2 Akorinto 13 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Akorinto 13:1-14

Mawu Otsiriza ndi Ochenjeza

1Uwu ndi ulendo wachitatu ndikubwera kudzakuyenderani. “Nkhani itsimikizike ndi umboni wa anthu awiri kapena atatu.” 2Ndinakuchenjezani kale pamene ndinali nanu ulendo wachiwiri uja. Tsopano ndikubwereza ndisanafike. Ndikabweranso sindidzachitira chifundo amene anachimwa poyamba paja kapena wina aliyense amene anachimwa, 3popeza mufuna chitsimikizo chakuti Khristu akuyankhula kudzera mwa ine. Iye siwofowoka pofuna kuchita nanu koma ndi wamphamvu pakati panu. 4Pofuna kutsimikizira, anapachikidwa ali wofowoka koma ali ndi moyo mwamphamvu ya Mulungu. Chomwechonso, ife ndife ofowoka mwa Iye, koma tidzakhala ndi moyo pamodzi naye ndi mphamvu ya Mulungu, potumikira pakati panu.

5Tadzisanthulani nokha kuti muone ngati muli mʼchikhulupiriro; dziyeseni nokha. Kodi simuzindikira kuti Khristu Yesu ali mwa inu, ngati si choncho mwalephera mayesowa? 6Ndipo ndikhulupirira kuti mudzazindikira kuti ife sitinalephere mayesowo. 7Tsopano tikupemphera kwa Mulungu kuti musadzachite kanthu kena kalikonse kolakwa. Osati chifukwa choti anthu aone kuti ife tapambana mayesowo koma kuti mudzachite zokhoza ngakhale anthu atamationa ngati olephera. 8Pakuti sitingachite chilichonse chotsutsana ndi choonadi, koma chokhacho chovomerezana ndi choonadi. 9Ife timasangalala kuti pamene tafowoka, inu muli amphamvu; ndipo pemphero lathu ndi lakuti mukhale angwiro. 10Nʼchifukwa chake ndimalemba zinthu zoterezi pamene ndili kutali, kuti ndikabwera ndisadzagwiritse ntchito ulamuliro wanga mokalipa, uwu ndi ulamuliro umene Ambuye anandipatsa kuti ndikukuzeni inu osati kukuwonongani.

Malonje Otsiriza

11Potsiriza abale, ndikuti tsalani bwino. Yesetsani kukhala angwiro, mvetsetsani pempho langa, khalani a mtima umodzi, khalani mwamtendere. Ndipo Mulungu wachikondi ndi mtendere adzakhala nanu.

12Lonjeranani ndi mpsopsono wachiyero. 13Anthu onse a Mulungu akupereka moni.

14Chisomo cha Ambuye Yesu Khristu, ndi chikondi cha Mulungu, ndi chiyanjano cha Mzimu Woyera zikhale ndi inu nonse.