2 Mbiri 15 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Mbiri 15:1-19

Asa Akonza Chipembedzo

1Mzimu wa Mulungu unabwera pa Azariya mwana wa Odedi. 2Iye anapita kukakumana ndi Asa ndipo anati kwa iye, “Tandimverani, inu Asa ndi Ayuda onse ndi Benjamini. Yehova ali ndi inu, inunso mukakhala naye. Ngati inu mumufunafuna Iye mudzamupeza, koma ngati mumusiya, Iye adzakusiyani. 3Kwa nthawi yayitali Israeli anali wopanda Mulungu weniweni, wopanda wansembe wophunzitsa ndi wopanda malamulo. 4Koma pamene anali pa mavuto anatembenukira kwa Yehova, Mulungu wa Israeli ndi kufunafuna Iye, ndipo anamupeza. 5Masiku amenewo sikunali kwabwino kuyenda ulendo, pakuti anthu onse okhala mʼdziko anali pa mavuto aakulu. 6Mtundu umodzi umakanthidwa ndi mtundu wina ndipo mzinda wina umakanthidwa ndi mzinda wina, pakuti Mulungu amawasautsa ndi mazunzo a mtundu uliwonse. 7Koma inu, khalani amphamvu ndipo musataye mtima, pakuti mudzalandira mphotho ya ntchito yanu.”

8Asa atamva mawu awa ndiponso uneneri wa Azariya mwana wa Odedi, analimba mtima. Iye anachotsa mafano onse onyansa mʼdziko lonse la Yuda ndi Benjamini ndi mʼmizinda yonse imene analanda a ku mapiri a Efereimu. Iye anakonzetsa guwa lansembe la Yehova limene linali kutsogolo kwa khonde la Nyumba ya Mulungu.

9Kenaka anasonkhanitsa anthu onse a ku Yuda ndi Benjamini ndiponso anthu ochokera ku Efereimu, Manase ndi Simeoni amene ankakhala pakati pawo, pakuti gulu lalikulu linabwera kwa iye kuchokera ku Israeli litaona kuti anali ndi Yehova Mulungu wake.

10Iwo anasonkhana mu Yerusalemu mwezi wachitatu wa chaka cha 15 cha ulamuliro wa Asa. 11Pa nthawi imeneyi anapereka nsembe kwa Yehova, ngʼombe 700 ndiponso nkhosa ndi mbuzi 7,000 zochokera pa zolanda ku nkhondo zimene anabweretsa. 12Iwo anachita pangano loti azifunafuna Yehova, Mulungu wa makolo awo, ndi mtima ndi moyo wawo wonse. 13Aliyense wosafunafuna Yehova Mulungu wa Israeli aziphedwa, kaya ndi wamngʼono kapena wamkulu, mwamuna kapena mkazi. 14Iwo analumbira kwa Yehova, mokweza mawu, akuyimba malipenga ndi mbetete. 15Anthu onse a ku Yuda anakondwera pa kulumbirako chifukwa analumbira ndi mtima wawo wonse. Iwo anafunafuna Mulungu mwachidwi, ndipo anamupeza Iye. Kotero Yehova anawapatsa mpumulo mbali zonse.

16Mfumu Asa anachotsanso Maaka agogo ake pa udindo wa amayi a mfumu chifukwa anapanga fano lonyansa la Asera. Asa anagwetsa fanolo, naliswa ndipo kenaka anakaliwotcha ku chigwa cha Kidroni. 17Ngakhale kuti sanachotse malo opembedzerako mafano mu Israeli, mtima wa Asa unali wodzipereka kwathunthu kwa Yehova, masiku onse a moyo wake. 18Iye anabweretsanso mʼNyumba ya Mulungu zipangizo zasiliva, golide ndi ziwiya zina zimene iyeyo ndi abambo ake anazipatula.

19Panalibenso nkhondo mpaka chaka cha 35 cha ufumu wa Asa.