2 Mbiri 19 – CCL & CARSA

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Mbiri 19:1-11

1Yehosafati, mfumu ya Yuda itabwerera mwamtendere ku nyumba yake yaufumu ku Yerusalemu, 2mlosi Yehu, mwana wa Hanani, anatuluka kukakumana naye ndipo anati kwa mfumu, “Kodi nʼkoyenera kuthandiza oyipa ndi kukonda iwo amene amadana ndi Yehova? Chifukwa cha zimenezi mkwiyo wa Yehova uli pa inu. 3Komabe, muli zinthu zina zabwino mwa inu, pakuti inu mwachotsa mʼdziko muno mafano a Asera ndipo mwakhazikitsa mtima wanu pa kufunafuna Mulungu.”

Yehosafati Asankha Oweruza

4Yehosafati anakakhala ku Yerusalemu, ndipo amayenda pakati pa anthu kuchokera ku Beeriseba mpaka ku dziko lamapiri la Efereimu ndipo anawatembenuzira kwa Yehova, Mulungu wa makolo awo. 5Iye anasankha oweruza mʼdzikomo, mu mzinda uliwonse wotetezedwa wa Yuda. 6Ndipo anawawuza kuti, “Muganize bwino zimene mukuchita, chifukwa simukuweruza mʼmalo mwa munthu koma Yehova, amene ali nanu pamene mukupereka chiweruzo. 7Tsopano kuopsa kwa Yehova kukhale pa inu. Muweruze mosamala, pakuti ndi Yehova Mulungu wathu palibe kupotoza chilungamo kapena kukondera kapenanso kulandira ziphuphu.”

8Mu Yerusalemu, Yehosafati anasankha Alevi ena, ansembe ndi atsogoleri a mabanja a Aisraeli kuti aziyangʼanira Malamulo a Yehova ndi kuweruza milandu. Ndipo iwo amakhala mu Yerusalemu. 9Iye anawalamula kuti, “Inu mutumikire mokhulupirika ndi mtima wanu wonse moopa Yehova. 10Pa mlandu uliwonse wobwera kwa inu kuchokera kwa abale anu amene amakhala mʼmizinda, mlandu wokhetsa magazi kapena mlandu wosamvera malamulo kapena malangizo kapena ziphunzitso zina, inu muziwachenjeza kuti asachimwire Yehova pakuti mukapanda kutero mkwiyo wake udzakhala pa inu ndi abale anu. Chitani zimenezi ndipo simudzachimwa.

11“Amariya, mkulu wa ansembe adzakhala wokuyangʼanirani pa zonse zokhudza Yehova, ndipo Zebadiya mwana wa Ismaeli, mtsogoleri wa fuko la Yuda, adzakhala wokuyangʼanirani pa zonse zokhudza mfumu ndipo Alevi adzatumikira ngati okuyangʼanirani. Muchite molimba mtima ndipo Yehova akhale ndi iwo amene adzachita bwino.”

Священное Писание (Восточный перевод), версия с «Аллахом»

2 Летопись 19:1-11

1Когда Иосафат, царь Иудеи, благополучно вернулся в свой дворец в Иерусалиме, 2провидец Иеву, сын Ханани, вышел ему навстречу и сказал царю:

– Разве следовало тебе помогать нечестивцу и любить тех, кто ненавидит Вечного? За это на тебе гнев Вечного. 3Есть, однако, в тебе и доброе, потому что ты очистил землю от столбов Ашеры и отдал сердце тому, чтобы искать Аллаха.

Иосафат обновляет судебный порядок

4Иосафат жил в Иерусалиме. Он опять начал путешествовать среди народа от Беэр-Шевы до нагорий Ефраима и обращать их к Вечному, Богу их предков. 5Он назначил судей в стране, в каждом из укреплённых городов Иудеи. 6Он сказал судьям:

– Внимательно смотрите за тем, что вы делаете, потому что вы судите не от имени людей, но от имени Вечного, Который будет с вами всякий раз, как вы выносите приговор. 7Итак, пусть будет у вас страх перед Вечным. Судите осмотрительно, потому что у Вечного, нашего Бога, нет ни несправедливости, ни пристрастия, ни подкупа.

8И в Иерусалиме Иосафат тоже назначил некоторых из левитов, священнослужителей и глав исраильских семейств творить суд Вечного и решать тяжбы между горожанами. 9Он повелел им:

– Вы должны служить верно и от всего сердца, в страхе перед Вечным. 10Во всяком деле, какое поступит к вам от ваших соплеменников, живущих в своих городах, – будь то кровопролитие или вопросы Закона, повелений, установлений и правил – вы должны предостерегать их не грешить против Вечного, иначе Его гнев падёт на вас и на ваших сородичей. Поступайте так, и вы не согрешите. 11Главный священнослужитель Амария будет у вас главным во всяком деле, которое касается Вечного, а Зевадия, сын Исмаила, правитель дома Иуды, будет у вас главным во всяком деле, которое касается царя, левиты же будут у вас сановниками. Действуйте смело, и пусть Вечный будет с теми, кто творит добро.