1 Samueli 8 – CCL & CCB

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Samueli 8:1-22

Aisraeli Apempha kuti Akhale ndi Mfumu

1Samueli atakalamba anasankha ana ake kuti akhale oweruza Aisraeli. 2Mwana wake woyamba anali Yoweli, wachiwiri anali Abiya, ndipo ankaweruza ku Beeriseba. 3Koma ana akewo sanatengere makhalidwe ake abwino. Iwo ankapotokera ku zoyipa namatsata phindu mwachinyengo. Ankalandira ziphuphu ndi kumaweruza mwachinyengo.

4Tsono akuluakulu onse a Israeli anasonkhana pamodzi ndipo anabwera kwa Samueli ku Rama. 5Iwo anati kwa iye “Taonani, inu mwakula tsopano ndipo ana anu sakutsata makhalidwe anu abwino. Tsono mutipatse mfumu kuti izitilamulira, monga momwe ikuchitira mitundu ina yonseyi.”

6Koma mawu oti, “Mutipatse mfumu kuti izitilamulira,” sanakondweretse Samueli. Choncho anapemphera kwa Yehova. 7Yehova anamuyankha nati, “Mvera zonse zimene anthuwa akukuwuza. Si ndiwe amene akumukana, koma akukana Ine kuti ndikhale mfumu yawo. 8Kuyambira tsiku limene ndinawatulutsa mʼdziko la Igupto mpaka lero zochita zawo zakhala zondikana Ine nʼkumatumikira milungu ina. Tsopano akukukananso iwe. 9Tsono amvere zimene akunena, koma uwachenjeze kwambiri ndipo uwawuzitse za khalidwe la mfumu imene idzawalamulire.”

10Samueli anawawuza anthu amene amamupempha mfumu aja mawu onse a Yehova. 11Iye anati, “Zimene mfumu imene idzakulamulireniyo idzachite ndi izi: Izidzatenga ana anu aamuna kuti akhale ankhondo ake; ena pa magaleta ake, ena pa akavalo ake ndipo ena othamanga patsogolo pa magaleta akewo. 12Ena adzawayika kukhala olamulira asilikali 1,000, ena olamulira asilikali makumi asanu, ndi ena otipula minda yake, ndi kukolola ndiponso ena adzakhala osula zida zankhondo ndi zida za magaleta ake. 13Iyo idzatenga ana anu akazi kuti akhale oyenga mafuta onunkhira, ophika chakudya ndi kupanga buledi. 14Idzatenga minda yanu yabwino ya mpesa ndi ya mitengo ya olivi ndipo adzayipereka kwa antchito ake. 15Idzatenga gawo lakhumi la tirigu wanu ndi mphesa zanu ndi kupereka kwa nduna zake ndi akapitawo ake. 16Mfumuyo idzatenga antchito anu aamuna ndi aakazi. Idzatenganso ngʼombe zanu zabwino ndi abulu anu nʼkumazingwiritsa ntchito. 17Iyo idzatenga gawo lakhumi la zoweta zanu, ndipo inu eni mudzakhala akapolo ake. 18Nthawi imeneyo ikadzafika inu mudzalira momvetsa chisoni chifukwa cha mfumu imene mwadzisankhira, koma Yehova sadzakuyankhani.”

19Koma anthu anakana kumumvera Samueli. Iwo anati, “Ayi! Ife tikufuna mfumu yotilamulira. 20Kotero ifenso tidzakhala ngati mayiko ena. Mfumu yathu idzatiweruza ndiponso idzatuluka nafe kutitsogolera kukamenya nkhondo.”

21Samueli atamva zonse zimene anthuwo ananena, iye anakazifotokozanso kwa Yehova. 22Yehova anamuyankha nati, “Amvere zimene akunena ndipo apatse mfumu.”

Ndipo Samueli anati kwa Aisraeli aja, “Bwererani aliyense kwawo.”

Chinese Contemporary Bible (Simplified)

撒母耳记上 8:1-22

以色列人要求立王

1撒母耳在年老的时候立了他的儿子做以色列人的士师。 2他的长子是约珥,次子是亚比亚,他们在别示巴做士师。 3然而,他们没有效法自己的父亲,而是爱慕不义之财,贪赃枉法。

4于是,以色列的长老一起到拉玛去见撒母耳5说:“你年纪大了,你的儿子不效法你。现在求你为我们立一个王治理我们,像其他国家一样。” 6撒母耳听到他们要求立一个王治理他们,心中不悦,就向耶和华祷告。 7耶和华对撒母耳说:“你照他们所说的去做吧,因为他们不是拒绝你,而是拒绝我做他们的王。 8自从我把他们从埃及领出来以后,他们就常常背弃我,去供奉其他神明。现在,他们也这样对待你。 9你就照他们所求的去做吧!但你要警告他们,让他们知道将来王会怎样管辖他们。”

10撒母耳就把耶和华的话转告给那些请求他立王的民众,说: 11“将来管辖你们的王会征用你们的儿子做他的战车兵、骑兵,要他们跑在他的战车前面。 12他会派一些人做千夫长、五十夫长,一些人为他耕种田地、收割庄稼,一些人制造兵器和战车的装备。 13他会把你们的女儿带走,要她们给他造香膏、煮饭和烤饼。 14他会夺去你们最好的田地、葡萄园和橄榄园,送给他的臣仆。 15他会从你们的粮食和葡萄园的出产中收取十分之一,送给他的官员和臣仆。 16他会征用你们的仆婢及最好的牛8:16 ”有古卷作“青年”。和驴来为他效劳。 17他会拿去你们羊群的十分之一,并让你们做他的奴仆。 18将来你们会因所选之王的压迫而呼求耶和华,耶和华却不会垂听你们。”

19民众却不肯听从撒母耳的话。他们说:“不,我们想要一个王治理我们, 20这样我们就会像其他国家一样,有王来统治我们,率领我们,为我们作战。” 21撒母耳把这些人的话一五一十地告诉了耶和华。 22耶和华对撒母耳说:“照他们说的去为他们立一个王吧。”于是,撒母耳以色列人说:“你们各人回自己的城去吧。”