Yehu Adzozedwa Ufumu wa ku Israeli
1Mneneri Elisa anayitanitsa mmodzi mwa ana a aneneri, namuwuza kuti, “Manga lamba mʼchiwuno mwako, tenga botolo la mafuta mʼdzanja lako ndipo upite ku Ramoti Giliyadi. 2Ukakafika kumeneko, ukafunefune Yehu mwana wa Yehosafati, mwana wa Nimisi. Ukapite kwa iye, ukamuchotse pakati pa anzake ndi kukamulowetsa mʼchipinda chamʼkati. 3Ndipo ukatenge botololi ndi kuthira mafuta pa mutu wake ndipo ukanene kuti, ‘Yehova akuti, Ine ndikudzoza iwe kukhala mfumu ya Israeli.’ Kenaka ukatsekule chitseko ndi kuthawa ndipo usakachedwe!”
4Choncho mneneri wachinyamatayo anapita ku Ramoti Giliyadi. 5Atafika ku Giliyadiko anapeza atsogoleri a ankhondo ali pa msonkhano. Iye anati, “Mtsogoleri, ine ndili ndi uthenga wanu.”
Ndipo Yehu anafunsa kuti, “Uthengawo ndi wa yani pakati pathu?”
Mneneriyo anayankha kuti, “Ndi wa inuyo, mtsogoleri.”
6Yehu anayimirira nakalowa mʼnyumba. Pamenepo mneneriyo anakhuthulira mafuta pamutu pa Yehu ndipo ananena kuti, “Yehova Mulungu wa Israeli akuti, ‘Ine ndikukudzoza kukhala mfumu ya Israeli, anthu a Yehova. 7Uyenera kuwononga nyumba ya mbuye wako Ahabu ndipo ndidzabwezera imfa ya atumiki anga, aneneri ndiponso imfa ya atumiki ena onse a Yehova amene anaphedwa ndi Yezebeli. 8Banja lonse la Ahabu lidzatheratu. Ndidzachotsa munthu aliyense wamwamuna wa banja la Ahabu kaya ndi kapolo kapena mfulu. 9Ndidzachititsa kuti banja la Ahabu lifanane ndi banja la Yeroboamu mwana wa Nebati ndiponso ngati banja la Baasa mwana wa Ahiya. 10Kunena za Yezebeli, agalu adzamudya ku dera la Yezireeli ndipo palibe amene adzamuyike mʼmanda.’ ” Kenaka mneneriyo anatsekula chitseko nʼkuthawa.
11Yehu atatuluka kupita kumene kunali atsogoleri anzake, mmodzi mwa iwo anamufunsa kuti, “Kodi zonse zili bwino? Kodi munthu wamisala uja anabwera kudzatani kwa iwe?”
Yehu anayankha kuti, “Iwe ukumudziwa munthu uja ndiponso ukudziwa zomwe amayankhula.”
12Atsogoleri aja anati, “Ukunama! Tiwuze.”
Yehu anati, “Zimene wandiwuza ndi izi: ‘Yehova akuti: Ine ndakudzoza iwe kukhala mfumu ya Israeli.’ ”
13Atsogoleri aja mofulumira anatenga zofunda zawo naziyala pansi pa makwerero kuti Yehu akhalepo. Kenaka analiza lipenga, nafuwula kuti, “Yehu ndiye mfumu!”
Yehu Apha Yoramu ndi Ahaziya
14Choncho Yehu mwana wa Yehosafati, mwana wa Nimisi, anachitira chiwembu Yoramu. (Nthawi imeneyi nʼkuti Yoramu ndi Aisraeli onse akuteteza Ramoti Giliyadi kwa Hazaeli mfumu ya ku Aramu, 15koma nʼkuti Yoramu atabwerera ku Yezireeli kuti akachire mabala amene Aaramu anamuvulaza pa nkhondo ndi Hazaeli mfumu ya ku Aramu.) Yehu anati, “Ngati mukugwirizana nazo zimenezi, wina aliyense asatuluke mu mzinda muno kupita kukafotokoza nkhaniyi ku Yezireeli.” 16Pamenepo Yehu anakwera galeta lake, napita ku Yezireeli, chifukwa Yoramu anali akupumula kumeneko ndipo Ahaziya, mfumu ya ku Yuda, nʼkuti ali komweko kudzamuona.
17Mlonda amene ankayimirira pa nsanja yolondera mzinda wa Yezireeli ataona gulu lankhondo la Yehu likuyandikira, anafuwula kuti, “Ndikuona gulu lankhondo likubwera.”
Yoramu analamula kuti, “Peza munthu wokwera kavalo, mutume kuti akakumane nawo ndi kuwafunsa kuti, ‘Kodi mukubwera mwamtendere?’ ”
18Choncho munthu wokwera kavalo anapita kukakumana ndi Yehu ndipo anati, “Mfumu ikufunsa kuti, ‘Kodi mukubwera mwamtendere?’ ”
Yehu anayankha kuti, “Kodi iwe nkhani ya mtendere yakukhudza bwanji? Tiye, zinditsata pambuyo panga.”
Mlonda uja anakafotokoza kwa mfumu kuti, “Wamthenga uja wakafika kwa anthuwo koma sakubwerera.”
19Choncho mfumu inatumanso munthu wina wachiwiri wokwera kavalo. Atafika kwa anthuwo iye anati, “Mfumu ikufunsa kuti, ‘Kodi mukubwera mwamtendere?’ ”
Yehu anayankha kuti, “Kodi iwe nkhani ya mtendere yakukhudza bwanji? Tiye, zinditsata pambuyo panga.”
20Mlonda uja anakanenanso kuti, “Wamthenga uja wakafika kwa anthuwo koma sakubwereranso. Kuyendako kukukhala ngati kwa Yehu mwana wa Nimisi, iye amayenda ngati munthu wamisala.”
21Yoramu analamula kuti, “Konzani galeta langa.” Ndipo atakonza galeta lake, Yoramu mfumu ya Israeli ndi Ahaziya mfumu ya ku Yuda anakwera nʼkutuluka mu mzindamo, aliyense atakwera galeta lake, kukakumana ndi Yehu. Iwo anakumana ndi Yehu pa munda umene unali wa Naboti, wa ku Yezireeli. 22Yoramu ataona Yehu anafunsa kuti, “Yehu, kodi wabwera mwamtendere?”
Yehu anayankha kuti, “Pangakhale bwanji mtendere pamene zopembedza mafano zonse zilipo ndiponso ufiti wa amayi ako Yezebeli uli ponseponse?”
23Yoramu anatembenuka, nathawa akufuwula kwa Ahaziya kuti, “Ahaziya, anthuwa atiwukira!”
24Pamenepo Yehu anakoka uta wake ndipo analasa Yoramu kumsana pakati pa mapewa. Muviwo unakalasa mtima wake ndipo anagwa pansi mʼgaleta lakelo. 25Yehu anawuza Bidikara, mtsogoleri wa galeta lake kuti, “Munyamule ndipo ukamuponye mʼmunda umene unali wa Naboti wa ku Yezireeli, chifukwa kumbukira mmene iwe ndi ine tinkayenda pambuyo pa Ahabu abambo ake, kuti Yehova ananeneratu za iye kuti, 26‘Zoonadi dzulo ndinaona magazi a Naboti ndi magazi a ana ake, akutero Yehova, ndipo Ine ndidzakubwezera ndithu choyipa chimenechi pa munda womwe uno, akutero Yehova.’ Tsono munyamule ndipo ukamuponye mʼmundamo, potsatira zimene Yehova ananena.”
27Ahaziya mfumu ya ku Yuda ataona zimene zinachitika, anathawira ku Beti Hagani. Yehu anamuthamangitsa, uku akufuwula kuti, “Mupheninso!” Iwo anamuvulaza ali mʼgaleta lakelo pa njira yopita ku Guri pafupi ndi Ibuleamu, koma iye anathawira ku Megido ndipo anakafera kumeneko. 28Antchito ake anamunyamulira mʼgaleta kupita naye ku Yerusalemu ndipo anamuyika mʼmanda pamodzi ndi makolo ake mu mzinda wa Davide. 29(Mʼchaka cha khumi ndi chimodzi cha ufumu wa Yoramu mwana wa Ahabu, Ahaziya anakhala mfumu ya ku Yuda).
Kuphedwa kwa Yezebeli
30Kenaka Yehu anapita ku Yezireeli. Yezebeli atamva zimene zinachitika, anapaka zodzikometsera mʼmaso, naluka tsitsi lake, namasuzumira pa zenera. 31Pamene Yehu ankalowa pa chipata iye anafunsa kuti, “Kodi wabwera mwamtendere, iwe Zimuri, munthu wopha mbuye wako?”
32Yehu anakweza maso nayangʼana pa zenera, ndipo anafuwula kuti, “Kodi ndani ali mbali yanga? Ndani?” Anthu ofulidwa awiri kapena atatu anayangʼana Yehu pansipo. 33Yehu anawawuza kuti, “Muponyeni pansi!” Motero anamuponya pansi ndipo magazi ake ena anafalikira pa khoma ndi pa akavalo pamene ankamupondaponda.
34Yehu analowa mʼnyumba yaufumu ndipo anadya ndi kumwa. Kenaka iye anati, “Kamutoleni mkazi wotembereredwayo, ndipo kamuyikeni mʼmanda, popeza ndi mwana wa mfumu.” 35Koma atapita kuti akamuyike mʼmanda, sanapeze kanthu kupatula chibade cha mutu wokha, mapazi ake ndi manja ake. 36Choncho iwo anabwerera kwa Yehu ndi kukamufotokozera kuti, “Mawu amene Yehova anayankhula kudzera mwa mtumiki wake Eliya wa ku Tisibe ndi awa: Pa munda wa ku Yezireeli agalu adzadya mtembo wa Yezebeli. 37Mtembo wa Yezebeli udzakhala ngati zinyalala pa munda wa ku Yezireeli, kotero kuti palibe amene adzathe kunena kuti, ‘Uyu ndi Yezebeli.’ ”
Помазание Иеву на царство в Исроиле
1Пророк Елисей призвал одного из учеников пророческих и сказал ему:
– Поторопись, возьми этот сосуд с маслом и ступай в Рамот Галаадский. 2Когда придёшь туда, разыщи там Иеву, сына Иосафата, внука Нимши. Пойди к нему и уведи его от его друзей во внутреннюю комнату. 3Возьми этот сосуд, полей масло ему на голову и произнеси: «Так говорит Вечный: „Я помазываю9:3 Посредством обряда помазания человек посвящался на определённое служение. Такого помазания удостаивались пророки, цари и священнослужители. тебя в цари Исроила“». Потом открой дверь и беги, не задерживайся!
4И молодой ученик пошёл в Рамот Галаадский. 5Когда он пришёл туда, он увидел военачальников, сидящих вместе.
– У меня есть весть для тебя, военачальник, – сказал он.
– Для кого из нас? – спросил Иеву.
– Для тебя, военачальник, – ответил он.
6Иеву встал и прошёл в дом. И пророк возлил масло на голову Иеву и произнёс:
– Так говорит Вечный, Бог Исроила: «Я помазываю тебя в цари Исроила, народа Вечного. 7Истреби дом Ахава, твоего господина, чтобы Мне отомстить за кровь Моих рабов пророков и за кровь всех рабов Вечного, пролитую Иезевелью. 8Погибнет весь дом Ахава. Я истреблю у Ахава всякого человека мужского пола – и раба, и свободного. 9Я уподоблю дом Ахава дому Иеровоама, сына Невата, и дому Бааши, сына Ахии9:9 См. 3 Цар. 14:10-11; 16:3-4.. 10А Иезевель сожрут псы на участке земли в Изрееле, и никто её не похоронит».
После этого он открыл дверь и убежал. 11Когда Иеву вышел к друзьям, один из них спросил его:
– Всё ли благополучно? Зачем к тебе приходил этот сумасшедший?
– Вы сами знаете, что это за человек и что он может сказать, – ответил Иеву.
12– Неправда! – сказали они. – Расскажи нам.
Иеву сказал:
– Он сказал мне: «Так говорит Вечный: „Я помазываю тебя в цари Исроила“».
13Они заторопились, взяли плащи и постелили их ему прямо на ступеньках. Потом они затрубили в рог и закричали:
– Воцарился Иеву!
Гибель царей Иорама и Охозии
(2 Лет. 22:7-9)
14Иеву, сын Иосафата, внук Нимши, составил заговор против Иорама. (Иорам и весь Исроил защищали Рамот Галаадский от Хазаила, царя Сирии, 15но царь Иорам вернулся в Изреель, чтобы оправиться от ран, которые сирийцы нанесли ему в битве с царём Сирии Хазаилом.) Иеву сказал:
– Если вы согласны, то не давайте никому выйти из города и рассказать новости в Изрееле.
16Он взошёл на колесницу и поехал в Изреель, потому что там отдыхал Иорам, а Охозия, царь Иудеи, пришёл его навестить. 17Когда часовой, стоявший на башне в Изрееле, увидел, как приближаются воины Иеву, он закричал:
– Я вижу воинов!
– Отправь им навстречу всадника, – приказал Иорам. – Пусть спросит: «С миром ли вы?»
18Всадник выехал навстречу Иеву и сказал:
– Царь спрашивает, с миром ли вы?
– Что тебе до мира? – ответил Иеву. – Поезжай за мной.
И часовой доложил:
– Посланец доехал до них, но назад не возвращается.
19Тогда царь послал второго всадника. Подъехав к ним, он сказал:
– Царь спрашивает, с миром ли вы?
Иеву ответил:
– Что тебе до мира? Поезжай за мной.
20И часовой доложил:
– Посланец доехал до них, но и он не возвращается назад. А человек, скачущий впереди, похож на Иеву, сына Нимши, – он скачет, как безумец.
21– Запрягай мою колесницу, – приказал Иорам.
И когда её запрягли, Иорам, царь Исроила, и Охозия, царь Иудеи, выехали в своих колесницах навстречу Иеву. Они встретили его у участка земли, который принадлежал Навоту из Изрееля.
22Увидев Иеву, Иорам спросил:
– Ты с миром, Иеву?
– Какой мир, – ответил Иеву, – пока множатся идолопоклонство и чародейство твоей матери Иезевели?
23Иорам повернул назад и обратился в бегство, крича Охозии:
– Измена, Охозия!
24Иеву натянул лук и поразил Иорама между лопатками. Стрела пронзила ему сердце, и он осел в колеснице. 25А Иеву сказал своему сановнику Бидкару:
– Подними его и брось на поле, что принадлежало Навоту из Изрееля. Помнишь, как мы с тобой ехали в колесницах за его отцом Ахавом, когда Вечный изрёк о нём такое пророчество: 26«Вчера Я видел кровь Навота и кровь его сыновей, – возвещает Вечный, – и непременно взыщу с тебя за неё на этом участке земли». Итак, подними его и брось на тот самый участок, по слову Вечного9:25-26 См. 3 Цар. 21:19, 24, 29..
27Увидев, что случилось, Охозия, царь Иудеи, бежал по дороге к Бет-Гану9:27 Или: «по дороге, которая ведёт к садовому дому».. Иеву гнался за ним, крича:
– Убейте и этого!
Люди ранили Охозию в колеснице на дороге, поднимающейся к Гуру, что близ Ивлеама, но он скрылся в городе Мегиддо, где и умер. 28Слуги отвезли его на колеснице в Иерусалим и похоронили с предками в его гробнице в Городе Довуда. 29(Охозия стал царём Иудеи на одиннадцатом году правления Иорама, сына Ахава.)
Гибель Иезевели
30А Иеву пошёл в Изреель. Когда Иезевель услышала об этом, она подвела глаза, уложила волосы и стала смотреть в окно. 31Когда Иеву вошёл в ворота, она спросила:
– Обрёл ли покой Зимри, убийца своего господина?9:31 Иезевель намекает здесь на судьбу военачальника Зимри, который убил своего царя Елу и истребил весь царский род, но сам погиб через семь дней (см. 3 Цар. 16:9-20).
32Он поднял взгляд к окну и позвал:
– Кто за меня? Кто?
Из окна выглянули два или три евнуха.
33– Сбросьте её вниз! – сказал Иеву.
Они сбросили её, и её кровь брызнула на стену и на коней, которые растоптали её.
34Иеву зашёл, поел и попил. Потом он сказал:
– Разыщите эту проклятую и похороните, она всё-таки царская дочь.
35Но когда пошли её хоронить, то не нашли ничего, кроме черепа, ног и кистей рук 36и, вернувшись, доложили Иеву, который сказал:
– Это слово Вечного, которое Он изрёк через Своего раба Ильёса из Тишбы: «На земле Изрееля псы сожрут тело Иезевели. 37Труп Иезевели будет на участке Изрееля как навоз на поле, так что никто не скажет: „Это Иезевель“»9:33-37 См. ст. 10 и 3 Цар. 21:23..