Kupulumutsidwa kwa Yerusalemu
1Mfumu Hezekiya atamva zimenezi, anangʼamba zovala zake navala chiguduli ndipo analowa mʼNyumba ya Yehova. 2Iye anatuma Eliyakimu, woyangʼanira nyumba ya mfumu, Sebina mlembi wa bwalo ndi ansembe akuluakulu, onse atavala ziguduli, kwa mneneri Yesaya mwana wa Amozi. 3Iwo anamuwuza kuti, “Hezekiya akunena kuti, ‘Lero ndi tsiku lamavuto, lachilango ndi lamanyazi. Ife lero tili ngati mayi woyembekezera amene pofika nthawi yoti achire akupezeka kuti alibe mphamvu zoberekera. 4Mwina Yehova Mulungu wanu adzamva mawu onse a Rabusake amene mbuye wake, mfumu ya ku Asiriya anamutuma kudzanyoza Mulungu wamoyo, ndipo Mulunguyo adzamulanga chifukwa cha mawu amene Yehova Mulungu wanu wamva. Choncho pemphererani anthu otsala amene akanali ndi moyo.’ ”
5Akuluakulu a Mfumu Hezekiya atafika kwa Yesaya, 6Yesaya anawawuza kuti, “Kawuzeni mbuye wanu kuti, ‘Yehova akunena kuti: Usachite mantha ndi zimene wamva, mawu amene nthumwi za mfumu ya ku Asiriya zandinyoza nawo Ine. 7Tamverani! Ine ndidzayika mwa mfumuyo mzimu wina kotero kuti akadzamva mphekesera ya nkhondo, adzabwerera ku dziko lake ndipo Ine ndidzachititsa kuti aphedwe ndi lupanga kwawo komweko.’ ”
8Rabusake atamva kuti mfumu ya ku Asiriya yachoka ku Lakisi, iye anabwerera mʼmbuyo ndipo anakapeza mfumu ikuchita nkhondo ndi mzinda wa Libina.
9Nthawi imeneyi Senakeribu analandira uthenga wakuti Tirihaka, mfumu ya ku Kusi, akubwera kudzachita naye nkhondo. Choncho iye anatumanso amithenga kwa Hezekiya ndi mawu awa: 10“Kawuzeni Hezekiya mfumu ya Yuda kuti: Usalole kuti Mulungu amene ukumudalira akupusitse ponena kuti, ‘Yerusalemu sadzaperekedwa mʼmanja mwa mfumu ya ku Asiriya.’ 11Ndithu iwe unamva chimene mafumu a Asiriya anachita ku mayiko ena onse, kuti anawawononga kotheratu. Ndipo kodi iwe nʼkupulumuka? 12Kodi milungu ya mitundu imene makolo anga anayigonjetsa, milungu ya anthu a ku Gozani, Harani, Rezefi ndi Aedeni amene anali ku Teli Asara, inawapulumutsa? 13Kodi mafumu a Hamati, Aripadi ndi mafumu a mizinda ya Sefaravaimu, Hena ndi Iva, ali kuti?”
Pemphero la Hezekiya
14Hezekiya analandira kalata kwa amithenga aja nayiwerenga. Pomwepo anapita ku Nyumba ya Yehova nayika kalatayo pamaso pa Yehova. 15Ndipo Hezekiya anapemphera kwa Yehova nati, “Inu Yehova Mulungu wa Israeli, Inu amene mumakhala pa Akerubi, Inu nokha ndinu Mulungu wolamulira maufumu onse a dziko lapansi. Inu munalenga kumwamba ndi dziko lapansi. 16Inu Yehova, tcherani khutu lanu ndipo mumve Yehova tsekulani maso anu ndipo muone, imvani mawu onse amene Senakeribu watumiza kunyoza Inu Mulungu wamoyo.
17“Inu Yehova, nʼzoonadi kuti mafumu a Asiriya anawononga mitundu iyi ndi mayiko awo. 18Iwo anaponya milungu yawo pa moto ndi kuyiwononga pakuti sinali milungu koma mitengo ndi miyala chabe, yopangidwa ndi anthu. 19Ndipo tsopano Inu Yehova Mulungu wathu, tipulumutseni ndithu mʼdzanja lake, kuti maufumu onse a dziko lapansi adziwe kuti Inu nokha, Inu Yehova, ndinu Mulungu.”
Yankho la Mulungu Kudzera mwa Yesaya
20Ndipo Yesaya mwana wa Amozi anatumiza uthenga kwa Hezekiya wakuti, “Yehova Mulungu wa Israeli akuti, ‘Ndamva pemphero lako lonena za Senakeribu mfumu ya ku Asiriya.’ ” 21Mawu amene Yehova wayankhula wotsutsana naye ndi awa:
“Namwali wa Ziyoni
akukunyoza ndi kukuseka iwe.
Mwana wamkazi wa Yerusalemu
akupukusa mutu wake kumbuyo kwako.
22Kodi iweyo wanyoza ndi kuchitira chipongwe yani?
Kodi ndani amene wamufuwulira mawu ako
ndi kumuyangʼana monyada?
Wachitiratu izi Woyera wa Israeli!
23Kudzera mwa amithenga ako
wonyoza Ambuye.
Ndipo wanena kuti,
‘Ndi magaleta ochuluka
ndinakwera mapiri ataliatali,
pa msonga za mapiri a Lebanoni.
Ndigwetsa mitengo yake ya mkungudza yayitali kwambiri,
mitengo yake ya payini yabwino kwambiri.
Ndalowanso mʼkati mwake mwenimweni,
mwa nkhalango yake yowirira kwambiri.
24Ndakumba zitsime ku mayiko achilendo
ndipo ndinamwa madzi a kumeneko.
Ndi mapazi anga
ndawumitsa mitsinje yonse ya ku Igupto.’ ”
25“ ‘Kodi sunamvepo?
Zimenezi ndinazikhazikitsa kalekale.
Ndinazikonzeratu masiku amakedzana;
tsopano ndachita kuti zichitikedi,
iwe kwako kunali kungosandutsa mizinda yotetezedwa
kukhala milu ya miyala.
26Anthu a kumeneko ndi opanda mphamvu,
athedwa nzeru ndipo ali ndi manyazi.
Ali ngati mbewu za mʼmunda,
ngati udzu wanthete,
ali ngati udzu womera pa denga,
umene umawuma usanakule nʼkomwe.’ ”
27“ ‘Koma Ine ndimadziwa kukhala kwako,
kutuluka kwako ndi kulowa kwako,
ndi mkwiyo wako pa Ine.
28Chifukwa chakuti wandikwiyira
ndipo ndamva za mwano wako,
ndidzakola mphuno yako ndi mbedza
ndi kuyika chitsulo changa mʼkamwa mwako,
ndipo ndidzakubweza pokudzeretsa
njira yomwe unadzera pobwera.’
29“Koma iwe Hezekiya, chizindikiro chako chidzakhala ichi:
“Chaka chino mudzadya tirigu wamphulumukwa,
ndipo chaka chamawa mudzadya tirigu wongodzimerera.
Koma chaka chachitatu mudzadzala ndi kukolola,
mudzawoka mphesa ndipo mudzadya zipatso zake.
30Anthu a nyumba ya Yuda amene adzatsale
adzazika mizu ndi kubereka zipatso.
31Pakuti ku Yerusalemu kudzachokera anthu otsala,
ndi ku phiri la Ziyoni kudzachokera gulu la anthu opulumuka.”
“Changu cha Yehova Wamphamvuzonse chidzachita zimenezi.
32“Choncho chimene Yehova akunena za mfumu ya ku Asiriya ndi ichi:
“ ‘Iye sadzalowa mu mzinda umenewu
kapena kuponyamo muvi.
Sadzayandikira mzindawu ndi zishango zake
kapena kumanga nthumbira ya nkhondo.
33Adzabwerera potsata njira imene anadzera pobwera;
sadzalowa mu mzinda umenewu,
akutero Yehova.
34Ndidzateteza mzinda umenewu kuwupulumutsa,
chifukwa cha Ine mwini ndiponso chifukwa cha Davide mtumiki wanga.’ ”
35Usiku umenewo mngelo wa Yehova anapita ku misasa ya ku Asiriya ndi kupha ankhondo 185,000. Ndipo pamene anthu anadzuka mmawa, taonani, mitembo inali ngundangunda! 36Choncho Senakeribu mfumu ya ku Asiriya anapasula misasa ndi kuchoka. Anabwerera ku Ninive nakakhala kumeneko.
37Tsiku lina, pamene Senakeribu ankapembedza mʼnyumba ya Nisiroki mulungu wake, ana ake Adirameleki ndi Sarezeri anamupha ndi lupanga ndipo anathawira ku dziko la Ararati. Tsono Esrahadoni, mwana wake, analowa ufumu mʼmalo mwake.
希西迦向以賽亞求助
1希西迦王聽了就撕裂衣服,披上麻衣,進入耶和華的殿。 2他派身披麻衣的宮廷總管以利亞敬、書記舍伯那和祭司中的長者去見亞摩斯的兒子以賽亞先知, 3對他說:「希西迦說,『今天是遭難、蒙羞、受辱的日子,就像嬰兒要出生,產婦卻無力生產一樣。 4亞述王派他的將軍來辱罵永活的上帝,也許你的上帝耶和華聽見那些話,就會懲罰他。所以,請你為我們這些剩下的人禱告。』」 5希西迦王的臣僕說完這些話後, 6以賽亞對他們說:「告訴你們主人,耶和華這樣說,『你不要因亞述王的僕人那些褻瀆我的話而害怕。 7我必驚動19·7 「驚動」希伯來文是「使靈進入」。亞述王的心,讓他聽見一些風聲後便返回本國,在那裡死於刀下。』」
希西迦向上帝禱告
8亞述的將軍聽說亞述王已離開拉吉,便回去見王,發現王在攻打立拿。 9亞述王聽說古實王特哈加正前來攻打他,便再次派使者去對希西迦說: 10「不要讓你所倚靠的上帝愚弄你,說什麼耶路撒冷必不會被亞述王攻陷。 11你肯定聽過亞述諸王掃滅列國的事,難道你能倖免嗎? 12我先祖毀滅了歌散、哈蘭、利色和提·拉撒的伊甸人,這些國家的神明救得了他們嗎? 13哈馬王、亞珥拔王、西法瓦音城的王、希拿王和以瓦王如今在哪裡呢?」
14希西迦從使者手中接過信,讀完後走進耶和華的殿,在耶和華面前展開信, 15禱告說:「坐在二基路伯天使之上、以色列的上帝耶和華啊,唯有你是天下萬國的上帝,你創造了天地。 16耶和華啊,求你側耳垂聽!耶和華啊,求你睜眼察看!求你聽聽西拿基立派使者來辱罵永活上帝的話。 17耶和華啊,亞述諸王確實掃滅列國,使其土地荒涼, 18把列國的神像丟在火中。因為那些神像只是人用木頭石頭製造的,根本不是神。 19我們的上帝耶和華啊,現在求你從亞述王手中拯救我們,讓天下萬國都知道唯有你是耶和華。」
以賽亞給希西迦的信息
20亞摩斯的兒子以賽亞派人告訴希西迦:「以色列的上帝耶和華說,『我已經聽見你關於亞述王西拿基立的禱告。 21以下是耶和華對他的判語,
『錫安的居民藐視你,嘲笑你;
耶路撒冷的居民朝你逃竄的背影搖頭。
22你在侮辱、褻瀆誰呢?
你不放在眼裡、
高聲罵的是誰呢?
是以色列的聖者!
23你藉你的使者辱罵主,
你說你率領許多戰車上到群山之巔,
上到黎巴嫩的巔峰,
砍下最高的香柏樹和上好的松樹,
征服最高的山和最美的樹林。
24你自誇已在外邦之地挖井取水,
已用腳掌踏乾埃及的河流。
25『難道你不知道這是我在太初所定、
在亙古就籌畫好的嗎?
如今我實現了所定的計劃——
藉著你使堅城淪為廢墟。
26城中的居民軟弱無力,
驚慌失措,羞愧難當,
脆弱如野草和菜蔬,
又像還未長大就被曬焦的房頂草。
27『你起你坐,你出你進,
你向我發怒,我都知道。
28因為你向我發怒,
你狂傲的話達到了我耳中,
我要用鉤子鉤住你的鼻子,
把嚼環放在你嘴裡,
使你原路返回。』
29「希西迦啊,我要賜給你們一個兆頭,你們今年要吃野生的,明年也要吃自然生長的,後年要播種收割,栽種葡萄園,吃園中的果子。 30猶大的倖存者要再次向下扎根,向上結果。 31因為將有餘民從耶路撒冷出來,有倖存者從錫安山出來。耶和華必熱切地成就這事。
32「至於亞述王,耶和華說,『他必不能進這城或向這裡射一箭,必不能手持盾牌兵臨城下或修築攻城的高臺。 33他從哪條路來,也將從哪條路回去,他必進不了這城。這是耶和華說的。 34我必為自己和我僕人大衛而保護、拯救這城。』」
35當晚,耶和華的天使到亞述營中殺了十八萬五千人。人們清早起來,發現到處是屍體。 36亞述王西拿基立便拔營回國,住在尼尼微。 37一天,亞述王在他的神明尼斯洛的廟裡祭拜時,他的兩個兒子亞得米勒和沙利色用刀殺了他,逃往亞拉臘。他的另一個兒子以撒哈頓繼位。