2 Mbiri 26 – CCL & HTB

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Mbiri 26:1-23

Uziya Mfumu ya Yuda

1Kenaka anthu onse a ku Yuda anatenga Uziya amene anali wa zaka 16, namuyika kukhala mfumu mʼmalo mwa Amaziya abambo ake. 2Iye anamanganso mzinda wa Eloti ndi kuwubwezeranso ku Yuda abambo ake atamwalira.

3Uziya anali wa zaka 16 pamene anakhala mfumu ndipo analamulira mu Yerusalemu kwa zaka 70. Dzina la amayi ake linali Yekoliya wa ku Yerusalemu. 4Iye anachita zolungama pamaso pa Yehova, monga momwe anachitira Amaziya abambo ake. 5Iye anapembedza Mulungu nthawi ya Zekariya, amene ankamulangiza za kuopa Mulungu amene anamupatsa chipambano.

6Iyeyo anapita kukachita nkhondo ndi Afilisti ndipo anagwetsa makoma a Gati, Yabine ndi Asidodi. Ndipo kenaka anamanganso mizinda ya pafupi ndi Asidodi ndi malo ena pafupi ndi Afilisti. 7Mulungu anamuthandiza polimbana ndi Afilisti ndi Aarabu amene amakhala ku Guri-Baala ndiponso polimbana ndi Ameuni. 8Aamoni ankabweretsa msonkho kwa Uziya ndipo mbiri yake inamveka mpaka ku malire a dziko la Igupto chifukwa anali wamphamvu kwambiri.

9Uziya anamanga nsanja ku Yerusalemu ku Chipata Chapangodya, ku Chigwa cha Chipata ndi pokhotera mpanda, ndipo anayikamo chitetezo. 10Iye anamanganso nsanja ku chipululu ndi kukumbanso zitsime zambiri chifukwa anali ndi ziweto zambiri mʼmbali mwa phiri ndi ku zigwa. Iye anali ndi anthu amene ankagwira ntchito mʼminda yake ndiponso mʼminda yake ya mphesa mʼphiri ndi malo achonde, pakuti ankakonda nthaka.

11Uziya anali ndi gulu lankhondo lophunzitsidwa bwino, lokonzekera kupita ku nkhondo mʼmagulu monga mwa chiwerengero chawo chimene mlembi Yeiyeli ndi Maaseya anasonkhanitsa motsogozedwa ndi Hananiya mmodzi mwa akuluakulu a mfumu. 12Chiwerengero chonse cha atsogoleri a mʼmabanja oyangʼanira anthu ochita nkhondo chinali 2,600. 13Pansi pa ulamuliro wawo panali asilikali 307,500 ophunzitsidwa nkhondo, gulu lamphamvu lothandiza mfumu kulimbana ndi adani ake. 14Uziya anawapangira asilikaliwo zishango, mikondo, zipewa zankhondo, malaya ankhondo achitsulo, mauta ndi miyala yogendera. 15Mu Yerusalemu anapanga makina okonzedwa ndi anthu aluso amene amagwiritsidwa ntchito pa malo otetezera a pa nsanja ndi pa ngodya kuponyera mivi ndi kugubuduzira miyala. Mbiri yake inamveka kutali ndi ponseponse pakuti anathandizidwa kwambiri mpaka anakhala wamphamvu kwambiri.

16Koma pamene Uziya anakhala wamphamvu kwambiri, kunyada kwake kunamuwononga. Iye sanakhulupirike kwa Yehova Mulungu wake, ndipo analowa mʼNyumba ya Yehova kukafukiza lubani pa guwa lofukizira. 17Wansembe Azariya pamodzi ndi ansembe a Yehova ena 80 olimba mtima anamutsatira. 18Iwo anatsutsana naye ndipo anati, “Sibwino kuti inu mfumu muzifukiza lubani koma zidzukulu za Aaroni, zimene zinapatulidwa kuti zizifukiza lubani. Chokani pa malo opatulika ano, pakuti inu mwakhala osakhulupirika, ndipo simudzalemekezedwa ndi Yehova Mulungu.”

19Uziya, amene anali ndi chofukizira mʼmanja mwake wokonzeka kuti afukize lubani, anapsa mtima. Iye anakwiyira ansembewo. Ndipo ansembe aja akuona patsogolo pa guwa lofukizira lubani mʼNyumba ya Mulungu, khate linayamba pamphumi pake. 20Azariya, mkulu wa ansembe pamodzi ndi ansembe ena onse atamuyangʼana anaona kuti anali ndi khate pamphumi pake, ndipo anamutulutsa mofulumira. Ndipo iye mwini anafulumira kutuluka, chifukwa Yehova anamulanga.

21Mfumu Uziya anali ndi khate mpaka tsiku limene anamwalira. Iye amakhala mʼnyumba ya yekha ngati wakhate, ndipo samalowa mʼNyumba ya Yehova. Yotamu mwana wake ndiye amayangʼanira nyumba yaufumu ndipo ankalamulira anthu a mʼdzikomo.

22Ntchito zina za mfumu Uziya, kuyambira pachiyambi mpaka pa mapeto, zinalembedwa ndi mneneri Yesaya mwana wa Amozi. 23Uziya analondola makolo ake, ndipo anamuyika pamodzi ndi makolo ake ku malo a manda a mafumu, koma osati mʼmanda mwawomo poti anthu anati, “Iyeyu anali ndi khate.” Ndipo Yotamu mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake.

Het Boek

2 Kronieken 26:1-23

Uzzia, koning van Juda

1De inwoners van Juda kroonden hierna Amaziaʼs zestienjarige zoon Uzzia tot hun nieuwe koning. 2Na zijn vaders dood herbouwde hij de stad Elat en voegde deze bij Juda. 3In totaal regeerde hij tweeënvijftig jaar over Juda vanuit Jeruzalem. Zijn moeder heette Jecholia en kwam uit Jeruzalem. 4Hij volgde het voorbeeld van zijn vader Amazia en was in de ogen van de Here een goede koning. 5Tijdens Zachariaʼs leven deed Uzzia steeds zijn best zoveel mogelijk naar Gods wil te leven. Zacharia was een man die leefde vanuit een diep ontzag voor God. En zolang de koning deed wat God van hem verlangde, ging alles voorspoedig, want God zegende hem. 6Hij verklaarde de Filistijnen de oorlog en maakte de muren van de stad Gath met de grond gelijk. Hetzelfde deed hij met Jabné en Asdod. Daarna bouwde hij nieuwe steden in het gebied van Asdod en in andere delen van het Filistijnse land. 7God hielp hem niet alleen in zijn strijd tegen de Filistijnen, maar gaf hem ook overwinningen op de Arabieren uit Gur-Baäl en op de Meünieten. 8De Ammonieten betaalden hem jaarlijks belasting en zijn roem bereikte zelfs Egypte, zo machtig was hij. 9Hij bouwde versterkte torens op de stadsmuren van Jeruzalem, één bij de Hoekpoort, één bij de Dalpoort en op de plaatsen waar de muur een bocht maakte. 10Tevens bouwde hij torens in de Negev en sloeg waterputten voor de grote kudden vee die hij in de dalen en op de vlakten hield. Hij was een man met een voorliefde voor de landbouw en bezat heel wat boerderijen en wijngaarden, zowel op de berghellingen als in de vruchtbare vlakten. 11Verder beschikte Uzzia over een sterk leger, dat was verdeeld in afdelingen waarvan de grootte was bepaald door de legersecretaris Jeïël en zijn assistent Maäseja. Het geheel stond onder toezicht van Hananja, een van de hoofdbestuurders van de koning. 12De familiehoofden, zesentwintighonderd in totaal, voerden het bevel over de moedige mannen in deze afdelingen. 13Het leger bestond uit driehonderdzevenduizend vijfhonderd manschappen, allemaal getraind om voor de koning te vechten in tijd van oorlog. 14Uzzia rustte hen uit met schilden, speren, helmen, harnassen, bogen en slingers. 15Tevens liet hij in Jeruzalem vernuftige oorlogsmachines maken. Deze waren ontworpen door vindingrijke werklieden en werden gebruikt voor het afschieten van pijlen en zware stenen vanaf de torens. Op die manier werd hij beroemd, want de Here hielp hem op wonderbaarlijke wijze bij de opbouw van zijn macht.

16Maar toen hij zoʼn grote macht had opgebouwd, werd hij hoogmoedig en dat veroorzaakte zijn ondergang. Hij zondigde tegen de Here, zijn God, door het voor hem verboden heiligdom van de tempel binnen te gaan en daar zelf reukwerk op het altaar te verbranden. 17-18 Onmiddellijk ging de hogepriester Azarja hem achterna met tachtig andere moedige priesters en verzocht hem weg te gaan. ‘Koning Uzzia, het is u niet toegestaan reukwerk te verbranden,’ verklaarden zij. ‘Dat is het werk van de priesters, de zonen van Aäron, die voor dat werk zijn geheiligd. Ga hier weg, want u bent in overtreding en deze daad zal de Here u niet in dank afnemen.’ 19Uzzia, die het reukwerkvat vasthield om reukwerk te verbranden, werd razend. Maar toen verscheen plotseling melaatsheid op zijn voorhoofd. 20Toen Azarja en de anderen dat zagen, brachten zij hem snel naar buiten. Hij stribbelde niet meer tegen, want hij was zelf veel te erg geschrokken door deze straf van de Here. 21Koning Uzzia bleef tot zijn dood melaats en leefde in afzondering, totaal geïsoleerd van zijn volk en van de tempel. Zijn zoon Jotham werd regent en regelde alle koninklijke aangelegenheden en het bestuur van het land.

22Alle regeringsdaden van Uzzia zijn van begin tot eind beschreven door de profeet Jesaja, de zoon van Amoz. 23Na zijn dood werd koning Uzzia naast de koninklijke begraafplaats begraven, vanwege zijn ziekte. Zijn zoon Jotham volgde hem op als koning.