1 Samueli 7 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Samueli 7:1-17

1Choncho anthu a ku Kiriati-Yearimu anabwera ndi kudzatenga Bokosi la Yehova. Iwo anapita nalo ku nyumba ya Abinadabu ya ku phiri ndipo anapatula Eliezara mwana wake kuti aziyangʼanira Bokosi la Yehovalo.

Samueli Agonjetsa Afilisti ku Mizipa

2Zaka makumi awiri zinapita kuyambira pamene Bokosi la Yehova linakhala ku Kiriati-Yearimu, ndipo anthu a Israeli onse analira kupempha Yehova kuti awathandize. 3Ndipo Samueli anati kwa nyumba yonse ya Israeli, “Ngati mukubwerera kwa Yehova ndi mtima wanu wonse, muchotse milungu yachilendo ndi Asiteroti pakati panu ndipo mitima yanu ikhazikike pa Yehova ndi kutumikira Iye yekha. Mukatero Iye adzakupulumutsani mʼmanja mwa Afilisti.” 4Choncho Aisraeli anachotsa milungu yawo ya Baala ndi Asitoreti ndi kutumikira Yehova yekha.

5Kenaka Samueli anati, “Sonkhanitsani Aisraeli onse ku Mizipa ndipo ine ndidzakupemphererani kwa Yehova.” 6Choncho anasonkhana ku Mizipa, ndipo anatunga madzi ndi kuwathira pansi pamaso pa Yehova. Pa tsiku limenelo anasala kudya namanena kuti, “Ife tachimwira Yehova.” Ndipo Samueli anali mtsogoleri wa Israeli ku Mizipa.

7Afilisti anamva kuti Aisraeli asonkhana ku Mizipa, choncho akalonga awo anabwera kudzawathira nkhondo. Ndipo Aisraeli atamva anachita mantha chifukwa cha Afilisti. 8Choncho anati kwa Samueli, “Musasiye kutipempherera kwa Yehova Mulungu wathu, kuti atipulumutse mʼdzanja la Afilistiwa.” 9Ndipo Samueli anatenga mwana wankhosa wamkazi woyamwa ndi kumupereka monga nsembe yopsereza kwa Yehova. Iye anapemphera kwa Yehova mʼmalo mwa Aisraeli, ndipo Yehova anamuyankha.

10Samueli akupereka nsembe yopsereza, Afilisti anayandikira kuti ayambe kuwathira nkhondo Aisraeli. Koma tsiku limenelo Yehova anawaopseza Afilisti aja ndi mawu aakulu ngati bingu. Choncho anasokonezeka motero kuti Aisraeli anawagonjetsa. 11Aisraeli anatuluka ku Mizipa kuthamangitsa Afilisti aja nʼkumawapha mʼnjira yonse mpaka kumunsi kwa Beti-Kari.

12Kenaka Samueli anatenga mwala nawuyika pakati pa Mizipa ndi Seni. Iye anawutcha Ebenezeri, popeza anati, “Yehova watithandiza mpaka pano.” 13Kotero Afilisti anagonjetsedwa ndipo sanadzalowenso mʼdziko la Israeli.

Yehova analimbana ndi Afilisti masiku onse a Samueli. 14Mizinda yonse imene Afilisti analanda kuchokera ku Ekroni mpaka ku Gati inabwezedwa kwa Aisraeli. Choncho Aisraeli anapulumutsa dziko lawo. Ndipo panalinso mtendere pakati pa Aisraeli ndi Aamori.

15Samueli anatsogolera Aisraeli moyo wake wonse. 16Chaka ndi chaka Samueli ankakonza ulendo wozungulira kuchokera ku Beteli mpaka ku Giligala ndi Mizipa, kuweruza milandu ya Aisraeli mʼmadera onsewa. 17Koma pambuyo pake ankabwerera ku Rama, kumene kunali nyumba yake. Ankaweruza Aisraeli kumeneko. Ndipo iye anamanga guwa lansembe la Yehova kumeneko.