2 Atesalonika 3 – CCL & CCB

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Atesalonika 3:1-18

Tipempherereni

1Potsiriza, abale, mutipempherere kuti uthenga wa Ambuye ufalikire msanga ndi kulemekezedwa monga momwe munachitira inu. 2Ndipo pempherani kuti tilanditsidwe mʼmanja mwa anthu ovuta ndi oyipa, pakuti si onse amene ali nacho chikhulupiriro. 3Koma Ambuye ndi wokhulupirika, ndipo adzakulimbikitsani ndi kukutetezani kwa woyipayo. 4Tili ndi chikhulupiriro mwa Ambuye kuti mukuchita zonse ndipo mudzapitirira kuchita zimene tinakulamulirani. 5Ambuye atsogolere mitima yanu kuti mudziwe chikondi cha Mulungu ndiponso kupirira kumene Khristu amapereka.

Awachenjeza za Kusagwira Ntchito

6Abale, tikukulamulani mʼdzina la Ambuye Yesu Khristu, kuti mupewe mʼbale aliyense amene ndi waulesi ndi wachisokonezo, wosafuna kutsata zimene tinakuphunzitsani. 7Pakuti inu mukudziwa zimene muyenera kuchita pofuna kutitsatira. Ife sitinali alesi pamene tinali nanu 8ndipo sitinadye chakudya cha aliyense osalipira. Komatu tinkagwira ntchito mwamphamvu usiku ndi usana kuti tisakhale cholemetsa kwa aliyense. 9Sitinachite zimenezi chifukwa choti tinalibe mphamvu zolamula kuti mutithandize koma kuti tikhale chitsanzo choti mutsatire. 10Pakuti ngakhale pamene tinali nanu, tinakupatsani lamulo lakuti, “Munthu wosafuna kugwira ntchito, asadye.”

11Ife tikumva kuti pakati panu pali ena amene ndi alesi. Iwo safuna kugwira ntchito, koma amangolowerera pa za eni. 12Mʼdzina la Ambuye Yesu Khristu, tikuwalamula ndi kuwakakamiza kuti azigwira ntchito mwabata ndi kumadya chakudya chodzigwirira ntchito okha. 13Koma inu abale, musatope nʼkuchita zabwino.

14Ngati wina aliyense akana kumvera malangizo athu a mʼkalatayi, mumuonetsetse ameneyo ndipo musayanjane naye kuti achite manyazi. 15Komatu musamutenge kukhala mdani, koma muchenjezeni ngati mʼbale.

Malonje Otsiriza

16Tsopano Ambuye mwini mtendere akupatseni mtendere nthawi zonse mwa njira iliyonse. Ambuye akhale ndi inu nonse.

17Ine Paulo, ndikulemba malonje awa ndi dzanja langa, chimene ndi chizindikiro chodziwika mʼmakalata anga onse. Umo ndi mmene ndimalembera.

18Chisomo cha Ambuye athu Yesu Khristu chikhale ndi inu nonse.

Chinese Contemporary Bible (Simplified)

帖撒罗尼迦后书 3:1-18

请求代祷

1弟兄姊妹,最后我还要请你们为我们祷告,好使主的道像在你们那里一样迅速传开,受到尊崇, 2并使我们能避开那些邪恶的人,因为不是人人都有信心。

3主是信实的,祂必使你们刚强,保护你们脱离那恶者。 4我们靠着主深信你们现在遵行了我们的吩咐,而且以后还会继续遵行。

5愿主引导你们的心领悟上帝的爱和基督的坚忍。

不可游手好闲

6弟兄姊妹,现在我们奉主耶稣基督的名吩咐你们,要远离那些游手好闲、不遵守我们教导的信徒。 7你们自己知道应该怎样效法我们,因为我们在你们那里的时候,并没有懒懒散散, 8也没有白吃谁的饭,而是昼夜辛勤工作,免得成为你们任何人的负担。 9我们并不是没有权利接受供应,而是要给你们树立学习的榜样。 10我们在你们那里的时候,曾吩咐过你们:不肯工作的人没有资格吃饭。 11我们听说在你们当中有些人游手好闲,无所事事,却专管闲事。 12我们奉主耶稣基督的名吩咐并劝诫这些人要安分守己,自食其力。

13弟兄姊妹,你们要坚持行善,不要灰心。 14如果有人不听从这信上的教导,要注意提防他,不要和他来往,好使他羞愧。 15只是不可把他当作仇人,要像对待弟兄姊妹一样劝诫他。

问候

16愿平安之主随时随地亲自赐你们平安!愿主与你们同在! 17我保罗在这里亲笔问候你们,这是我的笔迹,我所有的信都以此为记号。

18愿我们主耶稣基督的恩典与你们众人同在!