2 Mbiri 27 – CCL & CARS

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Mbiri 27:1-9

Yotamu Mfumu ya Yuda

1Yotamu anakhala mfumu ali ndi zaka 25 ndipo analamulira mu Yerusalemu kwa zaka 16. Dzina la amayi ake linali Yerusa mwana wa Zadoki. 2Iye anachita zolungama pamaso pa Yehova, monga anachitira Uziya abambo ake, kupatula kuti iyeyo sanalowe mʼNyumba ya Yehova. Komabe anthu anapitirira kuchita zoyipa. 3Yotamu anamanganso chipata chakumtunda cha Nyumba ya Yehova ndipo anagwira ntchito yayikulu yomanga khoma la ku phiri la Ofeli. 4Iye anamanga mizinda mʼmapiri a ku Yuda ndipo anamanganso malinga ndi nsanja mʼmadera a ku nkhalango.

5Yotamu anachita nkhondo ndi mfumu ya Aamoni ndipo anawagonjetsa. Chaka chimenecho Aamoni anapereka makilogalamu 3,400, matani 1,000 a tirigu ndiponso matani 1,000 a barele. Aamoni anabweretsa zinthu zomwezi chaka chachiwiri ndi chachitatu.

6Yotamu anakula mphamvu chifukwa anayenda molungama pamaso pa Yehova Mulungu wake.

7Zina ndi zina zokhudza ulamuliro wa Yotamu, kuphatikizapo nkhondo zake zonse ndi zinthu zina zimene anachita, zinalembedwa mʼbuku la mafumu a Israeli ndi Yuda. 8Iye anakhala mfumu ali ndi zaka 25 ndipo analamulira mu Yerusalemu kwa zaka 16. 9Yotamu anamwalira ndipo anayikidwa mʼmanda mu Mzinda wa Davide. Ndipo Ahazi mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake.

Священное Писание

2 Летопись 27:1-9

Иотам – царь Иудеи

(4 Цар. 15:32-38)

1Иотаму было двадцать пять лет, когда он стал царём, и правил он в Иерусалиме шестнадцать лет. Его мать звали Иеруша, она была дочерью Цадока. 2Он делал то, что было правильным в глазах Вечного, как и его отец Уззия, но в отличие от него, он не вторгался в храм Вечного. А народ продолжал грешить. 3Иотам перестроил Верхние ворота храма Вечного и выполнил большие работы у городской стены на холме Офел. 4Он строил города в иудейских горах и крепости с башнями в лесистых местностях.

5Иотам пошёл войной на царя аммонитян и победил его. Ежегодно в течение трёх лет аммонитяне выплачивали ему три тысячи шестьсот килограммов серебра, тысячу восемьсот тонн27:5 Букв.: «сто талантов… десять тысяч ко́ров». пшеницы и столько же ячменя.

6Иотам стал могущественным царём, потому что жил, во всём повинуясь Вечному, своему Богу.

7Прочие события царствования Иотама, все его войны и другие деяния, записаны в «Книге царей Исраила и Иудеи». 8Ему было двадцать пять лет, когда он стал царём, и правил он в Иерусалиме шестнадцать лет. 9Иотам упокоился со своими предками и был похоронен в Городе Давуда. И царём вместо него стал его сын Ахаз.