1 Timoteyo 5 – CCL & KJV

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Timoteyo 5:1-25

Malangizo kwa Amayi Amasiye, Akulu Ampingo ndi Akapolo

1Usadzudzule munthu wachikulire mokalipa, koma umuchenjeze ngati abambo ako. Achinyamata uwatenge ngati abale ako. 2Amayi achikulire uwatenge ngati amayi ako ndipo amayi achitsikana uwatenge ngati alongo ako, nʼkuyera mtima konse.

3Uziwachitira ulemu akazi amasiye amene ali okhaokha. 4Koma ngati mkazi wamasiye ali ndi ana ndi zidzukulu, anawo ayambe aphunzira kukwaniritsa udindo wawo pa banja lawo moopa Mulungu, potero akubweza zabwino kwa makolo awo ndi agogo awo. Pakuti zimenezi ndiye zimakondweretsa Mulungu. 5Mkazi wamasiye amene ali yekha ndi wopanda womuthandiza, ameneyo wayika chiyembekezo chake pa Mulungu, ndipo amapemphera kosalekeza usana ndi usiku kuti Mulungu azimuthandiza. 6Koma mkazi wamasiye amene amangokhalira kuchita zosangalatsa moyo wake, wafa kale ngakhale akanali ndi moyo. 7Pereka malangizo amenewa kwa anthu kuti akhale opanda zolakwa. 8Ngati wina sasamalira abale ake, makamaka a mʼbanja mwake mwenimweni, ameneyo wakana chikhulupiriro ndipo ndi woyipa kuposa wosakhulupirira.

9Mayi wamasiye aliyense amene sanakwanitse zaka 60 zakubadwa, asakhale mʼgulu la akazi amasiye. Akhale woti anakwatiwapo ndi mwamuna wake mmodzi yekha. 10Akhale mayi woti amadziwika bwino pa ntchito zake zabwino monga kulera ana, kusamalira alendo, kusambitsa mapazi a anthu a Mulungu, kuthandiza amene ali pa mavuto ndi kudzipereka pa ntchito zonse zabwino.

11Akazi amasiye achitsikana, usawayike mʼgulu limeneli. Pakuti zilakolako zawo zikayamba kuwavutitsa nʼkuwalekanitsa ndi Khristu, amafuna kukwatiwanso. 12Zikatero amadziweruza okha chifukwa aphwanya lonjezo lawo loyamba. 13Komanso amakhala ndi chizolowezi cha ulesi ndi kumangoyenda khomo ndi khomo. Ndipo sikungokhala aulesi kokha komanso kuchita miseche, kududukira za eni ake, kumangokamba zinthu zosayenera kukamba. 14Kotero, ndikulangiza akazi amasiye achitsikana kuti akwatiwe, akhale ndi ana, asamalire makomo awo ndipo asamupatse mdani mpata wonyoza 15Akazi amasiye ena apatuka kale nʼkumatsatira Satana.

16Ngati mayi aliyense wokhulupirira ali ndi akazi amasiye amene akuwasamalira, apitirizebe kuwasamalira ndipo asalemetse mpingo, kuti mpingo uthandize akazi amasiye amene ali okhaokha.

17Akulu ampingo amene amayangʼanira bwino zochitika za mu mpingo, ndi oyenera ulemu wowirikiza, makamaka amene ntchito yawo ndi kulalikira ndi kuphunzitsa. 18Pakuti Mawu a Mulungu amati, “Musamange ngʼombe pakamwa pamene ikupuntha tirigu,” ndi “Wantchito ngoyenera kulandira malipiro ake.” 19Usamamvere mawu oneneza akulu ampingo pokhapokha patakhala mboni ziwiri kapena zitatu. 20Akulu ampingo amene akuchimwa, uwadzudzule poyera kuti ena aphunzirepo.

21Ndikukulamulira pamaso pa Mulungu, pamaso pa Yesu Khristu ndi pamaso pa angelo osankhika, kuti usunge malangizowa mosachotsera ndipo usachite kalikonse mokondera.

22Usafulumire kusanjika manja munthu, ndipo usavomerezane ndi anthu ena pa machimo. Usunge bwino kuyera mtima kwako.

23Uleke kumangomwa madzi okha, koma uzimwako vinyo pangʼono chifukwa cha vuto lako la mʼmimba ndi kudwala kwako kwa pafupipafupi.

24Anthu ena machimo awo amaonekeratu poyera, amakafika pa mpando wachiweruzo eni akewo asanakafike. Machimo a anthu ena amabwera mʼmbuyo mwawo. 25Momwemonso, ntchito zabwino zimaonekera poyera, ndipo ngakhale zipande kutero, sizingatheke kubisika.

King James Version

1 Timothy 5:1-25

1Rebuke not an elder, but intreat him as a father; and the younger men as brethren; 2The elder women as mothers; the younger as sisters, with all purity. 3Honour widows that are widows indeed. 4But if any widow have children or nephews, let them learn first to shew piety at home, and to requite their parents: for that is good and acceptable before God. 5Now she that is a widow indeed, and desolate, trusteth in God, and continueth in supplications and prayers night and day. 6But she that liveth in pleasure is dead while she liveth. 7And these things give in charge, that they may be blameless. 8But if any provide not for his own, and specially for those of his own house, he hath denied the faith, and is worse than an infidel. 9Let not a widow be taken into the number under threescore years old, having been the wife of one man, 10Well reported of for good works; if she have brought up children, if she have lodged strangers, if she have washed the saints’ feet, if she have relieved the afflicted, if she have diligently followed every good work. 11But the younger widows refuse: for when they have begun to wax wanton against Christ, they will marry; 12Having damnation, because they have cast off their first faith. 13And withal they learn to be idle, wandering about from house to house; and not only idle, but tattlers also and busybodies, speaking things which they ought not. 14I will therefore that the younger women marry, bear children, guide the house, give none occasion to the adversary to speak reproachfully. 15For some are already turned aside after Satan. 16If any man or woman that believeth have widows, let them relieve them, and let not the church be charged; that it may relieve them that are widows indeed. 17Let the elders that rule well be counted worthy of double honour, especially they who labour in the word and doctrine. 18For the scripture saith, Thou shalt not muzzle the ox that treadeth out the corn. And, The labourer is worthy of his reward. 19Against an elder receive not an accusation, but before two or three witnesses. 20Them that sin rebuke before all, that others also may fear. 21I charge thee before God, and the Lord Jesus Christ, and the elect angels, that thou observe these things without preferring one before another, doing nothing by partiality. 22Lay hands suddenly on no man, neither be partaker of other men’s sins: keep thyself pure. 23Drink no longer water, but use a little wine for thy stomach’s sake and thine often infirmities. 24Some men’s sins are open beforehand, going before to judgment; and some men they follow after. 25Likewise also the good works of some are manifest beforehand; and they that are otherwise cannot be hid.