2 Mbiri 21 – CCL & CCBT

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Mbiri 21:1-20

1Yehosafati anamwalira nayikidwa mʼmanda pamodzi ndi makolo ake mu mzinda wa Davide. Ndipo Yehoramu mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake. 2Abale ake a Yehoramu, ana aamuna a Yehosafati, anali Azariya, Yehieli, Zekariya, Azariyahu, Mikayeli ndi Sefatiya. Onsewa anali ana a Yehosafati mfumu ya Israeli. 3Abambo awo anawapatsa mphatso zambiri za siliva, golide ndi zinthu zina zamtengowapatali komanso mizinda yotetezedwa ya Yuda. Koma iye anapereka ufumu kwa Yehoramu chifukwa anali mwana wake woyamba kubadwa.

Yehoramu Mfumu ya Yuda

4Yehoramu atakhazikika pa ufumu wa abambo ake, iye anapha abale ake ndi lupanga pamodzi ndi atsogoleri ena a Israeli. 5Yehoramu anali wa zaka 32 pamene anakhala mfumu, ndipo analamulira mu Yerusalemu zaka zisanu ndi zitatu. 6Iye anayenda mʼnjira za mafumu a Israeli, monga mmene linachitira banja la Ahabu, pakuti anakwatira mwana wa Ahabu. Ndipo anachita zoyipa pamaso pa Yehova. 7Komabe, chifukwa cha pangano limene Yehova anachita ndi Davide, Yehova sanafune kuwononga banja la Davide. Iye analonjeza kusungira nyale Davide ndi zidzukulu zake mpaka muyaya.

8Pa nthawi ya Yehoramu, Edomu anawukira Yuda ndipo anadzisankhira mfumu. 9Choncho Yehoramu anapita kumeneko pamodzi ndi atsogoleri ake ndi magaleta ake onse. Aedomu anamuzungulira pamodzi ndi atsogoleri ake koma iye ananyamuka ndi kuthawa usiku. 10Mpaka lero lino Edomu ndi wowukira ulamuliro wa Yuda.

Pa nthawi yomweyi, mzinda wa Libina unawukiranso chifukwa Yehoramu anasiya Yehova, Mulungu wa makolo ake. 11Iye anamanganso malo opembedzerapo mafano mʼmapiri a Yuda ndipo anachititsa anthu a mu Yerusalemu kukhala osakhulupirika. Choncho anasocheretsa anthu a ku Yuda.

12Yehoramu analandira kalata yochokera kwa mneneri Eliya yonena kuti,

“Yehova Mulungu wa Davide abambo ako akuti, ‘Iwe sunayende mʼnjira ya Yehosafati abambo ako kapena Asa mfumu ya Yuda. 13Koma wayenda mʼnjira za mafumu a Israeli ndipo watsogolera anthu a ku Yuda ndi Yerusalemu kukhala osakhulupirika, monga linachitira banja la Ahabu. Waphanso abale ako, abale a banja la abambo ako, anthu amene anali abwino kuposa iweyo. 14Kotero tsono Yehova ali pafupi kukantha anthu ako, ana ako, akazi ako ndi zinthu zako zonse, ndi chilango chachikulu. 15Ndipo iwe udzadwala nthenda yoopsa yamʼmimba, mpaka nthendayo idzachititsa matumbo ako kutuluka.’ ”

16Yehova anamuutsira Yehoramuyo mkwiyo wa Afilisti ndi Aarabu amene amakhala pafupi ndi Akusi. 17Iwo anathira nkhondo Yuda. Analowanso ndi kutenga katundu yense amene anamupeza mʼnyumba ya mfumu pamodzi ndi ana ake ndi akazi ake. Palibe mwana amene anatsala kupatula mwana wake wamngʼono kwambiri, Ahaziya.

18Izi zonse zitachitika, Yehova anakantha Yehoramu ndi nthenda yamʼmimba imene inali yosachiritsika. 19Patapita nthawi, kumapeto kwa chaka chachiwiri, matumbo ake anatuluka chifukwa cha nthendayo, ndipo anafa imfa yopweteka kwambiri. Anthu ake sanasonkhe moto kumuchitira ulemu, monga anachitira ndi makolo ake.

20Yehoramu anali wa zaka 32 pamene anakhala mfumu. Iyeyo analamulira mu Yerusalemu zaka zisanu ndi zitatu. Ndipo anamwalira popanda odandawula, nayikidwa mʼmanda mu mzinda wa Davide, koma osati mʼmanda a mafumu.

Chinese Contemporary Bible (Traditional)

歷代志下 21:1-20

1約沙法與祖先同眠後,葬在大衛城他的祖墳裡。他兒子約蘭繼位。

猶大王約蘭

2亞撒利雅耶歇撒迦利雅亞撒列夫米迦勒示法提雅約蘭的兄弟、猶大約沙法的兒子。 3他們的父親賜給他們許多金銀、財寶和猶大境內的堅城,但將王位賜給了約蘭,因為他是長子。 4約蘭登基,鞏固了王位後,就用刀殺了他所有的兄弟和一些以色列首領。 5約蘭三十二歲登基,在耶路撒冷執政八年。 6他與亞哈家一樣步以色列諸王的後塵,因為他娶了亞哈的女兒為妻,做耶和華視為惡的事。 7但耶和華不願毀滅大衛家,因為祂曾與大衛立約,應許讓大衛和他的子孫永遠做王。

8約蘭執政期間,以東人反叛猶大,自己立王。 9約蘭率將領及所有戰車前去討伐,結果被以東人包圍。但他們乘夜突出重圍。 10以東人至今仍脫離猶大的統治,立拿人也在那時候叛變了,因為約蘭背棄了他祖先的上帝耶和華。 11約蘭猶大的山上修建邱壇,引誘耶路撒冷的居民和猶大人與假神苟合。

12以利亞先知寫信給約蘭說:「你祖先大衛的上帝耶和華這樣說,『因為你沒有效法你父親約沙法,也沒有效法猶大亞撒13而是重蹈以色列諸王的覆轍,與亞哈家一樣,引誘猶大人和耶路撒冷的居民與假神苟合,還殺了比你好的兄弟。 14因此,耶和華要降大災禍給你的人民、兒女、妻妾及一切所有。 15你必患嚴重的腸病,並且日益加重,直到你的腸子掉出來。』」

16耶和華驅使非利士人和古實附近的阿拉伯人攻打約蘭17他們起兵攻打猶大,侵入境內,擄走了王宮裡的所有財物以及約蘭的兒子和妻妾,只留下他最小的兒子約哈斯

18這事以後,耶和華使約蘭患了無法醫治的腸病, 19日益加重,兩年後腸子掉了出來,他痛苦地死去了。他的百姓沒有像對待他祖先那樣向他焚火致哀。 20約蘭三十二歲登基,在耶路撒冷執政八年。他死後無人向他致哀。他葬在大衛城,但沒有葬在王陵裡。