2 Mafumu 11 – CCL & CCBT

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Mafumu 11:1-21

Ataliya ndi Yowasi

1Ataliya amayi ake a Ahaziya ataona kuti mwana wawo wafa, ananyamuka nakawononga banja lonse la mfumu. 2Koma Yehoseba, mwana wamkazi wa Mfumu Yehoramu, mlongo wake wa Ahaziya, anatenga Yowasi mwana wa Ahaziya, namusunga kutali ndi ana a mfumu amene ankati awaphewo. Anamuyika iye pamodzi ndi mlezi wake mʼchipinda chogona chamʼkati kubisira Ataliya kotero iye sanaphedwe. 3Mwanayo anakhala mobisala pamodzi ndi mlezi wake mʼnyumba ya Yehova kwa zaka zisanu ndi chimodzi pamene Ataliya ankalamulira dzikolo.

4Koma mʼchaka chachisanu ndi chiwiri, Yehoyada anatumiza mawu kukayitana atsogoleri olamulira asilikali 100 olondera mfumu ndiponso alonda olonda nyumba yaufumu ndipo anabwera nawo mʼNyumba ya Yehova. Iye anapangana nawo pangano ndipo anawalumbiritsa mʼnyumba ya Yehova. Kenaka anawaonetsa mwana wamwamuna wa mfumu uja. 5Yehoyada anawalamulira kuti, “Chimene muti muchite ndi ichi: Inu magulu atatu amene muti mudzakhale pa ntchito tsiku la Sabata, gulu loyamba lidzalondera nyumba ya mfumu, 6gulu lachiwiri lidzalondera Chipata cha Suri, ndipo gulu lachitatu lidzalondera chipata cha kumbuyo kwa asilikali amene amasinthana polondera nyumbayo. 7Ndipo inu amene muli mʼmagulu ena awiri amene simugwira ntchito pa tsiku la Sabata, nonse mudzalondere mfumu ku nyumbayo. 8Mudzakhale mozungulira mfumuyo, munthu aliyense ali ndi chida mʼmanja mwake. Wina aliyense amene adzakuyandikireni adzayenera kuphedwa. Muzikhala pafupi ndi mfumu kulikonse kumene ikupita.”

9Atsogoleri olamulira asilikali 100 aja anachitadi zonse monga analamulira wansembe Yehoyada. Aliyense anatenga anthu ake, iwo amene amakagwira ntchito pa tsiku la Sabata ndi amene amapita kukapuma ndipo anabwera kwa wansembe Yehoyada. 10Ndipo wansembeyo anawapatsa asilikaliwo mikondo ndi zishango zimene zinali za mfumu Davide ndipo zinali mʼNyumba ya Yehova. 11Alondawo, aliyense ali ndi chida mʼmanja mwake, anayima mozungulira mfumu, pafupi ndi guwa lansembe ndi nyumbayo, kuchokera mbali ya kummwera mpaka mbali ya kumpoto kwa nyumbayo.

12Yehoyada anatulutsa mwana wa mfumuyo namuveka chipewa chaufumu ndipo anamupatsa Buku la Chipangano ndi kumuyika kukhala mfumu. Iwo anamudzoza ndipo anthu anamuwombera mʼmanja akufuwula kuti, “Mfumu ikhale ndi moyo wautali!”

13Ataliya atamva phokoso limene alonda ndi anthuwo amachita, anapita ku Nyumba ya Yehova kumene kunali anthuwo. 14Iye anayangʼana naona mfumu itayima pa chipilala, potsata mwambo waufumu. Atsogoleri a asilikali ndi oyimba malipenga anali pafupi ndi mfumuyo, ndipo anthu onse a mʼderalo ankasangalala ndi kuyimba malipenga. Pamenepo Ataliya anangʼamba mkanjo wake nafuwula kuti, “Kuwukira! Kuwukira!”

15Wansembe Yehoyada analamula atsogoleri a asilikali 100 amene amayangʼanira asilikaliwo kuti, “Mutulutseni ameneyo pakati panu ndipo muphe ndi lupanga aliyense amene adzamutsata.” Pakuti nʼkuti wansembeyo atanena kuti, “Ataliyayo asaphedwere mʼNyumba ya Yehova.” 16Choncho anamugwira pamene amafika pa malo amene akavalo amalowera ku nyumba ya mfumu ndipo anamuphera pamenepo.

17Tsono Yehoyada anachititsa pangano pakati pa Yehova ndi mfumu ndi anthu kuti adzakhala anthu a Yehova. Iye anachititsanso pangano pakati pa mfumu ndi anthu. 18Anthu onse a mʼdzikomo anapita ku nyumba ya Baala nakayigwetsa. Iwo anaphwanya kotheratu maguwa ansembe ndi mafano ake ndipo anapha Matani wansembe wa Baala patsogolo pa maguwa pomwepo.

Pamenepo wansembe Yehoyada anasankha oyangʼanira Nyumba ya Yehova. 19Iye anatenga atsogoleri a asilikali 100 aja, alonda olonda nyumba yaufumu pamodzi ndi anthu onse a mʼdzikomo ndipo onse pamodzi anayitulutsa mfumu mʼNyumba ya Yehova ndi kukalowa ku nyumba yaufumu podzera pa chipata cha alonda. Ndipo mfumuyo inakhala pa mpando wake waufumu. 20Choncho anthu onse a mʼdzikomo anasangalala. Ndipo mu mzindamo munakhala bata chifukwa Ataliya nʼkuti ataphedwa ndi lupanga ku nyumba ya mfumu.

21Yowasi anali wa zaka zisanu ndi ziwiri pamene anayamba kulamulira.

Chinese Contemporary Bible (Traditional)

列王紀下 11:1-21

耶何耶大立約阿施為王

1亞哈謝的母親亞她利雅見兒子死了,便決定除掉王室後裔。 2約蘭王的女兒、亞哈謝的妹妹約示芭把亞哈謝的兒子約阿施從被殺的王子中偷出來,將他和乳母藏在一間臥室裡,才躲過亞她利雅,使約阿施沒有被殺。 3約阿施和他的乳母在耶和華的殿裡藏了六年,那時亞她利雅篡位當政。

4第七年,耶何耶大派人召迦利11·4 迦利人」指雇來保護王的外族衛兵。和衛兵的百夫長們到耶和華的殿裡,與他們立約,讓他們在耶和華的殿裡起誓,然後把約阿施王子帶到他們面前。 5耶何耶大吩咐他們說:「你們在安息日值班的,三分之一要守衛王宮, 6三分之一要守衛蘇珥門,三分之一要守住衛兵院後門。你們要輪流守衛。 7安息日沒有值班的兩隊要在耶和華的殿裡保護王, 8各人要手持兵器護衛在王周圍。凡擅自闖入者,都要處死。無論王去哪裡,你們都要緊隨左右。」 9眾百夫長依令而行,各自率領安息日值班和休班的隨從來見耶何耶大10耶何耶大把耶和華殿中大衛王的矛槍和盾牌交給百夫長。 11從殿右到殿左,在祭壇和殿周圍,衛兵都手持兵器護衛王。 12耶何耶大祭司領王子出來,給他戴上王冠,把律法書交給他,膏立他為王。眾人都鼓掌高呼:「願王萬歲!」

13亞她利雅聽見衛兵和眾人的歡呼聲,便走進耶和華的殿,眾人都聚集在那裡。 14她看見王照例站在柱旁,百夫長和吹號的人侍立在王左右,眾人都歡呼吹號,便撕裂衣服喊叫:「反了!反了!」 15耶何耶大祭司認為不可在耶和華的殿裡處死亞她利雅,便命令領兵的百夫長:「把她帶出去。凡跟隨她的,都要殺掉。」 16他們抓住她,把她帶到馬匹進出王宮的入口,在那裡殺了她。

17耶何耶大讓王及民眾與耶和華立約,做耶和華的子民,也讓王與民眾立約。 18於是,民眾出去拆毀了巴力廟,砸碎祭壇和偶像,在壇前殺了巴力的祭司瑪坦耶何耶大派守衛保護耶和華的殿, 19然後率領百夫長、迦利人、衛兵和民眾,護送王從耶和華的殿下來,經過衛兵院的門進入王宮。這樣,約阿施坐上了王位。 20民眾都歡喜快樂,城裡安定,因為亞她利雅已在王宮那裡被處死。 21約阿施七歲登基。