1 Timoteyo 6 – CCL & NRT

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Timoteyo 6:1-21

1Onse amene ali mu ukapolo ayenera kuona ambuye awo ngati oyenera kuwachitira ulemu, kuti anthu anganyoze dzina la Mulungu ndi chiphunzitso chathu. 2Amene ambuye awo ndi okhulupirira, asawapeputse chifukwa ambuye ndi abale mʼchikhulupiriro. Mʼmalo mwake akuyenera kuwatumikira bwino chifukwa ambuye wawo ndi okondedwa monga okhulupirira ndiponso ndi odzipereka kusamalira akapolo awo.

Aphunzitsi Onyenga ndi Kukonda Ndalama

Zinthu izi ukuyenera kuziphunzitsa ndi kuwalamula anthu. 3Ngati wina aphunzitsa zosiyana ndi zimenezi, wosagwirizana ndi malangizo woona a Ambuye athu Yesu Khristu ndi chiphunzitso cholemekeza Mulungu, 4ameneyo ndi wodzitukumula ndipo sakudziwa chilichonse. Iyeyo ali ndi maganizo oyipa, wokonda kusemphana mawu ndi kutsutsana. Zimenezi zimabweretsa nsanje, mikangano, mʼnyozo, kuganizirana zoyipa, 5ndi kulimbana kosatha pakati pa anthu amitima yopotoka amene alandidwa choonadi ndipo amaganiza kuti kulemekeza Mulungu ndi njira yopezera chuma.

6Koma kulemekeza Mulungu kuli ndi phindu lalikulu. 7Pakuti sitinabweretse kanthu mʼdziko lapansi, ndipo sitingatengenso kanthu pochoka mʼdziko lapansi. 8Koma ngati tili ndi chakudya ndi zovala, zimenezi zitikwanire. 9Anthu amene amafuna kulemera amagwa mʼmayesero ndi mu msampha ndi mʼzilakolako zambiri zopusa ndi zoopsa zimene zimagwetsera anthu mʼchitayiko ndi mʼchiwonongeko. 10Pakuti kukonda ndalama ndiye muzu wa zoyipa za mitundu yonse. Anthu ena ofunitsitsa ndalama, asochera ndipo asiya njira yachikhulupiriro ndipo adzitengera zowawitsa zambiri.

Malangizo Otsiriza kwa Timoteyo

11Koma iwe, munthu wa Mulungu, thawa zinthu zonsezi. Tsatira chilungamo, moyo wolemekeza Mulungu, chikhulupiriro, chikondi, kupirira ndi kufatsa. 12Menya nkhondo yabwino yachikhulupiriro. Gwiritsitsa moyo wosatha umene anakuyitanira pamene unavomereza bwino lomwe pamaso pa mboni zambiri. 13Ndikukulamula pamaso pa Mulungu amene amapatsa moyo zinthu zonse, ndiponso pamaso pa Khristu Yesu amene pochitira umboni pamaso pa Pontiyo Pilato, ananena zoona zenizeni. 14Usunge lamuloli mopanda banga ndi cholakwa kufikira Ambuye athu Yesu Khristu ataonekera. 15Pa nthawi yake Mulungu adzamubweretsa kwa ife. Mulungu ndi wodalitsika ndipo Iye yekha ndiye Wolamulira, Mfumu ya mafumu, Mbuye wa ambuye. 16Ndiye yekha wosafa ndipo amakhala mʼkuwala koopsa. Mulungu amene munthu aliyense sanamuone. Kwa Iye kukhale ulemu ndi mphamvu mpaka muyaya. Ameni.

Za Kudalira Chuma

17Anthu onse amene ali ndi chuma uwalamule kuti asanyade kapena kuyika mitima yawo pa chuma chimene nʼchosadalirika. Koma chiyembekezo chawo chikhale mwa Mulungu amene amatipatsa mowolowamanja zonse zotisangalatsa. 18Uwalamule kuti azichita zabwino, kuti azikhala olemera pa ntchito zabwino, owolowamanja ndi okonda kugawana zinthu zawo ndi anzawo. 19Potero adzadziwunjikira chuma chokhalitsa ngati maziko okhazikika a nthawi zakutsogolo, kuti akalandire moyo, umene ndi moyo weniweni.

Mawu Otsiriza

20Timoteyo, samalitsa zimene unapatsidwa. Upewe nkhani zopanda pake zosalemekeza Mulungu ndiponso maganizo otsutsana amene amaganizidwa molakwika kuti ndi nzeru. 21Anthu ena chifukwa chovomereza nzeru zotere, asochera nʼkutaya chikhulupiriro chawo.

Chisomo chikhale nawe.

New Russian Translation

1 Тимофею 6:1-21

1Те, кто находится под игом рабства, пусть относятся со всем уважением к своим хозяевам, чтобы ни имя Бога, ни наше учение не были опорочены. 2Рабы, у которых хозяева христиане, не должны оказывать им меньше уважения на том основании, что они братья. Наоборот, они должны служить еще лучше, потому что те, кому они служат, – верные и любимые братья. Этому ты должен учить людей и к этому их призывать.

Ложное учение и истинное богатство

3Кто учит чему-то другому и не согласен со здравыми наставлениями нашего Господа Иисуса Христа и с учением, соответствующим истинному богопочитанию, 4тот заносчив, но не имеет знания. У него есть лишь нездоровое желание спорить и вести праздные дебаты, что лишь рождает зависть, распри, кощунство, недобрые подозрения 5и постоянные разногласия между людьми с развращенным умом, далекими от истины: для них благочестие стало лишь способом наживы.

6Великое приобретение быть благочестивым и довольным. 7Ведь мы ничего не принесли с собой в этот мир и ничего не можем взять с собой из него. 8Мы должны быть довольны, если у нас есть пропитание и одежда. 9Те же, кто стремится разбогатеть, впадают в искушение и попадают в ловушку множества глупых и опасных желаний, которые погружают людей в пучину несчастья и гибели. 10Любовь к деньгам – это корень всех зол. Есть много людей, которых любовь к деньгам увела от веры и принесла им много страданий.

Наказ Тимофею

11Ты же, человек Божий, беги от этого. Стремись к праведности, благочестию, вере, любви, терпению, кротости. 12Доблестно сражайся за веру, держись вечной жизни, к которой ты призван, ведь ты достойно и открыто говорил о своей вере перед многими свидетелями. 13Я требую от тебя перед Богом, дающим всему жизнь, и перед Христом Иисусом, Который засвидетельствовал пред Понтием Пилатом доброе исповедание: 14верно и безукоризненно исполняй то, что я тебе повелел, вплоть до явления нашего Господа Иисуса Христа, 15которое в свое время откроет блаженный и единый Повелитель, Царь царей и Господь господствующих6:15 См. Втор. 10:17; Пс. 135:3., 16единственный Бессмертный, обитающий в неприступном свете, Которого никто из людей не видел и не может видеть. Ему принадлежит честь и могущество навсегда! Аминь.

17Тех, кто в этой земной жизни богат, предупреждай, чтобы не гордились и не надеялись на свое богатство: оно ненадежно. Пусть лучше надеются на Бога, щедро дающего все необходимое, чтобы мы могли наслаждаться жизнью. 18Требуй от них делать добро и обогащаться добрыми делами, быть щедрыми и охотно делиться с другими своим богатством. 19Таким образом, они соберут себе сокровища, которые станут добрым основанием их будущего, и получат подлинную жизнь.

20Тимофей, храни то, что тебе вверено. Не занимайся безбожным пустословием и спорами о том, что ложно называют знанием. 21Увлекшись этим, некоторые ушли в сторону от веры.

Пусть благодать будет с вами6:21 В нескольких рукописях: «с тобой»..