2 Akorinto 2 – CCL & CCBT

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Akorinto 2:1-17

1Kotero ndinatsimikiza maganizo anga kuti ndisachitenso ulendo wina owawa wobwera kwanuko. 2Pakuti ngati ndikumvetsani chisoni, kodi angandisangalatse ndani, kupatula inuyo amene ndakumvetsani chisoni? 3Nʼchifukwa chake ndinakulemberani monga ndinachitiramo kuti nditabwera kwanuko ndisadzamve chisoni ndi anthu oyenera kundisangalatsa. Ndinali ndi chikhulupiriro ndi inu nonse kuti inuyo mukakhala ndi chimwemwe poona kuti inenso ndili ndi chimwemwe. 4Pakuti ndinakulemberani kalata ija ndili wopsinjika ndi wowawidwa mtima kwambiri ndi kutuluka misozi yambiri, osati pofuna kukumvetsani chisoni koma kuti ndikudziwitseni kuti ndimakukondani kwambiri.

Za Kukhululukira Wolakwa

5Koma ngati wina wamvetsa chisoni, sanamvetse chisoni ine ndekha, koma koposa mosawonjezera wakhumudwitsa nonsenu, kunenatu mosawonjezera. 6Chilango chimene ambiri a inu mwamupatsa munthu ameneyu nʼchokwanira. 7Mʼmalo mwake tsono, muyenera kumukhululukira ndi kumulimbikitsa mtima kuti asamve chisoni choposa muyeso, angataye mtima. 8Choncho ndikukupemphani kuti mutsimikizire chikondi chanu pa iye. 9Cholinga china chimene ndinakulemberani kalata ija chinali chofuna kukuonani ngati mudzandimvera pa zonse. 10Aliyense amene mumukhululukire, inenso ndimukhululukira. Ndipo ndikakhululukira, ngati pali kanthu koti ndikhululukire, ndiye kuti ndakhululuka chifukwa cha inu pamaso pa Khristu, 11kupewa kuti Satana angapezere mpata pa ife, pajatu timadziwa machenjerero ake.

Atumiki a Pangano Latsopano

12Tsono nditafika ku Trowa kuti ndilalikire Uthenga Wabwino wa Khristu, nʼkupeza kuti Ambuye anditsekulira khomo, 13ndinasowa mtendere mu mtima mwanga, chifukwa sindinapezeko mʼbale wanga Tito. Choncho ndinatsanzikana ndi anthu kumeneko nʼkupita ku Makedoniya.

14Koma tithokoze Mulungu amene amatitsogolera nthawi zonse monga ogwidwa ku nkhondo a Khristu pa chipambano chake. Tsono amatigwiritsa ntchito yofalitsa ponseponse nzeru zodziwira Khristu ngati fungo labwino. 15Pakuti kwa Mulungu ndife fungo labwino la Khristu pakati pa iwo amene akupulumutsidwa ndi amene akuwonongeka. 16Kwa amene akuwonongeka ndife fungo la imfa, limawapha. Ndipo kwa amene akupulumuka ndife fungo lamoyo, limawapatsa moyo. Ndani angayithe ntchito yotereyi? 17Kusiyana ndi ena ambiri, ife sitilalikira Mawu a Mulungu kuti tipeza phindu. Mʼmalo mwake, ife mwa Khristu timayankhula pamaso pa Mulungu moona mtima, monga anthu otumidwa ndi Mulungu.

Chinese Contemporary Bible (Traditional)

哥林多後書 2:1-17

愛之深責之切

1我已經決定了,下次到你們那裡時不再使大家憂傷。 2如果我使你們憂傷,那麼除了因我而憂傷的你們,還有誰能使我喜樂呢? 3我曾為這事寫信給你們,免得我到你們那裡時,那些本該使我喜樂的人反而使我憂傷。我也深信你們會以我的喜樂為你們的喜樂。 4我萬分難過、淚流滿面地給你們寫了前一封信,並非要使你們憂傷,而是要你們明白我是多麼疼愛你們。

要饒恕犯罪的人

5那個令人痛心的人與其說使我憂傷,倒不如說使你們大家都有幾分憂傷。我只說幾分憂傷,是怕說得太重,他受不了。 6這樣的人受了眾人的譴責也就夠了。 7你們現在要饒恕他、安慰他,免得他憂傷過度而一蹶不振。 8我勸你們要讓他確實知道你們仍然愛他。 9為此,我也曾寫信給你們,想知道你們是否凡事順服。 10你們饒恕誰,我也饒恕誰。我若饒恕,是為了你們的緣故在基督面前饒恕的, 11免得撒旦乘虛而入,因為我們並非不知道牠的詭計。

基督的香氣

12我前往特羅亞傳揚基督的福音時,主為我打開了傳福音的大門。 13那時,因為沒有找到提多弟兄,我心裡不安,便辭別眾人來到馬其頓

14感謝上帝!祂常常在基督裡率領我們走在凱旋的行列中,又藉著我們到處散發那因認識基督而有的香氣。 15不論是在得救的人當中還是在滅亡的人當中,對上帝來說,我們都是基督的馨香之氣。 16對滅亡的人而言,這香氣是叫人死亡的香氣;對得救的人來說,這香氣卻是叫人得生命的香氣。誰能擔當這樣的重任呢? 17我們並不像許多人為了謀利而出賣上帝的道。我們是上帝差遣的,在上帝面前靠著基督誠誠實實地講道。