2 Mbiri 13 – CCL & KJV

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Mbiri 13:1-22

Abiya Mfumu ya Yuda

1Mʼchaka cha 18 cha ulamuliro wa Yeroboamu, Abiya analowa ufumu wa Yuda, 2ndipo analamulira mu Yerusalemu kwa zaka zitatu. Dzina la amayi ake linali Maaka mwana wa Urieli wa ku Gibeya.

Koma panali nkhondo pakati pa Abiya ndi Yeroboamu. 3Abiya anapita ku nkhondo ndi asilikali odziwa bwino nkhondo 400,000, ndipo Yeroboamu anandandalitsa ankhondo, asilikali 800,000 odziwa bwino nkhondo, osankhidwa ndi amphamvu, woti amenyane naye.

4Abiya anayima pa phiri la Zemaraimu, mʼdziko lamapiri la Efereimu, ndipo anati, “Yeroboamu ndi Aisraeli onse, tandimverani! 5Kodi inu simukudziwa kuti Yehova, Mulungu wa Israeli, wapereka ufumu wa Israeli kwa Davide ndi zidzukulu zake mpaka muyaya ndiponso pangano la mchere? 6Komabe Yeroboamu mwana wa Nebati, mtumiki wa Solomoni mwana wa Davide, anawukira mbuye wake. 7Ndipo anthu ena achabechabe anasonkhana kwa iye ndipo anatsutsana ndi Rehobowamu mwana wa Solomoni pamene anali wamngʼono ndi wosalimba mtima ndi wopanda mphamvu kuti athe kulimbana nawo.

8“Ndipo tsopano inu mwakonzekera kutsutsana ndi ufumu wa Yehova, umene uli mʼmanja mwa zidzukulu za Davide. Inu ndithu mulipo ankhondo ambirimbiri ndipo muli ndi ana angʼombe agolide amene Yeroboamu anapanga kuti akhale milungu yanu. 9Koma kodi inu simunathamangitse ansembe a Yehova, ana a Aaroni ndiponso Alevi ndi kudzisankhira ansembe anuanu monga anthu ena amachitira? Aliyense amene amabwera kuti adzipatule atatenga mwana wangʼombe wamwamuna ndi nkhosa zazimuna zisanu ndi ziwiri amakhala wansembe wa zinthu zimene sizili milungu.

10“Koma kunena za ife, Yehova ndiye Mulungu wathu, ndipo sitinamusiye. Ansembe amene amatumikira Yehova ndi ana a Aaroni ndipo amathandizidwa ndi Alevi. 11Mmawa uliwonse ndi madzulo aliwonse amapereka nsembe zopsereza ndi kufukiza lubani kwa Yehova. Iwo amayika buledi pa tebulo loyeretsedwa monga mwa mwambo ndipo amayatsa nyale pa zoyikapo nyale zagolide madzulo aliwonse. Ife timachita zofuna za Yehova Mulungu wathu. Koma inu mwamusiya. 12Mulungu ali nafe pakuti ndiye mtsogoleri wathu. Ansembe ake atanyamula malipenga, adzayimba mfuwu wankhondo kulimbana nanu. Inu Aisraeli musalimbane ndi Yehova, Mulungu wa makolo anu, pakuti simungathe kupambana.”

13Tsono Yeroboamu anali atatumiza asilikali kumbuyo mowazungulira, kotero kuti iye ali kutsogolo kwa anthu a ku Yuda, anthu owabisalira anali kumbuyo kwawo. 14Asilikali a Yuda anatembenuka ndipo anaona kuti nkhondo imachitikira kutsogolo ndi kumbuyo. Ndipo iwo anafuwulira Yehova. Ansembe anayimba malipenga awo 15ndipo asilikali a Yuda anafuwula mawu ankhondo. Atafuwula mawu ankhondowo, Mulungu anagonjetsa Yeroboamu pamodzi ndi Aisraeli onse pamaso pa Abiya ndi Yuda. 16Aisraeli anathawa Ayuda. Ndipo Mulungu anawapereka mʼmanja mwawo. 17Abiya pamodzi ndi anthu ake anapha anthu ambiri, kotero kuti Aisraeli 500,000 odziwa bwino nkhondo anaphedwa. 18Ankhondo a Israeli anagonjetsedwa pa nthawi imeneyi, ndipo ankhondo a Yuda anapambana chifukwa anadalira Yehova, Mulungu wa makolo awo.

19Abiya anathamangitsa Yeroboamu ndipo anamulanda mizinda ya Beteli, Yesana, ndi Efroni pamodzi ndi midzi yawo yozungulira. 20Yeroboamu sanapezenso mphamvu nthawi ya Abiya. Ndipo Yehova anamukantha nafa.

21Koma Abiya mphamvu zake zinakula. Iye anakwatira akazi 14 ndipo anali ndi ana aamuna 22 ndi ana aakazi 16.

22Zina ndi zina zokhudza Abiya, zimene anachita ndi zimene anayankhula, zinalembedwa mʼbuku la mbiri ya mneneri Ido.

King James Version

2 Chronicles 13:1-22

1Now in the eighteenth year of king Jeroboam began Abijah to reign over Judah. 2He reigned three years in Jerusalem. His mother’s name also was Michaiah the daughter of Uriel of Gibeah. And there was war between Abijah and Jeroboam. 3And Abijah set the battle in array with an army of valiant men of war, even four hundred thousand chosen men: Jeroboam also set the battle in array against him with eight hundred thousand chosen men, being mighty men of valour.13.3 Abijah set: Heb. Abijah bound together

4¶ And Abijah stood up upon mount Zemaraim, which is in mount Ephraim, and said, Hear me, thou Jeroboam, and all Israel; 5Ought ye not to know that the LORD God of Israel gave the kingdom over Israel to David for ever, even to him and to his sons by a covenant of salt? 6Yet Jeroboam the son of Nebat, the servant of Solomon the son of David, is risen up, and hath rebelled against his lord. 7And there are gathered unto him vain men, the children of Belial, and have strengthened themselves against Rehoboam the son of Solomon, when Rehoboam was young and tenderhearted, and could not withstand them. 8And now ye think to withstand the kingdom of the LORD in the hand of the sons of David; and ye be a great multitude, and there are with you golden calves, which Jeroboam made you for gods. 9Have ye not cast out the priests of the LORD, the sons of Aaron, and the Levites, and have made you priests after the manner of the nations of other lands? so that whosoever cometh to consecrate himself with a young bullock and seven rams, the same may be a priest of them that are no gods.13.9 to consecrate…: Heb. to fill his hand 10But as for us, the LORD is our God, and we have not forsaken him; and the priests, which minister unto the LORD, are the sons of Aaron, and the Levites wait upon their business: 11And they burn unto the LORD every morning and every evening burnt sacrifices and sweet incense: the shewbread also set they in order upon the pure table; and the candlestick of gold with the lamps thereof, to burn every evening: for we keep the charge of the LORD our God; but ye have forsaken him. 12And, behold, God himself is with us for our captain, and his priests with sounding trumpets to cry alarm against you. O children of Israel, fight ye not against the LORD God of your fathers; for ye shall not prosper.

13¶ But Jeroboam caused an ambushment to come about behind them: so they were before Judah, and the ambushment was behind them. 14And when Judah looked back, behold, the battle was before and behind: and they cried unto the LORD, and the priests sounded with the trumpets. 15Then the men of Judah gave a shout: and as the men of Judah shouted, it came to pass, that God smote Jeroboam and all Israel before Abijah and Judah. 16And the children of Israel fled before Judah: and God delivered them into their hand. 17And Abijah and his people slew them with a great slaughter: so there fell down slain of Israel five hundred thousand chosen men. 18Thus the children of Israel were brought under at that time, and the children of Judah prevailed, because they relied upon the LORD God of their fathers. 19And Abijah pursued after Jeroboam, and took cities from him, Beth-el with the towns thereof, and Jeshanah with the towns thereof, and Ephrain with the towns thereof. 20Neither did Jeroboam recover strength again in the days of Abijah: and the LORD struck him, and he died.

21¶ But Abijah waxed mighty, and married fourteen wives, and begat twenty and two sons, and sixteen daughters. 22And the rest of the acts of Abijah, and his ways, and his sayings, are written in the story of the prophet Iddo.