и починил их. 4Он привёл священнослужителей и левитов, собрал их на площади с восточной стороны 5и сказал им:

– Слушайте меня, левиты! Освятитесь сегодня сами и освятите храм Вечного, Бога ваших предков. Выбросите из святилища всякую скверну. 6Наши отцы поступали беззаконно, делая зло в глазах Вечного, нашего Бога, и оставили Его. Они отвернули свои лица от жилища Вечного и повернулись к нему спиной. 7Они заперли двери притвора и погасили светильники. Они не возжигали благовоний и не приносили всесожжений в святилище Бога Исраила. 8За это гнев Вечного обрушился на Иудею и Иерусалим. Он отдал их на позор, на опустошение и на посмеяние, как вы видите своими глазами. 9Поэтому наши отцы пали от меча, а наши сыновья, дочери и жёны в плену. 10И теперь я хочу заключить соглашение с Вечным, Богом Исраила, чтобы Его пылающий гнев на нас прекратился. 11Дети мои, не будьте же беспечными, потому что Вечный избрал вас служить Ему и возжигать благовония.

12И начали своё служение левиты:

из потомков Каафа – Махат, сын Амасая, и Иоиль, сын Азарии;

из потомков Мерари – Киш, сын Авди, и Азария, сын Иехаллелила;

из потомков Гершона – Иоах, сын Зиммы, и Еден, сын Иоаха;

13из потомков Элицафана – Шимри и Иеил;

из потомков Асафа – Закария и Маттания;

14из потомков Емана – Иехиил и Шимей;

из потомков Иедутуна – Шемая и Узиил.

15Собрав своих братьев и освятившись, они пришли очищать храм Вечного, как, следуя словам Вечного, повелел царь. 16Священнослужители прошли в святилище Вечного, чтобы очистить его. Они вынесли во двор храма Вечного всё нечистое, что нашли в храме Вечного. Левиты взяли это и отнесли в долину Кедрон. 17Приступив к освящению в первый день первого месяца, они подошли к притвору храма Вечного в восьмой день того же месяца. Ещё восемь дней они освящали сам храм и закончили на шестнадцатый день первого месяца.

18Они пришли к царю Езекии и сказали:

– Мы очистили весь храм Вечного, жертвенник для всесожжений со всей его утварью и стол, на который кладут священный хлеб, со всей его утварью. 19Всю утварь, которую во время своего правления убрал неверный царь Ахаз, мы приготовили и освятили. Она сейчас перед жертвенником Вечного.

Освящение храма

20На следующий день, ранним утром, царь Езекия собрал начальников города и отправился в храм Вечного. 21Они привели семь быков, семь баранов, семь ягнят и семь козлов, чтобы принести их в жертву за грех за царскую семью, за святилище и за всю Иудею. Царь велел священнослужителям, потомкам Харуна, принести их в жертву на жертвеннике Вечного. 22Быков закололи, и священнослужители, взяв крови, окропили ею жертвенник. Затем закололи баранов и окропили жертвенник их кровью. Затем закололи ягнят и окропили жертвенник их кровью. 23А козлов, которые были предназначены в жертву за грех, поставили перед царём и собранием, и они возложили на них руки. 24Затем священнослужители закололи козлов и принесли их кровь на жертвеннике как жертву за грех, чтобы очистить весь Исраил, потому что царь велел совершить всесожжение и принести жертву за грех за весь Исраил.

25Езекия поставил левитов с тарелками, лирами и арфами в храме Вечного, по указанию Давуда, царского провидца Гада и пророка Нафана. Это установление было дано Вечным через Его пророков. 26Левиты стояли наготове с музыкальными инструментами Давуда, а священнослужители – с трубами.

27Езекия велел принести на жертвеннике всесожжение. Когда жертвоприношение началось, началось и пение Вечному под голос труб и музыкальных инструментов Давуда, царя Исраила. 28Всё собрание совершало поклонение, певцы пели, а трубачи трубили. Так продолжалось, пока жертвоприношение не было завершено.

29Когда жертвы были принесены, царь и все, кто был с ним, преклонили колени и поклонились. 30Царь Езекия со своими приближёнными велел левитам славить Вечного словами Давуда и провидца Асафа. И они радостно пели хвалу, кланялись и прославляли Вечного. 31Езекия сказал:

– Итак, вы посвятили себя Вечному. Приступайте, несите жертвы и благодарственные приношения в храм Вечного.

Народ принёс жертвы и благодарственные приношения, а все, кто был к этому расположен, принесли и всесожжения. 32Жертв всесожжения, которые принёс народ, было общим счётом: семьдесят быков, сто баранов и двести ягнят – всё это для всесожжения Вечному. 33Других священных жертв было: шестьсот голов крупного и три тысячи голов мелкого скота. 34Но священнослужителей было слишком мало, чтобы освежевать все туши жертв всесожжения, и пока другие священнослужители не освятились, их сородичи левиты помогали им, пока работа не была сделана, потому что левиты отнеслись к освящению добросовестнее, чем священнослужители. 35Жертв всесожжения и жира жертв примирения с жертвенными возлияниями, которыми сопровождались всесожжения, было в изобилии.

Так было восстановлено служение в храме Вечного. 36Езекия и весь народ радовались тому, что сделал для Своего народа Аллах, ведь сделано это было так быстро.