2 Mbiri 25 – CCL & BPH

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Mbiri 25:1-28

Amaziya Mfumu ya Yuda

1Amaziya anali wa zaka 25 pamene anakhala mfumu, ndipo analamulira mu Yerusalemu kwa zaka 29. Dzina la amayi ake linali Yehoyadini wa ku Yerusalemu. 2Iye anachita zolungama pamaso pa Yehova, koma osati ndi mtima wonse. 3Pamene mphamvu zonse zaufumu zinali mʼmanja mwake, iye anapha akuluakulu amene anapha abambo ake, mfumu ija. 4Komabe iye sanaphe ana awo koma anatsatira zolembedwa mʼbuku la Mose, mʼmene Yehova analamula kuti, “Makolo sadzaphedwa chifukwa cha ana awo kapena ana kuphedwa chifukwa cha makolo awo. Aliyense adzafera machimo ake.”

5Amaziya anasonkhanitsa anthu a ku Yuda ndipo anawapatsa zochita molingana ndi mabanja awo kukhala anthu olamulira 1,000, ndi olamulira 100 pa Ayuda onse ndi Benjamini. Ndipo iye anawerenga amene anali ndi zaka makumi awiri kapena kupitirirapo napeza kuti analipo amuna 300,000 okonzeka kugwira ntchito ya usilikali, okhoza kugwiritsa ntchito mkondo ndi chishango. 6Iye analembanso ntchito anthu odziwa nkhondo 100,000 ochokera ku Israeli pa mtengo wa makilogalamu 3,400 a siliva.

7Koma munthu wa Mulungu anabwera kwa iye ndipo anati, “Inu mfumu, asilikali awa ochokera ku Israeli asapite ndi inu, pakuti Yehova sali ndi Israeli kapena ndi aliyense wa anthu a Efereimu. 8Ngakhale mupite ndi kuchita nkhondo molimba mtima, Mulungu adzakugonjetsani pamaso pa adani anu, pakuti Mulungu ali ndi mphamvu yothandiza kapena kugonjetsa.”

9Amaziya anafunsa munthu wa Mulungu kuti, “Koma nanga za makilogalamu aja a siliva amene ndapereka kwa asilikali a Israeli?”

Munthu wa Mulungu anayankha kuti, “Yehova atha kukupatsani zambiri kuposa zimenezo.”

10Choncho Amaziya anachotsa asilikali amene anabwera kwa iye kuchokera ku Efereimu ndipo anawatumiza kwawo. Iwo anakwiyira anthu a ku Yuda ndipo anapita kwawo atapsa mtima kwambiri.

11Ndipo Amaziya analimba mtima ndipo anatsogolera gulu lake lankhondo ku Chigwa cha Mchere, kumene anapha anthu 10,000 a ku Seiri. 12Gulu la ankhondo la Yuda linagwiranso anthu amoyo 10,000, napita nawo pamwamba pa thanthwe ndipo anawaponya pansi kotero kuti onse ananyenyeka.

13Pa nthawi imeneyi asilikali amene Amaziya anawabweza ndipo sanawalole kuti achite nawo nkhondo, anakathira nkhondo mizinda ya Yuda kuyambira ku Samariya mpaka ku Beti-Horoni. Iwo anapha anthu 3,000 ndipo anafunkha katundu wambiri.

14Amaziya atabwerera kuja anakapha Aedomu, anabweretsa milungu ya anthu a ku Seiri. Ndipo anayika kuti ikhale milungu yake, ankayipembedza ndi kupereka nsembe zopsereza. 15Yehova anakwiyira Amaziya, ndipo anamutumizira mneneri amene anati, “Nʼchifukwa chiyani mukupembedza milungu ya anthu awa, imene sinathe kupulumutsa anthu ake mʼdzanja lanu?”

16Iye ali kuyankhula, mfumu inati, “Kodi ife takusankha iwe kuti ukhale mlangizi wa mfumu? Khala chete! Ufuna kuphedweranji?”

Choncho mneneriyo analeka koma anati, “Ine ndikudziwa kuti Mulungu watsimikiza kukuwonongani chifukwa mwachita izi ndipo simunamvere uphungu wanga.”

17Amaziya mfumu ya ku Yuda, atafunsa alangizi ake, anatumiza mawu awa kwa Yowasi mwana wa Yehowahazi mwana wa Yehu, mfumu ya Israeli: “Bwera udzakumane nane maso ndi maso.”

18Koma Yowasi mfumu ya Israeli inayankha Amaziya mfumu ya Yuda kuti, “Nthawi ina kamtengo kaminga ka ku Lebanoni kanatumiza mawu kwa mkungudza wa ku Lebanoni kuti, ‘Pereka mwana wako wamkazi kwa mwana wanga kuti amukwatire!’ Koma chirombo cha ku Lebanoni chinabwera ndi kupondaponda mtengo wa minga uja. 19Iwe ukuti wagonjetsa Edomu, ndipo tsopano ukudzikuza ndi kudzitamandira, koma khala kwanu komweko! Nʼchifukwa chiyani ukufuna mavuto ndi kudzichititsa kuti ugwe pamodzinso ndi Yuda?”

20Komabe Amaziya sanamvere pakuti ndi Mulungu amene anakonzeratu kuti awapereke kwa Yehowasi, chifukwa iwo amapembedza milungu ya ku Edomu. 21Kotero Yowasi mfumu ya Israeli inakamuthira nkhondo. Iye ndi Amaziya anayangʼanana maso ndi maso ku Beti-Semesi ku Yuda. 22Yuda anagonjetsedwa ndi Israeli ndipo munthu aliyense anathawira kwawo. 23Yehowahazi mfumu ya Israeli inagwira Amaziya mfumu ya Yuda, mwana wa Yowasi, mwana wa Ahaziya ku Beti-Semesi. Yehowasi anabwera naye ku Yerusalemu ndipo anagwetsa khoma la Yerusalemu kuyambira pa Chipata cha Efereimu mpaka ku Chipata Chapangodya, khoma lotalika mamita 180. 24Iye anatenga golide ndi siliva yense ndi zida zonse zimene zimapezeka mʼNyumba ya Mulungu zimene ankazisamalira Obedi-Edomu, pamodzinso ndi chuma cha mʼnyumba yaufumu ndipo anatenga anthu ngati chikole.

25Amaziya mwana wa Yowasi mfumu ya Yuda anakhala ndi moyo kwa zaka khumi ndi zisanu atamwalira Yehowasi mwana wa Yehowahazi mfumu ya Israeli. 26Ntchito zina za mfumu Amaziya, kuyambira pachiyambi mpaka pa mapeto, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mafumu a Yuda ndi Israeli? 27Kuyambira nthawi imene Amaziya analeka kutsatira Yehova anthu anamukonzera chiwembu mu Yerusalemu ndipo anathawira ku Lakisi, koma adaniwo anatumiza anthu ku Lakisiko ndipo anamupha komweko. 28Iwo anabwera naye ali pa kavalo ndipo anayikidwa mʼmanda ndi makolo ake mu mzinda wa Yuda.

Bibelen på hverdagsdansk

2. Krønikebog 25:1-28

Kong Amatzja af Juda

2.Kong. 14,1-20

1Amatzja var 25 år gammel, da han blev konge, og han regerede i Jerusalem i 29 år. Hans mor hed Jehoaddan og var fra Jerusalem. 2Han gjorde, hvad der var ret i Herrens øjne, men ikke helhjertet. 3Så snart han havde sikret sig magten, dræbte han de embedsmænd, der havde myrdet hans far. 4Men han skånede deres børn, for Herrens lov siger: „Forældre må ikke straffes for deres børns synder, og børn må ikke straffes for deres forældres synder. Dødsstraf kan kun idømmes den, der selv er ansvarlig for sin forbrydelse.”25,4 Jf. 5.Mos. 24,16.

5Amatzja indkaldte nu alle mændene i Judas og Benjamins land til tjeneste i hæren og organiserede dem under militære ledere efter hvilke slægter, de tilhørte. Det samlede antal våbenføre mænd over 20 år, som kunne håndtere spyd og sværd, blev optalt til 300.000. 6Derudover hyrede han 100.000 erfarne lejesoldater fra Efraim i Israel til en sum af 3,5 tons25,6 På hebraisk: „100 talenter”. sølv.

7Da kom en Guds mand til ham og sagde: „Herre konge, du bør ikke tage lejesoldaterne fra Israel med i krigen, for Herren er ikke med dem. 8Hvis du tager dem med, vil I blive besejret, lige meget hvor tappert I kæmper, for Gud har magt til at give enten jer eller jeres fjender sejren.”25,8 Teksten er uklar. 9„Jamen, hvad så med alle de penge, jeg har betalt for soldaterne?” indvendte Amatzja. „Herren kan give dig langt mere igen!” svarede profeten.

10Så sendte Amatzja lejesoldaterne tilbage til Efraim. Det tog de meget ilde op og blev rigtig godt sure på judæerne. 11Derefter tog Amatzja mod til sig og rykkede frem til Saltdalen, hvor hans mænd dræbte 10.000 soldater fra Seirs bjerge. 12Andre 10.000 blev taget til fange og ført op på en klippetop. Her blev de smidt ud over kanten, så de knustes mod klippen nedenunder.

13I mellemtiden hævnede de hjemsendte israelitter sig på de judæere, der boede i byerne i området mellem Bet-Horon og Samaria. De dræbte 3000 mennesker og røvede et stort bytte.

14Da kong Amatzja vendte hjem efter sejren over edomitterne, medbragte han flere af deres afgudsbilleder. Dem satte han op og begyndte at dyrke dem ved at kaste sig på knæ foran dem og brænde røgelse for dem. 15Da blev Herren vred og sendte en profet til Amatzja med følgende budskab: „Hvorfor beder du til de guder, der ikke kunne frelse deres eget folk?” 16„Siden hvornår har jeg bedt dig om råd?” snerrede kongen. „Ti stille, eller jeg slår dig ihjel!” Da forlod profeten ham med afskedsordene: „Nu ved jeg, at Gud har planer om at tilintetgøre dig, siden du ikke vil lytte til min advarsel!”

17Kong Amatzja af Juda rådførte sig i stedet med sine rådgivere og udstedte derefter en krigserklæring til kong Joash af Israel, der var søn af Joahaz, som var søn af Jehu.

18Kong Joash sendte følgende besked tilbage:

„Der var engang en tidsel i Libanon, som sagde til det statelige cedertræ: ‚Lad min søn få din datter til ægte!’ Men et vildt dyr kom løbende forbi og trampede tidslen ned. 19Du er hovmodig og stolt på grund af din sejr over Edom, men bliv du hellere hjemme og nyd sejren. Hvorfor udfordre skæbnen og styrte både dig selv og Judas land i ulykke?”

20Men Amatzja ville ikke høre efter, for Gud havde i sinde at udlevere ham til kong Joash, fordi han havde antaget Edoms afguder. 21Joash mobiliserede sin hær og mødte Amatzjas hær ved byen Bet-Shemesh i Juda. 22Dér blev judæerne besejret, og soldaterne flygtede hver til sit. 23Amatzja blev taget til fange, hvorefter Israels hær marcherede mod Jerusalem og ødelagde bymuren mellem Efraims port og Hjørneporten, en strækning på 200 meter. 24Joash tog det guld og sølv og de andre kostbarheder, der var tilbage i templets skatkamre under Obed-Edoms opsyn. Han tog også alle skattene i kongens palads og en del gidsler, hvorefter han vendte hjem til Samaria.

25Amatzja levede 15 år mere, efter at Joash var død, 26og hans livshistorie fra begyndelsen til enden står skrevet i Judas og Israels kongers krønikebog. 27Efter at Amatzja vendte sig bort fra Herren, havde hans embedsmænd i Jerusalem planer om at slå ham ihjel, men det lykkedes ham at flygte til Lakish. De sendte så nogle folk efter ham til Lakish, og han blev dræbt dernede. 28Hans lig blev bragt hjem til Jerusalem til hest, og han blev begravet sammen med sine forfædre i Judas hovedstad.25,28 Eller: „Davidsbyen”, som der står i LXX.