2 Akorinto 5 – CCL & CRO

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Akorinto 5:1-21

Matupi Atsopano

1Popeza tikudziwa kuti ngati msasa wa dziko lapansi umene tikukhalamo uwonongeka, tili ndi nyumba yochokera kwa Mulungu, nyumba yamuyaya yakumwamba, osati yomangidwa ndi manja a anthu. 2Pakali pano tibuwula, ndi kulakalaka kuvala nyumba yathu ya kumwambayo, 3chifukwa tikavala, sitidzapezekanso amaliseche. 4Pamene tili mu msasa uno, timalemedwa ndipo timabuwula, chifukwa sitifuna kukhala amaliseche koma ovala nyumba yathu ya kumwamba, kuti chimene chili chakufa chimezedwe ndi moyo. 5Tsono ndi Mulungu amene anatikonzeratu ife kuti tilandire zimenezi. Iye anatipatsa Mzimu ngati chikole, kutsimikizira zimene zikubwera.

6Nʼchifukwa chake nthawi zonse timalimba mtima, ndipo timadziwa kuti pamene tikukhala mʼthupi, ndiye kuti tili kutali ndi Ambuye. 7Ife timakhala mwachikhulupiriro, osati mwa zooneka ndi maso. 8Inde, ife tikulimba mtima, ndipo tikanakonda kulekana nalo thupi lathu ndi kukhala ndi Ambuye. 9Choncho timayesetsa kukondweretsa Ambuye, ngakhale tikhale mʼthupi, kapena tichokemo. 10Pakuti tonsefe tiyenera kukaonekera pa mpando woweruza wa Khristu, kuti aliyense wa ife akalandire zomuyenera molingana ndi zimene anachita ali mʼthupi; zabwino kapena zoyipa.

Ntchito Yoyanjanitsa

11Tsono popeza tikudziwa tanthauzo la kuopa Ambuye, ife timayesetsa kukopa anthu. Mulungu amatidziwa bwino lomwe, ndipo tikukhulupirira kuti inunso mumatidziwa bwino mʼmitima mwanu. 12Sitikudzichitiranso tokha umboni kwa inu, koma tikukupatsani mwayi oti muzitinyadira. Tikufuna kuti muwayankhe amene amanyadira zinthu zooneka ndi maso osati zimene zili mu mtima. 13Ngati ndife amisala, monga amanenera ena, nʼchifukwa chofuna kuti Mulungu alemekezedwe. Ngati si ife amisala, nʼkuti inu muthandizike. 14Pakuti chikondi cha Khristu ndicho chimatikakamiza, chifukwa tikutsimikiza kuti mmodzi anafera anthu onse, kotero kuti anthu onse anafanso. 15Ndipo Iye anafera anthu onse kuti amene ali ndi moyo, asakhale ndi moyo wofuna kudzikondweretsa okha, koma azikondweretsa amene anawafera naukitsidwa chifukwa cha iwowo.

16Choncho, kuyambira tsopano mpaka mʼtsogolo ife sitiganizirapo za munthu aliyense monga mwanzeru za umunthu, ngakhale kuti poyamba tinkaganiza za Khristu mʼnjira imeneyi, koma tsopano sititeronso. 17Nʼchifukwa chake, ngati munthu aliyense ali mwa Khristu, ndi wolengedwa kwatsopano; zinthu zakale zapita taonani, zakhala zatsopano. 18Zonsezi zichokera kwa Mulungu amene anatiyanjanitsa ndi Iye mwini kudzera mwa Khristu ndipo anatipatsa ife utumiki wa chiyanjanitso. 19Mulungu ankayanjanitsa dziko lapansi kwa Iye mwini kudzera mwa Khristu, osawerengera anthu monga mwa zochimwa zawo. Ndipo watisungitsa ife uthenga uwu wa chiyanjanitso. 20Choncho ife ndi akazembe a Khristu, monga ngati Mulungu akudandaulira anthu kudzera mwa ife. Ife tikukupemphani inu mʼmalo mwa Khristu kuti, yanjanitsidwani ndi Mulungu. 21Chifukwa cha ife, Mulungu anasandutsa wopanda tchimoyo kukhala tchimo, kuti mwa Iye ife tikakhale chilungamo cha Mulungu.

Knijga O Kristu

2 Korinćanima 5:1-21

Nova tijela

1Znamo da ćemo, kad se ovaj šator5:1 U grčkome: naša zemaljska kuća. u kojemu sada živimo sruši—kad umremo i napustimo tijela—imati nova tijela, vječni dom u nebu, koji će biti Božje djelo, a ne djelo ljudskih ruku. 2Zato uzdišemo u ovim tijelima i čeznemo za danom kada ćemo obući nebeska tijela. 3U njih obučeni, nećemo se naći golima. 4U ovima zemaljskim tijelima uzdišemo i stenjemo, ali ne zato što bismo željeli umrijeti i izići iz njih, već zato što se želimo obući u nova tijela, tako da vječni život proguta ova naša smrtna tijela. 5Za to nas je pripremio sam Bog i dao nam svojega Svetog Duha kao jamstvo.

6Stoga uvijek imamo pouzdanja iako znamo da dokle god smo u ovome tijelu, nismo kod kuće, kod Gospodina. 7Živimo po vjeri, a ne po onome što vidimo. 8Puni smo pouzdanja i radije bismo izišli iz ovih tijela jer ćemo tada biti u svojem domu, kod Gospodina. 9Zato mu uvijek nastojimo ugoditi, bilo da ostajemo u ovomu tijelu ili iz njega odlazimo, 10jer ćemo svi morati stati pred Kristov sud i svatko će primiti što je zaslužio: nagradu ili kaznu, već prema tome je li u ovomu tijelu činio dobro ili zlo.

Božji smo poslanici

11Zato puni straha Gospodnjega nastojimo pridobiti ljude za Boga. Bog zna da smo iskreni, a nadam se da i vi to znate. 12Ne hvalimo to opet sami sebe, nego vam dajemo razlog da se ponosite nama, kako biste imali što odgovoriti onima koji se ponose izvanjskim stvarima umjesto iskrenim srcem. 13Ako se čini da smo nerazumni, neka to ostane između Boga i nas. Ako smo zdrave pameti, to je za vaše dobro. 14Kristova ljubav prema nama ne ostavlja nam izbora kad shvatimo da je on jedan umro umjesto svih, pa su prema tome i svi oni nečemu umrli. 15On je, naime, umro umjesto svih kako oni koji su živi, više ne bi živjeli da ugode sebi, već da njemu koji je umro i uskrsnuo za njih. 16Zato mi više nikoga ne procjenjujemo po tjelesnim stvarima. Prije smo i Krista cijenili prema ljudskim mjerilima, ali sada to više ne činimo. 17Kad je tko u Kristu, on je novo stvorenje. Stari je čovjek nestao, a rodio se novi.

18Sve to dolazi od Boga, koji nas je kroz Krista pomirio sa sobom i koji nam je povjerio zadaću da izmirujemo ljude s njim. 19Jer Bog je u Kristu pomirio svijet sa sobom da više ljudima ne uračunava njihove prijestupe, a nama je dao da govorimo o tome pomirenju. 20Tako obavljamo poslaničku službu i u ime samoga Krista vas preklinjemo: pomirite se s Bogom! 21Jer je Bog Krista koji nikada nije zgriješio učinio umjesto nas grijehom da bismo mi u njemu mogli postati Božjom pravednošću.