Mayi wa ku Sunemu Atenganso Munda wake
1Ndipo Elisa anawuza mayi amene anamuukitsira mwana wake kuti, “Choka kuno pamodzi ndi banja lako ndipo ukakhale kulikonse ukufuna, chifukwa Yehova akubweretsa njala ya zaka zisanu ndi ziwiri mʼdziko muno.” 2Mayiyo ananyamuka nachita zimene munthu wa Mulungu ananena. Iye pamodzi ndi banja lake anachoka nakakhala ku dziko la Afilisti zaka zisanu ndi ziwiri.
3Zitatha zaka zisanu ndi ziwirizo anabwera kuchokera ku dziko la Afilisti ndipo anapita kwa mfumu kukafunsa za nyumba yake ndi munda wake. 4Ndipo mfumu inkayankhula ndi Gehazi, mtumiki wa munthu wa Mulungu kuti, “Tandiwuza zinthu zikuluzikulu zimene Elisa wachita.” 5Pamene Gehazi ankayiwuza mfumuyo momwe Elisa anaukitsira anthu akufa, mayi amene mwana wake Elisa anamuukitsa kwa akufayo analowa kudzafunsa mfumu za nyumba yake ndi munda wake.
Gehazi anati, “Mbuye wanga mfumu, mayi wake ndi uyu ndipo mwana wakeyo ndi uyu amene Elisa anamuukitsa kwa akufa.” 6Mfumu inafunsa mayiyo za nkhaniyi ndipo iye anayifotokozera mfumuyo.
Ndipo mfumu inasankha munthu woti ayendetse nkhani yake ndipo inati, “Mubwezereni zonse zimene zinali zake, kuphatikizapo phindu lonse lochokera mʼmunda wake, kuyambira tsiku limene anachoka mpaka tsopano lino.”
Hazaeli Apha Beni-Hadadi
7Elisa anapita ku Damasiko, ndipo Beni-Hadadi mfumu ya ku Aramu ankadwala. Mfumuyo itawuzidwa kuti, “Munthu wa Mulungu wabwera kuno kuchokera kutali,” 8inawuza Hazaeli kuti, “Tenga mphatso ndipo pita ukakumane ndi munthu wa Mulungu. Ukandifunsire kwa Yehova kudzera mwa iye kuti, ‘Kodi ndidzachira matenda angawa?’ ”
9Choncho Hazaeli anapita kukakumana ndi Elisa, atasenzetsa ngamira 40 mphatso za zinthu zosiyanasiyana zabwino kwambiri za ku Damasiko. Iye analowa mʼnyumba ya Elisa ndi kuyima pamaso pake, ndipo anati, “Mwana wanu Beni-Hadadi wandituma kuti ndidzakufunseni kuti, ‘Kodi ndidzachira matenda angawa?’ ”
10Elisa anayankha kuti, “Pita ndipo ukamuwuze kuti, ‘Udzachira ndithu,’ koma Yehova wandionetsa kuti adzafabe.” 11Elisa anamuyangʼana kwambiri Hazaeli mpaka anachita manyazi. Pamenepo munthu wa Mulungu anayamba kulira.
12Hazaeli anafunsa kuti, “Mbuye wanga mukulira chifukwa chiyani?”
Elisa anayankha kuti, “Chifukwa ndikudziwa choyipa chimene udzachitira Aisraeli. Udzatentha mizinda yawo ya chitetezo, udzapha anyamata awo ndi lupanga, udzaphwanyitsa pansi makanda awo ndiponso udzatumbula mimba za akazi awo oyembekezera.”
13Ndipo Hazaeli anati, “Kodi kapolo wanune, amene ndine wonyozeka ngati galu, ndingathe bwanji kuchita chinthu chachikulu chotere?”
Elisa anayankha kuti, “Yehova wandionetsa kuti iwe udzakhala mfumu ya ku Aramu.”
14Choncho Hazaeli anasiyana ndi Elisa ndi kubwerera kwa mbuye wake. Beni-Hadadi atafunsa kuti, “Elisa wakuwuza chiyani?” Hazaeli anayankha kuti, “Elisa wandiwuza kuti inu mudzachira ndithu.” 15Koma mmawa mwake Hazaeli anatenga nsalu yokhuthala ndi kuyiviyika mʼmadzi ndipo anaphimba nayo nkhope ya mfumu, kotero mfumuyo inafa. Hazaeli analowa ufumu mʼmalo mwake.
Yehoramu Mfumu ya ku Yuda
16Chaka chachisanu cha ufumu wa Yoramu mwana wa Ahabu mfumu ya ku Israeli, Yehosafati ali mfumu ya ku Yuda, Yehoramu mwana wake anakhala mfumu ya Ayuda. 17Yehoramu analowa ufumu ali ndi zaka 32, ndipo analamulira mu Yerusalemu zaka zisanu ndi zitatu. 18Iye anatsatira khalidwe la mafumu a ku Israeli, monga mmene linachitira banja la Ahabu, popeza iye anakwatira mwana wa Ahabu. Yehoramu anachita zoyipa pamaso pa Yehova. 19Komabe, chifukwa cha mtumiki wake Davide, Yehova sanafune kuwononga Yuda popeza Yehova analonjeza Davide kuti adzamupatsa nyale pamodzi ndi zidzukulu zake mpaka muyaya.
20Pa nthawi ya Yehoramu, Edomu anawukira ulamuliro wa Yuda ndipo anadzisankhira mfumu. 21Choncho Yehoramu anapita ku Zairi pamodzi ndi magaleta ake onse. Ndipo iye anakantha Aedomu amene anamuzungulira pamodzi ndi oyendetsa magaleta ake usiku. Koma ankhondo ake anathawa napita ku misasa yawo. 22Mpaka lero lino Edomu ndi wowukira Yuda. Nthawi yomweyo mzinda wa Libina unawukiranso.
23Ndipo ntchito zina za Yehoramu ndi zonse zomwe anachita, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri ya mafumu a Yuda? 24Choncho Yehoramu anamwalira ndipo anayikidwa mʼmanda pamodzi ndi makolo ake mu Mzinda wa Davide. Ndipo Ahaziya mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake.
Ahaziya Mfumu ya ku Yuda
25Mʼchaka cha khumi ndi chiwiri cha Yoramu mwana wa Ahabu mfumu ya Israeli, Ahaziya mwana wa Yehoramu mfumu ya Yuda anayamba kulamulira. 26Ahaziya anali ndi zaka 22 pamene anakhala mfumu ndipo analamulira mu Yerusalemu chaka chimodzi. Amayi ake anali Ataliya, chidzukulu cha Omiri mfumu ya Israeli. 27Iye anatsatira makhalidwe a banja la Ahabu ndipo anachita zoyipa pamaso pa Yehova, monga linachitira banja la Ahabu, pakuti anali mkamwini wa banja la Ahabu.
28Ahaziya anapita pamodzi ndi Yoramu mwana wa Ahabu kukachita nkhondo ndi Hazaeli mfumu ya Aramu ku Ramoti Giliyadi. Aaramu anavulaza Yoramu. 29Choncho mfumu Yoramu inabwerera ku Yezireeli kuti ikachire mabala ake amene Aaramu anamuvulaza ku Rama pa nkhondo yake ndi Hazaeli mfumu ya Aramu.
Tsono Ahaziya mwana wa Yehoramu mfumu ya ku Yuda anapita ku Yezireeli kuti akamuone Yoramu mwana wa Ahabu, popeza nʼkuti akudwala.
Возвращение земли шунемитянки
1Елисей сказал женщине, сына которой он воскресил:
– Уходи с семьёй и поселись, где сможешь, потому что Вечный навёл на страну голод, который будет длиться семь лет.
2Женщина собралась и сделала, как сказал пророк. Вместе с семьёй она ушла и семь лет жила в земле филистимлян. 3Через семь лет она вернулась из земли филистимлян и пошла к царю просить о своём доме и о земле. 4А царь в то время беседовал с Гехази, слугой пророка, и сказал:
– Расскажи мне о великих делах, которые совершил Елисей.
5Как раз, когда Гехази рассказывал царю о том, как Елисей воскресил мёртвого, женщина, чьего сына Елисей воскресил, пришла просить царя о своём доме и о земле. Гехази сказал:
– Вот это и есть та женщина, господин мой царь, а это её сын, которого воскресил Елисей.
6Царь расспросил женщину, и она рассказала ему всё. Тогда он поручил чиновнику рассмотреть её дело, сказав ему:
– Верни ей всё, что у неё было, а также все доходы от её земли, что были получены с того дня, как она покинула страну, до этого дня.
Предсказание Елисея об убийстве Бен-Адада
7Елисей пришёл в Дамаск, когда Бен-Адад, царь Сирии, был болен. Когда царю доложили, что пришёл пророк, 8он сказал Хазаилу:
– Возьми с собой подарок и иди встречать пророка. Спроси через него Вечного, выздоровею ли я от этой болезни.
9Хазаил пошёл встречать Елисея, взяв с собой в дар лучших товаров Дамаска на сорок верблюжьих поклаж. Он пришёл, встал перед ним и сказал:
– Твой сын Бен-Адад, царь Сирии, послал меня спросить: «Выздоровею ли я от этой болезни?»
10Елисей сказал:
– Иди и скажи ему: «Ты обязательно выздоровеешь», но Вечный открыл мне, что на самом деле он умрёт.
11Елисей смотрел на Хазаила не отрываясь, пока Хазаил не смутился. Тогда пророк заплакал.
12– Почему мой господин плачет? – спросил Хазаил.
– Потому что я знаю, какое зло ты причинишь исраильтянам, – ответил он. – Ты сожжёшь их крепости, юношей их убьёшь мечом, разобьёшь их младенцев о землю и порубишь их беременных женщин.
13Хазаил сказал:
– Как твой раб, который лишь пёс, сможет совершить такое дело?
– Вечный открыл мне, что ты станешь царём Сирии, – ответил Елисей8:13 Здесь Елисей произносит пророчество, которое ранее было открыто Всевышним Ильясу (см. 3 Цар. 19:15-17)..
14Тогда Хазаил ушёл от Елисея и вернулся к своему господину.
Бен-Адад спросил его:
– Что сказал тебе Елисей?
Хазаил ответил:
– Он сказал мне, что ты непременно выздоровеешь.
15Но на другой день он взял одеяло, намочил его водой и накрыл им лицо царя, и тот умер. А Хазаил стал царём вместо него.
Иорам – царь Иудеи
(2 Лет. 21:5-10, 20)
16На пятом году правления исраильского царя Иорама, сына Ахава, когда Иосафат ещё был царём Иудеи, в Иудее начал царствовать Иорам, сын Иосафата. 17Ему было тридцать два года, когда он стал царём, и правил он в Иерусалиме восемь лет. 18Он ходил путями царей Исраила, по примеру дома Ахава, потому что женился на дочери Ахава. Он делал зло в глазах Вечного. 19Но ради Своего раба Давуда Вечный не хотел погубить Иудею. Он обещал сохранить царство8:19 Букв.: «дать светильник». для него и для его потомков навеки.
20Во времена Иорама Эдом восстал против власти Иудеи и поставил себе своего царя. 21Тогда Иорам пошёл в город Цаир со всеми своими колесницами. Эдомитяне окружили его и начальников над его колесницами. Ночью он встал и пробился через кольцо врагов, а его войско бежало домой. 22И до сих пор Эдом не покорён власти Иудеи. Ливна восстала в то же самое время.
23Прочие события царствования Иорама и всё, что он сделал, записано в «Книге летописей царей Иудеи». 24Иорам упокоился со своими предками и был похоронен с ними в Городе Давуда. И царём вместо него стал его сын Охозия.
Охозия – царь Иудеи
(2 Лет. 22:1-6)
25На двенадцатом году правления исраильского царя Иорама, сына Ахава, над Иудеей начал царствовать Охозия, сын Иорама. 26Охозии было двадцать два года, когда он стал царём, и правил он в Иерусалиме один год. Его мать звали Аталия, она была внучкой Омри, царя Исраила. 27И так как Охозия был в родстве с домом Ахава8:27 Аталия, мать Охозии, была дочерью Ахава (см. ст. 18)., то он и ходил их путями и делал зло в глазах Вечного по примеру дома Ахава.
28Охозия ходил с Иорамом, сыном Ахава, воевать против Хазаила, царя Сирии, под Рамот Галаадский. Сирийцы ранили Иорама, 29и тот вернулся в Изреель, чтобы оправиться от ран, нанесённых ему сирийцами при Рамоте в битве с Хазаилом, царём Сирии. Тогда иудейский царь Охозия, сын Иорама, отправился в Изреель навестить Иорама, сына Ахава, потому что тот был ранен.