2 Mbiri 20 – CCL & CARS

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Mbiri 20:1-37

Yehosafati Agonjetsa Mowabu ndi Amoni

1Zitatha izi, Amowabu ndi Aamoni pamodzi ndi Ameuni ena anabwera kudzachita nkhondo ndi Yehosafati.

2Anthu ena anabwera kudzamuwuza Yehosafati kuti, “Gulu lalikulu kwambiri lankhondo likubwera kudzachita nanu nkhondo lochokera ku Edomu, ku mbali ina ya Nyanja. Gululi lafika kale ku Hazazoni Tamara” (ndiye kuti Eni-Gedi). 3Ndi mantha, Yehosafati anaganiza zofunsira kwa Yehova, ndipo analengeza kuti Ayuda onse asale zakudya. 4Anthu a ku Yuda anabwera pamodzi kudzafuna thandizo kwa Yehova, ndipo anabweradi kuchokera ku mzinda uliwonse wa mu Yuda kudzafunafuna Yehova.

5Yehosafati anayimirira pakati pa msonkhano wa Yuda ndi Yerusalemu, pa Nyumba ya Yehova patsogolo pa bwalo latsopano 6ndipo anati:

“Inu Yehova, Mulungu wa makolo athu, kodi Inu sindinu Mulungu amene muli kumwamba? Inu mumalamulira maufumu onse a mitundu ya anthu. Mphamvu ndi nyonga zili mʼmanja mwanu, ndipo palibe amene angalimbane nanu. 7Inu Mulungu wathu, kodi simunathamangitse nzika za dziko lino pamaso pa anthu anu Aisraeli ndipo munalipereka kwa zidzukulu za Abrahamu bwenzi lanu kwamuyaya? 8Iwo akhala mʼdzikolo ndipo anamangira Dzina lanu malo opatulika, nʼkumati, 9‘Ngati tsoka litigwera kaya ndi lupanga lachiweruzo, kapena mliri, kapenanso njala, ife tidzayima pamaso panu patsogolo pa Nyumba ya Mulungu ino imene imatchedwa ndi Dzina lanu ndipo tidzalirira kwa inu mʼmasautso athu, ndipo Inu mudzatimvera ndi kutipulumutsa.’

10“Koma tsopano pano pali anthu ochokera ku Amoni, Mowabu ndi Phiri la Seiri amene dziko lawo Inu simunawalole Aisraeli kuti alithire nkhondo pamene amabwera kuchokera ku Igupto. Kotero anatembenuka ndi kuwaleka ndipo sanawawononge. 11Taonani, mmene akutibwezera ife pobwera kudzatithamangitsa mʼdziko limene inu munatipatsa ngati cholowa chathu. 12Inu Mulungu wathu, kodi simuwaweruza? Pakuti ife tilibe mphamvu zolimbana ndi gulu lalikulu lankhondo limene likutithira nkhondoli. Ife sitikudziwa choti tichite, koma maso athu ali pa Inu.”

13Anthu onse a Yuda, pamodzi ndi akazi awo ndi ana ndi makanda, anayima chilili pamaso pa Yehova.

14Ndipo Mzimu wa Yehova unabwera pa Yahazieli mwana wa Zekariya, mwana wa Benaya, mwana wa Yeiyeli, mwana wa Mataniya Mlevi, chidzukulu cha Asafu, atayimirira mu msonkhano.

15Iye anati, “Tamverani mfumu Yehosafati ndi onse amene amakhala mu Yuda ndi Yerusalemu! Zimene Yehova akunena kwa inu ndi izi: ‘Musaope kapena kutaya mtima chifukwa cha gulu lalikulu lankhondo ili. Pakuti nkhondoyi si yanu, koma ya Mulungu. 16Mawa mupite mukamenyane nawo. Adzakhala akubwera mokweza kudzera Njira ya Zizi, ndipo mukawapeza kumapeto kwa chigwa cha ku chipululu cha Yeruweli. 17Sikudzafunika kuti Inu mumenyane nawo pa nkhondo imeneyi. Inu mukhale pa malo anu; imani molimba ndipo onani chipulumutso chimene Yehova adzakupatsani, Inu Yuda ndi Yerusalemu. Musaope, musataye mtima. Pitani kuti mukakumane nawo mawa, ndipo Yehova adzakhala nanu.’ ”

18Yehosafati anaweramitsa nkhope yake ndi kugunda pansi, ndiponso anthu onse a Yuda ndi Yerusalemu anagwa pansi ndi kulambira Yehova. 19Kenaka Alevi ena ochokera ku mabanja a Kohati ndi Kora anayimirira ndipo anatamanda Yehova Mulungu wa Israeli ndi mawu ofuwula kwambiri.

20Mmamawa, ananyamuka kupita ku chipululu cha Tekowa. Akunyamuka, Yehosafati anayimirira ndipo anati, “Tandimverani ine anthu a Yuda ndi Yerusalemu! Khalani ndi chikhulupiriro mwa Yehova Mulungu wanu ndipo mudzatchinjirizidwa, khalani ndi chikhulupiriro mwa aneneri ake ndipo mudzapambana.” 21Atafunsira kwa anthu, Yehosafati anasankha anthu oti ayimbire Yehova ndi kumutamanda chifukwa cha ulemerero wa chiyero chake pamene amapita ali patsogolo pa gulu la ankhondo, akunena kuti:

“Yamikani Yehova

pakuti chikondi chake ndi chosatha.”

22Atangoyamba kuyimba ndi kutamanda, Yehova anapereka mʼmanja mwawo anthu a ku Amoni ndi a ku Mowabu ndiponso a ku Phiri la Seiri amene amalimbana ndi Yuda, ndipo anagonjetsedwa. 23Anthu a ku Amoni ndi a ku Mowabu anawukira anthu ochokera ku Phiri la Seiri, ndipo anawawononga ndi kuwatheratu. Atatsiriza kuwapha anthu ochokera ku Seiri anamenyana wina ndi mnzake mpaka kuwonongana.

24Anthu a ku Yuda atafika pa malo oyangʼanana ndi chipululu ndi kuona kumene kunali gulu lalikulu lankhondo, iwo anangoona mitembo yokhayokha itagona pansi ndipo palibe amene anathawa. 25Choncho Yehosafati ndi anthu ake anapita kukafunkha, ndipo pakati pawo anapeza katundu wambiri ndi zovala ndiponso zinthu zina zamtengowapatali kuposa zomwe akanatha kunyamula. Kunali katundu wambiri kotero kuti zinawatengera masiku atatu kuti amutenge. 26Tsiku lachinayi anasonkhana ku chigwa cha Beraka kumene anatamanda Yehova. Nʼchifukwa chake malowa amatchedwa chigwa cha Beraka mpaka lero.

27Tsono motsogozedwa ndi Yehosafati, anthu onse a Yuda ndi Yerusalemu anabwerera ku Yerusalemu mokondwera pakuti Yehova anawagonjetsera adani awo. 28Iwo analowa mu Yerusalemu ndipo anapita ku Nyumba ya Mulungu akuyimba azeze, apangwe ndi malipenga.

29Kuopsa kwa Mulungu kunali pa maufumu onse a mayiko amene anamva mmene Yehova anamenyera adani a Aisraeli. 30Ndipo ufumu wa Yehosafati unali pa mtendere pakuti Mulungu wake anamupatsa mpumulo ku mbali zonse.

Kutha kwa Ufumu wa Yehosafati

31Choncho Yehosafati analamulira Yuda. Iye anali wa zaka 35 pamene anakhala mfumu ya Yuda ndipo analamulira mu Yerusalemu kwa zaka 25. Dzina la amayi ake linali Azuba mwana wa Sili. 32Iye ankayenda mʼnjira za Asa abambo ake ndipo sanapatuke pa zimenezi pakuti anachita zolungama pamaso pa Yehova. 33Komabe malo opembedzerapo mafano sanachotsedwe ndipo anthu sanaperekebe mitima yawo kwa Mulungu wa makolo awo.

34Zochitika zina zokhudza ufumu wa Yehosafati, kuyambira pachiyambi mpaka pa mapeto, zalembedwa mʼbuku la Yehu mwana wa Hanani, zomwe zikupezeka mʼbuku la mbiri ya mafumu a Israeli.

35Zitapita izi, Yehosafati mfumu ya Yuda inachita mgwirizano ndi Ahaziya mfumu ya Israeli, amene anachita zoyipa kwambiri. 36Iye anagwirizana ndi Ahaziya kuti apange sitima zapamadzi zochitira malonda. Atazipanga zimenezi ku Ezioni-Geberi, 37Eliezara mwana wa Dodavahu wa ku Maresa ananenera motsutsana ndi Yehosafati ndipo anati, “Chifukwa chakuti wachita mgwirizano ndi Ahaziya, Yehova adzawononga zimene mwapangazo!” Sitima za pamadzizo zinawonongeka ndipo sizinapite nʼkomwe kumene zimakachita malonda.

Священное Писание

2 Летопись 20:1-37

Поражение моавитян, аммонитян и жителей Сеира

1После этого моавитяне и аммонитяне с некоторыми из меунитян пришли, чтобы воевать с Иосафатом. 2Вестники пришли и доложили Иосафату:

– Из Эдома20:2 Или: «Сирии»., из-за Мёртвого моря, против тебя движется огромное войско. Они уже в Хацацон-Тамаре (то есть в Ен-Геди).

3Встревожившись, Иосафат решил вопросить Вечного и объявил по всей Иудее пост. 4Народ Иудеи собрался, чтобы искать помощи у Вечного, люди пришли из всех городов Иудеи, чтобы искать Его. 5Иосафат встал в собрании жителей Иудеи и Иерусалима в храме Вечного, перед новым двором, 6и сказал:

– Вечный, Бог наших предков, разве Ты не Бог, Который на небесах? Ты правишь всеми царствами народов. В Твоей руке власть и мощь, и никто не может противостоять Тебе. 7Бог наш, разве Ты не прогнал обитателей этой земли перед Твоим народом Исраилом и не отдал её навеки потомкам Ибрахима, Твоего друга? 8Они жили в ней и построили в ней святилище для поклонения Тебе, говоря: 9«Если к нам придёт беда, будь то меч наказания, мор или голод, мы предстанем пред Тобою перед этим храмом, в котором Ты пребываешь, и воззовём к Тебе в нашем горе, и Ты услышишь и спасёшь нас».

10Но вот явились жители Аммона, Моава и горы Сеир, чьи земли Ты не позволил завоевать исраильтянам, когда они вышли из Египта, и они свернули в сторону от них и не погубили их. 11Взгляни же, чем они воздают нам, явившись, чтобы выгнать нас из наших владений, которые Ты дал нам в наследие. 12Бог наш, неужели Ты не осудишь их? Ведь у нас нет сил, чтобы противостоять этому огромному войску, которое идёт на нас. Мы не знаем, что нам делать, но глаза наши устремлены на Тебя.

13Все мужчины Иудеи со своими жёнами, младенцами и старшими детьми предстали там пред Вечным. 14И Дух Вечного сошёл на Иахазиила, когда тот стоял в собрании. Иахазиил был сыном Закарии. Закария был сыном Бенаи. Беная был сыном Иеила. Иеил был сыном Маттании, левита и потомка Асафа. 15Иахазиил сказал:

– Слушайте, все жители Иудеи и Иерусалима и царь Иосафат! Так говорит вам Вечный: «Не бойтесь и не ужасайтесь из-за этого огромного войска. Ведь битва эта не ваша, а Всевышнего. 16Выступайте завтра против этих людей. Они будут подниматься по перевалу Циц, и вы найдёте их в конце долины перед пустыней Иеруил. 17Не вам биться в этом сражении. Вы лишь встаньте, стойте и смотрите на спасение Вечного, которое Он даст вам, Иудея с Иерусалимом. Не бойтесь, не ужасайтесь. Выходите завтра навстречу этим людям, и Вечный будет с вами».

18Иосафат поклонился лицом до земли, и все жители Иудеи и Иерусалима пали на колени перед Вечным, чтобы поклониться Ему. 19И некоторые левиты из каафитов и корахитов встали, чтобы во весь голос славить Вечного, Бога Исраила.

20Ранним утром войско Иосафата тронулось в путь к пустыне Текоа. Когда они выходили, Иосафат встал и сказал:

– Слушайте меня, Иудея с Иерусалимом! Верьте Вечному, вашему Богу, и вы будете непоколебимы, верьте Его пророкам, и вам будет сопутствовать успех.

21Посоветовавшись с народом, Иосафат назначил людей, которые должны были петь для Вечного и славить великолепие Его святости20:21 Или: «славить Его в святом облачении»; или: «славить Его в великолепном святилище»., идя во главе войска и говоря:

– Славьте Вечного,

потому что милость Его – навеки!

22Когда они начали петь и славить, Вечный возбудил вражду между моавитянами, аммонитянами и жителями горы Сеир, которые вторглись в Иудею, и те были разгромлены. 23Аммонитяне и моавитяне напали на жителей горы Сеир, чтобы губить и уничтожать их, а покончив с жителями Сеира, принялись убивать друг друга.

24Когда народ Иудеи добрался до сторожевой башни над пустыней и взглянул на огромное войско, они увидели только мёртвые тела, лежавшие на земле: никто не уцелел. 25Когда Иосафат со своими людьми пришли, чтобы забрать у них свою добычу, они нашли у них много добра, одежды и дорогих вещей – больше, чем могли унести. Добычи было так много, что им пришлось собирать её три дня. 26На четвёртый день они собрались в долине Бераха, где прославляли Вечного. Вот почему до сегодняшнего дня она называется долиной Бераха («благословение»).

27Затем под предводительством Иосафата все мужчины Иудеи и Иерусалима с радостью вернулись в Иерусалим, потому что Вечный дал им повод возрадоваться над своими врагами. 28Они вступили в Иерусалим и пошли к храму Вечного с лирами, арфами и трубами.

29Страх перед Всевышним напал на все царства окружающих земель, когда они услышали, как Вечный сразился с врагами Исраила. 30И в царстве Иосафата был мир, потому что Вечный даровал ему покой со всех сторон.

Конец правления Иосафата

(3 Цар. 22:41-50)

31Так Иосафат правил Иудеей. Ему было тридцать пять лет, когда он стал царём, и правил он в Иерусалиме двадцать пять лет. Его мать звали Азува, она была дочерью Шилхи. 32Он ходил путями своего отца Асы и не уклонялся от них, делая то, что было правильным в глазах Вечного. 33Но святилища на возвышенностях не были уничтожены, и народ всё ещё не обратил своё сердце к Богу их предков.

34Прочие события царствования Иосафата, от первых до последних, записаны в «Летописях Иеву, сына Ханани», которые включены в «Книгу царей Исраила».

35Впоследствии Иосафат, царь Иудеи, заключил договор с Охозией, царём Исраила, который творил беззакония. 36Он договорился с ним построить флотилию торговых кораблей20:36 Букв.: «кораблей, могущих ходить в Фарсис».. Когда они были построены в Эцион-Гевере, 37Элиезер, сын Додавагу из Мареши, изрёк пророчество против Иосафата, сказав:

– Раз ты заключил договор с Охозией, Вечный разрушит то, что ты построил.

Корабли разбились и не смогли отплыть для торговли20:37 Или: «отплыть в Фарсис»..