2 Mbiri 24 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Mbiri 24:1-27

Yowasi Akonzanso Nyumba ya Mulungu

1Yowasi anali wa zaka zisanu ndi ziwiri pamene anakhala mfumu, ndipo analamulira mu Yerusalemu kwa zaka makumi anayi. Dzina la amayi ake linali Zibiya wa ku Beeriseba. 2Yowasi anachita zolungama pamaso pa Yehova nthawi yonse ya moyo wa wansembe Yehoyada. 3Yehoyada anamupezera iye akazi awiri, ndipo anabereka ana aamuna ndi aakazi.

4Patapita nthawi Yowasi anatsimikiza zokonzanso Nyumba ya Yehova. 5Iye anayitanitsa pamodzi ansembe ndi Alevi ndipo anawawuza kuti, “Pitani ku mizinda ya Yuda ndi kukasonkhetsa ndalama za pa chaka kwa Aisraeli onse zokonzera Nyumba ya Mulungu wanu. Chitani zimenezi tsopano.” Koma Alevi sanachite zimenezi mwachangu.

6Choncho mfumu inayitanitsa Yehoyada, mkulu wa ansembe ndipo inati kwa iye, “Kodi nʼchifukwa chiyani simunawuze Alevi kuti asonkhetse ndalama ku Yuda ndi Yerusalemu, msonkho umene anakhazikitsa Mose mtumiki wa Yehova ndiponso gulu lonse la Aisraeli mu tenti yaumboni?”

7Ana a mkazi woyipa, Ataliya, anathyola chitseko cha Nyumba ya Mulungu ndipo anagwiritsa ntchito zinthu zopatulika popembedza Baala.

8Mfumu italamulira, bokosi linapangidwa ndipo linayikidwa panja pa chipata cha Nyumba ya Yehova. 9Ndipo analengeza kwa anthu a mu Yuda ndi mu Yerusalemu kuti abweretse kwa Yehova msonkho umene Mose mtumiki wa Mulungu analamulira Aisraeli mʼchipululu. 10Akuluakulu onse ndi anthu onse anabweretsa zopereka zawo mokondwera ndipo anaziponya mʼbokosi mpaka linadzaza. 11Nthawi ina iliyonse imene Alevi abweretsa bokosilo kwa akuluakulu a mfumu ndipo akaona kuti muli ndalama zambiri, mlembi waufumu ndi nduna yayikulu ya mkulu wa ansembe amabwera ndi kuchotsa ndalama mʼbokosi muja ndipo amalitenga kukaliyika pamalo pake. Iwo amachita izi nthawi ndi nthawi ndipo anapeza ndalama zambiri. 12Mfumu pamodzi ndi Yehoyada anapereka ndalamazo kwa anthu oyangʼanira ntchito ku Nyumba ya Yehova. Analemba ntchito amisiri a miyala ndi a matabwa kuti akonzenso Nyumba ya Yehova. Analembanso ntchito amisiri a zitsulo ndi mkuwa kuti akonze Nyumba ya Mulungu.

13Anthu amene ankagwira ntchito anali odziwa bwino, ndipo ntchitoyo inagwiridwa bwino ndi manja awo. Iwo anamanganso Nyumba ya Mulungu motsatira mapangidwe ake oyamba ndipo anayilimbitsa. 14Atamaliza, iwo anabweretsa ndalama zotsala kwa mfumu ndi Yehoyada, ndipo anazigwiritsira ntchito popangira zida za mʼNyumba ya Yehova: ziwiya zogwiritsa ntchito potumikira ndi popereka nsembe zopsereza, komanso mbale ndi ziwiya zagolide ndi siliva. Nthawi yonse ya moyo wa Yehoyada, nsembe zopsereza zinkaperekedwa mosalekeza mʼNyumba ya Yehova.

15Tsono Yehoyada anakalamba ndipo anali ndi zaka zambiri. Pambuyo pake iye anamwalira ali ndi zaka 130. 16Iyeyo anayikidwa mʼmanda pamodzi ndi mafumu mu mzinda wa Davide chifukwa cha zabwino zimene anachita mu Israeli, kuchitira Mulungu ndi Nyumba yake.

Kuyipa kwa Yowasi

17Atamwalira Yehoyada, akuluakulu a Yuda anabwera kudzapereka ulemu kwa mfumu, ndipo mfumu inawamvera. 18Iwo anasiya Nyumba ya Yehova, Mulungu wa makolo awo ndipo anapembedza Asera ndi mafano. Chifukwa cha kulakwa kwawo, mkwiyo wa Yehova unabwera pa Yuda ndi Yerusalemu. 19Ngakhale Yehova anatumiza aneneri kwa anthuwo kuti awabweze kwa Iye, ngakhale aneneri ananenera mowatsutsa, anthuwo sanamvere.

20Kenaka Mzimu wa Mulungu unabwera pa Zekariya mwana wa wansembe Yehoyada. Iye anayimirira pamaso pa anthu ndipo anati, “Zimene Mulungu akunena ndi Izi: ‘Chifukwa chiyani simukumvera Malamulo a Yehova? Simudzapindula. Chifukwa mwasiya Yehova, Iyenso wakusiyani.’ ”

21Koma anthuwo anamuchitira chiwembu molamulidwa ndi mfumu ndipo anamugenda miyala ndi kumupha mʼbwalo la Nyumba ya Mulungu. 22Mfumu Yowasi sinakumbukire zabwino zimene Yehoyada abambo ake a Zekariya anamuchitira, koma anapha mwana wake. Pamene amafa, iye ananena kuti, “Yehova aone zimenezi ndipo abwezere chilango.”

23Pakutha kwa chaka, gulu lankhondo la Aramu linadzamenyana ndi Yowasi. Linalowa mu Yuda ndi mu Yerusalemu ndi kupha atsogoleri onse a anthu. Zonse zimene analanda anazitumiza kwa mfumu ya ku Damasiko. 24Ngakhale kuti gulu lankhondo la Aramu linabwera ndi anthu ochepa okha, Yehova anapereka mʼmanja mwawo gulu lalikulu lankhondo. Chifukwa Yuda anasiya Yehova Mulungu wa makolo awo, chiweruzo chinachitika pa Yowasi. 25Pamene Aaramu amachoka, anasiya Yowasi atavulazidwa kwambiri. Akuluakulu ake anamuchitira chiwembu chifukwa anapha mwana wa wansembe Yehoyada, ndipo anamupha ali pa bedi pake. Choncho anafa ndipo anayikidwa mʼmanda mu mzinda wa Davide, koma osati manda a mafumu.

26Iwo amene anamuchitira chiwembu anali Zabadi mwana wa Simeati, mkazi wa ku Amoni, ndi Yehozabadi mwana wa Simiriti, mkazi wa ku Mowabu. 27Za ana ake aamuna, uneneri wonena za iye, mbiri ya kumanganso Nyumba ya Mulungu, zalembedwa mʼbuku lofotokoza za mafumu. Ndipo Amaziya mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake.