1 Timoteyo 1 – CCL & NIV

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Timoteyo 1:1-20

1Paulo, mtumwi wa Khristu Yesu mwa lamulo la Mulungu, Mpulumutsi wathu ndiponso Khristu Yesu chiyembekezo chathu.

2Kwa Timoteyo mwana wanga weniweni mʼchikhulupiriro.

Chisomo, chifundo ndi mtendere zochokera kwa Mulungu Atate ndi Khristu Yesu Ambuye athu zikhale ndi iwe.

Kutsutsa Aphunzitsi Onyenga

3Monga ndinakupempha pamene ndinkapita ku Makedoniya, khala ku Efeso komweko kuti uletse anthu ena kuphunzitsa ziphunzitso zonyenga, 4kapena kumangoyika mitima pa nthano zopeka ndi kufufuza za mayina a makolo awo. Zinthu zotere zimapititsa mʼtsogolo mikangano mʼmalo mwa ntchito ya Mulungu yomwe ndi ya chikhulupiriro. 5Cholinga cha lamuloli ndi chikondi, chomwe chimachokera mu mtima woyera, chikumbumtima chabwino ndi chikhulupiriro choona. 6Anthu ena anapatuka pa zimenezi ndipo anatsata nkhani zopanda tanthauzo. 7Iwo amafuna kukhala aphunzitsi amalamulo, koma sadziwa zimene akunena, kapena zimene akufuna kutsimikiza.

8Tikudziwa kuti Malamulo ndi abwino ngati munthu awagwiritsa ntchito bwino. 9Tikudziwanso kuti Malamulo sakhazikitsidwa chifukwa cha anthu olungama, koma ophwanya lamulo ndi owukira, osaopa Mulungu ndi ochimwa, wopanda chiyero ndi osapembedza; amene amapha abambo awo ndi amayi awo, kapena anthu ena. 10Malamulo amayikidwa chifukwa cha anthu achigololo ndi ochita zadama ndi amuna anzawo, anthu ogulitsa akapolo, abodza ndi olumbira zabodza, ndi ochita chilichonse chotsutsana ndi chiphunzitso choona. 11Chiphunzitso chimene chimagwirizana ndi Uthenga Wabwino wonena za ulemerero wa Mulungu wodala, umene Iye mwini anandisungitsa.

Chisomo cha Ambuye kwa Paulo

12Ndikuthokoza Khristu Yesu Ambuye athu, amene anandipatsa mphamvu pa ntchitoyi. Iye ananditenga kukhala wokhulupirira, nandipatsa ntchito mu utumiki wake. 13Ngakhale kuti kale ndinali wachipongwe, wozunza ndi wankhanza, anandichitira chifundo chifukwa ndinkachita mwaumbuli ndi mopanda chikhulupiriro. 14Chisomo cha Ambuye athu chinatsanulidwa pa ine mochuluka, pamodzi ndi chikhulupiriro ndi chikondi zimene zili mwa Khristu Yesu.

15Mawu odalirika ndi woyenera kuwavomereza kwathunthu ndi awa: Yesu Khristu anabwera pa dziko lapansi kudzapulumutsa ochimwa, ndipo mwa iwowo ine ndiye wochimwitsitsa. 16Ndipo pa chifukwa chimenechi, Mulungu anandichitira chifundo, kuti mwa ine, wochimwitsitsa, Khristu Yesu aonetse kuleza mtima kwake konse kuti ndikhale chitsanzo cha omwe angathe kumukhulupirira ndi kulandira moyo wosatha. 17Tsopano kwa Mfumu yamuyaya, yosafa, yosaoneka, amene Iye yekha ndiye Mulungu, kukhale ulemu ndi ulemerero mpaka muyaya. Ameni.

Ntchito ya Timoteyo

18Mwana wanga Timoteyo, ndikukupatsa langizo ili molingana ndi maulosi amene aneneri ananena za iwe. Pamene ukumbukira mawu amenewa udzatha kumenya bwino nkhondo 19utagwiritsitsa chikhulupiriro ndi chikumbumtima chabwino. Ena anazikana zimenezi motero chikhulupiriro chawo chinawonongeka. 20Ena mwa amenewa ndi Humenayo ndi Alekisandro, amene ndinawapereka kwa Satana kuti aphunzire kusachita chipongwe Mulungu.

New International Version

1 Timothy 1:1-20

1Paul, an apostle of Christ Jesus by the command of God our Savior and of Christ Jesus our hope,

2To Timothy my true son in the faith:

Grace, mercy and peace from God the Father and Christ Jesus our Lord.

Timothy Charged to Oppose False Teachers

3As I urged you when I went into Macedonia, stay there in Ephesus so that you may command certain people not to teach false doctrines any longer 4or to devote themselves to myths and endless genealogies. Such things promote controversial speculations rather than advancing God’s work—which is by faith. 5The goal of this command is love, which comes from a pure heart and a good conscience and a sincere faith. 6Some have departed from these and have turned to meaningless talk. 7They want to be teachers of the law, but they do not know what they are talking about or what they so confidently affirm.

8We know that the law is good if one uses it properly. 9We also know that the law is made not for the righteous but for lawbreakers and rebels, the ungodly and sinful, the unholy and irreligious, for those who kill their fathers or mothers, for murderers, 10for the sexually immoral, for those practicing homosexuality, for slave traders and liars and perjurers—and for whatever else is contrary to the sound doctrine 11that conforms to the gospel concerning the glory of the blessed God, which he entrusted to me.

The Lord’s Grace to Paul

12I thank Christ Jesus our Lord, who has given me strength, that he considered me trustworthy, appointing me to his service. 13Even though I was once a blasphemer and a persecutor and a violent man, I was shown mercy because I acted in ignorance and unbelief. 14The grace of our Lord was poured out on me abundantly, along with the faith and love that are in Christ Jesus.

15Here is a trustworthy saying that deserves full acceptance: Christ Jesus came into the world to save sinners—of whom I am the worst. 16But for that very reason I was shown mercy so that in me, the worst of sinners, Christ Jesus might display his immense patience as an example for those who would believe in him and receive eternal life. 17Now to the King eternal, immortal, invisible, the only God, be honor and glory for ever and ever. Amen.

The Charge to Timothy Renewed

18Timothy, my son, I am giving you this command in keeping with the prophecies once made about you, so that by recalling them you may fight the battle well, 19holding on to faith and a good conscience, which some have rejected and so have suffered shipwreck with regard to the faith. 20Among them are Hymenaeus and Alexander, whom I have handed over to Satan to be taught not to blaspheme.