2 Akorinto 11 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Akorinto 11:1-33

Paulo ndi Atumwi Onyenga

1Ndikukhulupirira kuti mupirira nako pangʼono kupusa kwanga. Chonde tandipirirani! 2Nsanje imene ndimakuchitirani ndi yofanana ndi ya Mulungu. Ndinakulonjezani mwamuna mmodzi yekha, mwamunayo ndiye Khristu, kuti ndidzakuperekeni inuyo kwa Iyeyo monga namwali wangwiro. 3Koma ndikuopa kuti monga Hava ananyengedwa ndi kuchenjera kwa njoka, mitima yanunso ingasocheretsedwe kuleka nʼkudzipereka moona mtima ndi modzipereka kwenikweni kwa Khristu. 4Pakuti ngati wina abwera kwa inu nalalikira Yesu wina wosiyana ndi Yesu amene tinamulalikira, kapena ngati mulandira mzimu wina wosiyana ndi Mzimu amene munalandira, kapena uthenga wabwino wina wosiyana ndi umene munawuvomereza, inuyo mumangolandira mosavuta.

5Komatu sindikuganiza kuti ndine wotsika kwambiri kwa “atumwi apamwamba.” 6Mwina ndikhoza kukhala wosaphunzitsidwa kayankhulidwe, koma ndili ndi chidziwitso. Izi tinakufotokozerani momveka bwinobwino. 7Kodi linali tchimo kwa ine kudzichepetsa nʼcholinga chakuti ndikukwezeni pamene ndinkalalikira Uthenga Wabwino wa Mulungu kwa inu mwaulere? 8Ndinkalanda mipingo ina pomalandira thandizo kwa iwo kuti ndikutumikireni. 9Ndipo pamene ndinali pakati panu, nditasowa kanthu, sindinalemetse munthu aliyense, pakuti abale ena amene anachokera ku Makedoniya anandipatsa zonse zimene ndinkazisowa. Ndayesetsa kuti ndisakhale cholemetsa kwa inu mʼnjira ina iliyonse, ndipo ndidzapitiriza kutero. 10Kunena moona mtima molingana ndi chilungamo cha Khristu chimene chili mwa ine, palibe amene angandiletse kudzitamandira mʼzigawo za ku Akaya. 11Nʼchifukwa chiyani ndikutero? Kodi nʼchifukwa choti sindikukondani? Mulungu akudziwa kuti ndimakukondani!

12Ndipo ndipitiriza kuchita zomwe ndikuchitazi nʼcholinga chakuti ndisapereke mpata kwa amene akufuna kupezera mwayi woti afanane nafe pa zinthu zimene iwowo amadzitamandira. 13Pakuti anthu oterewa ndi atumwi onama, antchito achinyengo, odzizimbayitsa ngati atumwi a Khristu. 14Sizododometsa zimenezi, pakuti Satana mwini amadzizimbayitsa kuoneka ngati mngelo wowunikira anthu. 15Nʼzosadabwitsa tsono ngati atumiki ake akudzizimbayitsa ngati otumikira chilungamo. Matsiriziro awo adzalandira zoyenerana ndi ntchito zawo.

Paulo Anyadira Mazunzo Ake

16Ndibwereze kunena kuti, wina aliyense asandiyese chitsiru. Koma ngati mutero, mundilandire monga mmene mukhoza kulandirira chitsiru, kuti ndinyadirepo pangʼono. 17Kudzinyadira kwangaku, sindikuyankhula monga mmene Ambuye akufunira koma ngati chitsiru. 18Popeza ambiri akudzitama monga dziko lapansi limachitira, inenso ndidzitamanso. 19Inu mumalolera kukhala ndi zitsiru mokondwera chifukwa mumati ndinu anzeru! 20Kunena zoona mumangololera aliyense; amene amakusandutsani akapolo, kapena amene amakudyerani masuku pamutu, kapena amene amakupezererani, kapena amene amadzitukumula, kapena amene amakumenyani khofi. 21Ndikuvomera mwamanyazi kuti ife sitinali olimba mtima kuti nʼkuchita zinthu zimenezi.

Ndikuyankhula ngati chitsiru kuti chimene wina aliyense akhoza kudzitama nacho, Inenso ndikhoza kudzitama nachonso. 22Kodi iwo ndi Ahebri? Inenso ndine Mhebri. Kodi iwo ndi Aisraeli? Inenso ndine Mwisraeli. Kodi iwo ndi zidzukulu za Abrahamu? Inenso ndine mdzukulu wa Abrahamu. 23Kodi iwo ndi atumiki a Khristu? Ndikuyankhula ngati wamisala. Ine ndine woposa iwowo. Ndagwira ntchito kwambiri kupambana iwo, ndakhala ndikuyikidwa mʼndende kawirikawiri, ndakwapulidwapo kwambiri, kawirikawiri ndinali pafupi kufa. 24Andikwapulapo kasanu zikoti zija za Ayuda, makumi anayi kuchotsapo chimodzi. 25Katatu anandimenya ndi ndodo. Kamodzi anandigendapo miyala. Katatu sitima yathu ya panyanja inasweka, ndipo ndinakhala usiku ndi usana ndi kuyandama pa nyanja. 26Ndakhala ndikuyenda maulendo ataliatali. Moyo wanga wakhala ukukumana ndi zoopsa pa mitsinje, zoopsa za achifwamba, zoopsa zochokera kwa abale anga Ayuda, zoopsa zochokera kwa anthu akunja. Ndinakumana ndi zoopsa mʼmizinda, mʼmidzi, pa nyanja, ndi pakati pa abale onyenga. 27Ndakhala ndikugwira ntchito molimbika ndipo kawirikawiri ndakhala ndikuchezera usiku wonse osagona. Ndakhala ndikumva njala ndi ludzu ndipo kawirikawiri ndakhala wopanda chakudya. Ndakhala ndi kuzizidwa ndi wosowa zovala. 28Kuwonjezera pa zonsezi, tsiku ndi tsiku ndimakhala pa chipsinjo cha nkhawa ya mipingo yonse. 29Ndani ali wofowoka, ine wosakhala naye mʼkufowoka kwakeko? Ndani amene mnzake amuchimwitsa, ine wosavutika mu mtima?

30Ngati nʼkoyenera kudzitamandira, ndidzadzitamandira pa zinthu zimene zimaonetsa kufowoka kwanga. 31Mulungu, Atate a Ambuye Yesu, amene tiyenera kumutamanda nthawi zonse, akudziwa kuti sindikunama. 32Ku Damasiko, bwanamkubwa woyimira Mfumu Areta, anayika alonda kuzungulira mzinda wonse kuti andigwire. 33Koma abale anandiyika mʼdengu nanditsitsira pa chipupa kudzera pa zenera la mpandawo, motero ndinapulumuka mʼmanja mwake.