2 Mafumu 19 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Mafumu 19:1-37

Kupulumutsidwa kwa Yerusalemu

1Mfumu Hezekiya atamva zimenezi, anangʼamba zovala zake navala chiguduli ndipo analowa mʼNyumba ya Yehova. 2Iye anatuma Eliyakimu, woyangʼanira nyumba ya mfumu, Sebina mlembi wa bwalo ndi ansembe akuluakulu, onse atavala ziguduli, kwa mneneri Yesaya mwana wa Amozi. 3Iwo anamuwuza kuti, “Hezekiya akunena kuti, ‘Lero ndi tsiku lamavuto, lachilango ndi lamanyazi. Ife lero tili ngati mayi woyembekezera amene pofika nthawi yoti achire akupezeka kuti alibe mphamvu zoberekera. 4Mwina Yehova Mulungu wanu adzamva mawu onse a Rabusake amene mbuye wake, mfumu ya ku Asiriya anamutuma kudzanyoza Mulungu wamoyo, ndipo Mulunguyo adzamulanga chifukwa cha mawu amene Yehova Mulungu wanu wamva. Choncho pemphererani anthu otsala amene akanali ndi moyo.’ ”

5Akuluakulu a Mfumu Hezekiya atafika kwa Yesaya, 6Yesaya anawawuza kuti, “Kawuzeni mbuye wanu kuti, ‘Yehova akunena kuti: Usachite mantha ndi zimene wamva, mawu amene nthumwi za mfumu ya ku Asiriya zandinyoza nawo Ine. 7Tamverani! Ine ndidzayika mwa mfumuyo mzimu wina kotero kuti akadzamva mphekesera ya nkhondo, adzabwerera ku dziko lake ndipo Ine ndidzachititsa kuti aphedwe ndi lupanga kwawo komweko.’ ”

8Rabusake atamva kuti mfumu ya ku Asiriya yachoka ku Lakisi, iye anabwerera mʼmbuyo ndipo anakapeza mfumu ikuchita nkhondo ndi mzinda wa Libina.

9Nthawi imeneyi Senakeribu analandira uthenga wakuti Tirihaka, mfumu ya ku Kusi, akubwera kudzachita naye nkhondo. Choncho iye anatumanso amithenga kwa Hezekiya ndi mawu awa: 10“Kawuzeni Hezekiya mfumu ya Yuda kuti: Usalole kuti Mulungu amene ukumudalira akupusitse ponena kuti, ‘Yerusalemu sadzaperekedwa mʼmanja mwa mfumu ya ku Asiriya.’ 11Ndithu iwe unamva chimene mafumu a Asiriya anachita ku mayiko ena onse, kuti anawawononga kotheratu. Ndipo kodi iwe nʼkupulumuka? 12Kodi milungu ya mitundu imene makolo anga anayigonjetsa, milungu ya anthu a ku Gozani, Harani, Rezefi ndi Aedeni amene anali ku Teli Asara, inawapulumutsa? 13Kodi mafumu a Hamati, Aripadi ndi mafumu a mizinda ya Sefaravaimu, Hena ndi Iva, ali kuti?”

Pemphero la Hezekiya

14Hezekiya analandira kalata kwa amithenga aja nayiwerenga. Pomwepo anapita ku Nyumba ya Yehova nayika kalatayo pamaso pa Yehova. 15Ndipo Hezekiya anapemphera kwa Yehova nati, “Inu Yehova Mulungu wa Israeli, Inu amene mumakhala pa Akerubi, Inu nokha ndinu Mulungu wolamulira maufumu onse a dziko lapansi. Inu munalenga kumwamba ndi dziko lapansi. 16Inu Yehova, tcherani khutu lanu ndipo mumve Yehova tsekulani maso anu ndipo muone, imvani mawu onse amene Senakeribu watumiza kunyoza Inu Mulungu wamoyo.

17“Inu Yehova, nʼzoonadi kuti mafumu a Asiriya anawononga mitundu iyi ndi mayiko awo. 18Iwo anaponya milungu yawo pa moto ndi kuyiwononga pakuti sinali milungu koma mitengo ndi miyala chabe, yopangidwa ndi anthu. 19Ndipo tsopano Inu Yehova Mulungu wathu, tipulumutseni ndithu mʼdzanja lake, kuti maufumu onse a dziko lapansi adziwe kuti Inu nokha, Inu Yehova, ndinu Mulungu.”

Yankho la Mulungu Kudzera mwa Yesaya

20Ndipo Yesaya mwana wa Amozi anatumiza uthenga kwa Hezekiya wakuti, “Yehova Mulungu wa Israeli akuti, ‘Ndamva pemphero lako lonena za Senakeribu mfumu ya ku Asiriya.’ ” 21Mawu amene Yehova wayankhula wotsutsana naye ndi awa:

“Namwali wa Ziyoni

akukunyoza ndi kukuseka iwe.

Mwana wamkazi wa Yerusalemu

akupukusa mutu wake kumbuyo kwako.

22Kodi iweyo wanyoza ndi kuchitira chipongwe yani?

Kodi ndani amene wamufuwulira mawu ako

ndi kumuyangʼana monyada?

Wachitiratu izi Woyera wa Israeli!

23Kudzera mwa amithenga ako

wonyoza Ambuye.

Ndipo wanena kuti,

‘Ndi magaleta ochuluka

ndinakwera mapiri ataliatali,

pa msonga za mapiri a Lebanoni.

Ndigwetsa mitengo yake ya mkungudza yayitali kwambiri,

mitengo yake ya payini yabwino kwambiri.

Ndalowanso mʼkati mwake mwenimweni,

mwa nkhalango yake yowirira kwambiri.

24Ndakumba zitsime ku mayiko achilendo

ndipo ndinamwa madzi a kumeneko.

Ndi mapazi anga

ndawumitsa mitsinje yonse ya ku Igupto.’ ”

25“ ‘Kodi sunamvepo?

Zimenezi ndinazikhazikitsa kalekale.

Ndinazikonzeratu masiku amakedzana;

tsopano ndachita kuti zichitikedi,

iwe kwako kunali kungosandutsa mizinda yotetezedwa

kukhala milu ya miyala.

26Anthu a kumeneko ndi opanda mphamvu,

athedwa nzeru ndipo ali ndi manyazi.

Ali ngati mbewu za mʼmunda,

ngati udzu wanthete,

ali ngati udzu womera pa denga,

umene umawuma usanakule nʼkomwe.’ ”

27“ ‘Koma Ine ndimadziwa kukhala kwako,

kutuluka kwako ndi kulowa kwako,

ndi mkwiyo wako pa Ine.

28Chifukwa chakuti wandikwiyira

ndipo ndamva za mwano wako,

ndidzakola mphuno yako ndi mbedza

ndi kuyika chitsulo changa mʼkamwa mwako,

ndipo ndidzakubweza pokudzeretsa

njira yomwe unadzera pobwera.’

29“Koma iwe Hezekiya, chizindikiro chako chidzakhala ichi:

“Chaka chino mudzadya tirigu wamphulumukwa,

ndipo chaka chamawa mudzadya tirigu wongodzimerera.

Koma chaka chachitatu mudzadzala ndi kukolola,

mudzawoka mphesa ndipo mudzadya zipatso zake.

30Anthu a nyumba ya Yuda amene adzatsale

adzazika mizu ndi kubereka zipatso.

31Pakuti ku Yerusalemu kudzachokera anthu otsala,

ndi ku phiri la Ziyoni kudzachokera gulu la anthu opulumuka.”

“Changu cha Yehova Wamphamvuzonse chidzachita zimenezi.

32“Choncho chimene Yehova akunena za mfumu ya ku Asiriya ndi ichi:

“ ‘Iye sadzalowa mu mzinda umenewu

kapena kuponyamo muvi.

Sadzayandikira mzindawu ndi zishango zake

kapena kumanga nthumbira ya nkhondo.

33Adzabwerera potsata njira imene anadzera pobwera;

sadzalowa mu mzinda umenewu,

akutero Yehova.

34Ndidzateteza mzinda umenewu kuwupulumutsa,

chifukwa cha Ine mwini ndiponso chifukwa cha Davide mtumiki wanga.’ ”

35Usiku umenewo mngelo wa Yehova anapita ku misasa ya ku Asiriya ndi kupha ankhondo 185,000. Ndipo pamene anthu anadzuka mmawa, taonani, mitembo inali ngundangunda! 36Choncho Senakeribu mfumu ya ku Asiriya anapasula misasa ndi kuchoka. Anabwerera ku Ninive nakakhala kumeneko.

37Tsiku lina, pamene Senakeribu ankapembedza mʼnyumba ya Nisiroki mulungu wake, ana ake Adirameleki ndi Sarezeri anamupha ndi lupanga ndipo anathawira ku dziko la Ararati. Tsono Esrahadoni, mwana wake, analowa ufumu mʼmalo mwake.