2 Mafumu 12 – CCL & CCB

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Mafumu 12:1-21

Yowasi Akonzanso Nyumba ya Yehova

1Mʼchaka chachisanu ndi chiwiri cha Yehu, Yowasi anakhala mfumu, ndipo analamulira mu Yerusalemu zaka makumi anayi. Amayi ake anali Zibiya wa ku Beeriseba. 2Yowasi anachita zolungama pamaso pa Yehova masiku onse amene wansembe Yehoyada ankamulangiza. 3Komabe sanachotse malo opembedzerapo mafano ndipo anthu anapitiriza kupereka nsembe ndi kufukiza lubani ku malo opembedzerako mafanowo.

4Yowasi anati kwa ansembe, “Tolerani ndalama zonse zimene zimaperekedwa monga chopereka chopatulika ku Nyumba ya Yehova, ndalama zonse zamsonkho wa munthu aliyense, ndalama zomwe munthu amapereka akalonjeza ndiponso ndalama zimene munthu amapereka mwaufulu ku Nyumba ya Yehova. 5Wansembe aliyense alandire ndalamazo kuchokera kwa abwenzi ake, ndipo zigwiritsidwe ntchito yokonzera chilichonse chimene chipezeke kuti ndi chowonongeka mʼnyumbayo.”

6Koma pofika chaka cha 23 cha ufumu wa Yowasi, ansembewo anali asanakonze nyumbayo. 7Choncho Mfumu Yowasi inayitanitsa wansembe Yehoyada ndi ansembe ena ndipo inafunsa kuti, “Chifukwa chiyani simukukonza malo owonongeka a mʼnyumbayi? Musasungenso ndalama zina zochokera kwa abwenzi anu, koma muzipereke kuti akonzere nyumbayi.” 8Ansembe anavomera kuti salandiranso ndalama kuchokera kwa anthu ndipo kuti sindiwo amene ati akonzenso nyumbayo.

9Koma wansembe Yehoyada anatenga bokosi ndipo anabowola chivundikiro chake. Anayika bokosilo pambali pa guwa lansembe, kudzanja lamanja la aliyense amene akulowa mʼNyumba ya Yehovayo. Ansembe amene ankalondera pa khomopo ankaponya mʼbokosi ndalama zonse zimene ankabwera nazo ku nyumba ya Yehova. 10Nthawi zonse akaona kuti mʼbokosimo muli ndalama zambiri, mlembi wa mfumu ndi mkulu wa ansembe ankabwera ndipo ankawerenga ndalama zomwe anthu ankabwera nazo ku Nyumba ya Yehova ndi kuziyika mʼmatumba. 11Ankati akadziwa kuti ndalamazo zilipo zingati, ankazipereka kwa anthu amene ankayangʼanira ntchito yokonza nyumbayo. Ndalamazo ankalipira anthu amene ankagwira ntchito yokonza Nyumba ya Yehova, amisiri a matabwa ndi amisiri omanga nyumba, 12amisiri a miyala ndiponso anthu ophwanya miyala. Iwo ankagula matabwa ndi miyala yosema yokonzera Nyumba ya Yehova ndipo ankalipira zinthu zonse zofunika pokonzanso nyumbayo.

13Koma ndalama zomwe anthu ankabwera nazo ku nyumbayo sanagulire siliva wopangira mabeseni, zozimitsira nyale, mbale zowazira magazi, malipenga kapena ziwiya zina zilizonse zagolide kapena zasiliva za ku Nyumba ya Yehova. 14Ndalamazi anazipereka kwa anthu antchito amene anazigwiritsa ntchito yokonzera nyumbayo. 15Koma sanawafunse kuti afotokoze kagwiritsidwe ntchito ka ndalama zolipira amene ankagwira ntchito, chifukwa anthuwo ankagwira ntchitoyo mokhulupirika kwambiri. 16Ndalama zomwe zinkaperekedwa pa nsembe yopepesera machimo ndi nsembe yoperekedwa chifukwa cha tchimo sanabwere nazo ku Nyumba ya Yehova pakuti zinali za ansembe.

17Pa nthawi imeneyo, Hazaeli, mfumu ya Aramu anapita kukathira nkhondo mzinda wa Gati nawulanda. Kenaka Hazaeli anatembenuka kupita kukathira nkhondo mzinda wa Yerusalemu. 18Koma Yowasi mfumu ya Yuda anatenga zinthu zonse zopatulika zomwe anazipatula Yehosafati, Yehoramu, ndi Ahaziya abambo ake, mafumu a Yuda ndi mphatso zonse zomwe iye mwini anazipereka: golide yense amene anapezeka mʼnyumba yosungiramo chuma cha mʼnyumba ya Yehova ndi zomwe zinali mʼnyumba ya mfumu, nazipereka kwa Hazaeli mfumu ya Aramu. Pamenepo iye anachoka ku Yerusalemuko.

19Ndipo ntchito zina za Yowasi ndi zonse zimene anachita, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri ya mafumu a Yuda? 20Akuluakulu ake anamuchitira chiwembu ndi kumupha ku Beti Milo, pa njira yotsikira ku Silo. 21Yozakara mwana wa Simeati ndi Yehozabadi mwana wa Someri atumiki ake anamukantha nafa. Ndipo anamuyika mʼmanda pamodzi ndi makolo ake mu Mzinda wa Davide. Ndipo Amaziya mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake.

Chinese Contemporary Bible (Simplified)

列王纪下 12:1-21

约阿施做犹大王

1以色列耶户执政第七年,约阿施登基,在耶路撒冷执政四十年。他母亲叫西比亚,是别示巴人。 2耶何耶大祭司的教导下,约阿施一生做耶和华视为正的事。 3但他没有拆毁丘坛,人们仍在那里献祭烧香。

4约阿施对祭司们说:“你们要收集那些奉献到耶和华殿的圣银,即人口普查时收取的银子、个人还愿的银子和自愿奉献的银子。 5每位祭司要从奉献的人手中收取银子,用来修殿。” 6可是,直到约阿施执政第二十三年,祭司仍未动工。 7约阿施召来耶何耶大祭司及其他祭司,对他们说:“你们为什么还不修殿呢?不要再向奉献的人收银子了,要把所收的银子交出来修殿。” 8祭司们答应不再向民众收钱,但也不动工修殿。

9耶何耶大祭司在耶和华殿的入口右边的祭坛旁放了一个箱子,箱盖上开了个洞。守门的祭司将奉献到耶和华殿的所有银子放进箱子里。 10箱子里的银子多了,王的书记和大祭司就把银子点好,装在袋子里。 11他们将称好的银子交给修耶和华殿的督工。督工把报酬转交给在殿里工作的木匠、建筑工人、 12泥水匠和石匠,购买修耶和华殿用的木料和凿好的石头,并支付其他的修殿费用。 13献到耶和华殿里的银子没有用于制造殿里的银碗、蜡剪、盆、号及其他金银器皿, 14只用于修殿。 15督工们办事忠诚可靠,不需要跟他们清算账目。 16赎过祭和赎罪祭的银子没有带到耶和华的殿里,而是归给祭司。

17那时,亚兰哈薛攻陷了迦特,准备进攻耶路撒冷18犹大约阿施把先王约沙法约兰亚哈谢和他自己奉献的圣物以及耶和华殿里和王宫库房里的所有金子都送给了亚兰哈薛哈薛便从耶路撒冷退兵。

19约阿施其他的事及其一切作为都记在犹大的列王史上。 20约阿施的臣仆谋反,在去悉拉途中的米罗宫杀了他。 21杀他的是示米押的儿子约撒甲朔默的儿子约萨拔约阿施葬在大卫城他的祖坟里。他儿子亚玛谢继位。