2 Akorinto 12 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Akorinto 12:1-21

Masomphenya a Paulo ndi Minga ya Mʼthupi Mwake

1Ndiyenera kupitiriza kudzitamandira. Ngakhale palibe choti ndipindule, ndipitiriza kufotokoza za masomphenya ndi mavumbulutso ochokera kwa Ambuye. 2Ndikudziwa munthu mwa Khristu amene zaka khumi ndi zinayi zapitazo anatengedwa kupita kumwamba kwachitatu. Sindikudziwa ngati zinachitika ali mʼthupi kapena ayi, zimenezo akudziwa ndi Mulungu. 3Ndipo ndikumudziwa munthu ameneyu. Sindikudziwa ngati zinachitika mʼthupi kapena ayi, zimenezo akudziwa ndi Mulungu. 4Munthuyu anatengedwa kupita ku paradizo. Ndipo anamva zinthu zosatheka kuneneka, zinthu zimene munthu saloledwa kunena. 5Ndidzatamanda za munthu ngati ameneyu, koma sindidzadzitamandira ine mwini kupatula za kufowoka kwanga. 6Ngakhale nditafuna kudzitamandira, sindingakhale chitsiru, chifukwa ndikunena zoona. Koma ndimapewa kuti pasapezeke munthu wondiganizira moposera chimene ndili chifukwa cha zimene ndimachita kapena kuyankhula, 7kapena chifukwa cha mavumbulutso aakulu kuposa awa. Choncho, kuti ndisadzitukumule, ndinayikidwa minga mʼthupi langa, wamthenga wa Satana, kuti adzindizunza. 8Katatu konse ndinapempha Ambuye kuti andichotsere. 9Koma anandiwuza kuti, “Chisomo changa ndi chokukwanira, pakuti mphamvu zanga zimaoneka kwathunthu mwa munthu wofowoka.” Choncho ndidzadzitamandira mokondwera chifukwa cha zofowoka zanga, kuti mʼkutero mphamvu ya Khristu ikhale pa ine. 10Tsono, chifukwa cha Khristu, ndimakondwera pamene ndili wofowoka, pamene akundinyoza, pamene ndikumva zowawa, ndi pamene akundizunza ndi kundisautsa. Pakuti pamene ndili wofowoka ndiye kuti ndili wamphamvu.

Paulo Akhudzidwa ndi Akorinto

11Ndadzisandutsa wopusa, koma inu mwandichititsa zimenezi. Ndinu amene munayenera kundichitira umboni. Ngakhale kuti sindine kanthu, koma sindine wochepetsetsa kwa “atumwi apamwamba” aja. 12Ndinapirira pokuonetserani zizindikiro za mtumwi weniweni, pochita pakati panu zizindikiro, zodabwitsa ndi ntchito zamphamvu. 13Kodi inu munaoneka ochepa motani ku mipingo ina, kupatula kuti sindinali cholemetsa kwa inu? Mundikhululukire cholakwa chimenechi!

14Ndakonzeka tsopano kudzakuyenderani kachitatu, ndipo sindidzakhala cholemetsa kwa inu chifukwa ndikungofuna inuyo osati zinthu zanu. Pakuti ana sasamalira makolo koma makolo ndiwo asamalira ana. 15Motero ndidzakondwera kukupatsani zanga zonse zimene ndili nazo ndi kudziperekanso ine mwini chifukwa cha inu. Kodi ine ndikamakukondani kwambiri chotere, inuyo mudzandikonda pangʼono? 16Ena mwa inu amavomereza kuti sindinali cholemetsa. Komabe ena amaganiza kuti ndine wochenjera, ndipo ndinakuchenjererani. 17Kodi ndinakudyerani masuku pamutu kudzera mwa wina aliyense amene ndinamutumiza kwa inu? 18Ndinamupempha Tito kuti abwere kwanuko ndipo ndinamutumiza pamodzi ndi mʼbale wathu. Kodi kapena Tito anakudyerani masuku pamutu? Kodi iye ndi ine sitinachite zinthu mofanana ndi Mzimu mmodzi yemweyo?

19Kodi mukuyesa kuti nthawi yonseyi takhala tikudzitchinjiriza tokha? Takhala tikuyankhula pamaso pa Mulungu monga anthu amene ali mwa Khristu; ndipo abwenzi okondedwa, chilichonse chimene timachita ndi chofuna kukulimbikitsani. 20Pakuti ndikuona kuti pamene ndibwera sindidzakupezani monga mmene ndikufunira kuti muzikhalira, ndipo simungadzandione monga mmene mukufunira kundionera. Ndikuopa kuti pangadzakhale mkangano, nsanje, kupserana mitima, kugawikana, ugogodi, miseche, kudzitukumula ndi chisokonezo. 21Ndikuopa kuti pamene ndidzabwerenso, Mulungu adzandichepetsa pamaso panu, ndipo ndidzamva chisoni ndi ambiri amene anachimwa kale ndipo sanalape zonyansa, zachigololo ndi zilakolako zoyipa zimene anachita.