1 Samueli 28 – CCL & CCBT

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Samueli 28:1-25

Sauli ndi Mfiti ya ku Endori

1Mʼmasiku amenewo Afilisti anasonkhanitsa ankhondo awo kuti akamenyane ndi Aisraeli. Akisi anawuza Davide kuti, “Udziwe kuti iwe pamodzi ndi anthu ako mudzapita nane ku nkhondo.”

2Davide anayankha kuti, “Tsono inu mudzaona zimene mtumiki wanune ndingachite.”

Akisi anayankha kuti, “Chabwino ine ndidzakuyika iwe kukhala mlonda wanga moyo wako wonse.”

3Nthawi imeneyi nʼkuti Samueli atamwalira, ndipo Aisraeli onse anamulira namuyika mʼmanda ku mzinda wake wa Rama. Sauli anali atachotsa mʼdzikomo anthu owombeza mawula ndi woyankhula ndi mizimu ya anthu akufa.

4Tsono Afilisti anasonkhana nabwera kudzamanga misasa yawo ku Sunemu. Nayenso Sauli anasonkhanitsa Aisraeli onse ndi kumanga misasa yawo ku Gilibowa. 5Sauli ataona gulu lankhondo la Afilisti anaopa ndipo ananjenjemera kwambiri. 6Choncho Sauli anafunsa nzeru kwa Yehova koma Yehova sanamuyankhe ngakhale kudzera mʼmaloto, kapena mwa Urimu ngakhalenso kudzera mwa aneneri. 7Kenaka Sauli anawuza nduna zake kuti, “Mundipezere mkazi amene amawombeza mawula kuti ndipite ndikafunse kwa iye.”

Nduna zakezo zinamuyankha kuti, “Alipo mkazi woyankhula ndi mizimu ya anthu akufa ku Endori.”

8Kotero Sauli anadzizimbayitsa navala zovala zachilendo. Tsono iye pamodzi ndi anthu awiri anapita nakafika kwa mkazi uja usiku, ndipo anamupempha kuti, “Chonde ndifunsireni nzeru kwa mizimu ya anthu akufa. Koma makamaka munditulutsire mzimu wa amene ndimutchule.”

9Koma mkaziyo anayankha kuti, “Ndithu inu mukudziwa chimene Sauli anachita. Paja iye anachotsa mʼdziko muno anthu onse owombeza ndi woyankhula ndi mizimu ya anthu akufa. Chifukwa chiyani mukutchera moyo wanga msampha kuti ndiphedwe?”

10Koma Sauli analonjeza mkaziyo molumbira nati, “Pali Yehova wamoyo, iweyo sudzalangidwa chifukwa cha zimenezi.”

11Kenaka mkaziyo anafunsa, “Ndikuyitanireni yani?”

Iye anati, “Undiyitanire Samueli.”

12Pamene mkaziyo anaona Samueli anakuwa kwambiri, nawuza Sauli kuti, “Nʼchifukwa chiyani inu mwandipusitsa? Inu ndinu Sauli!”

13Mfumuyo inamuwuza kuti, “Usaope. Kodi ukuona chiyani?”

Mkaziyo anayankha kuti, “Ndikuona mzimu ukutuluka pansi.”

14Sauli anafunsa, “Kodi mzimuwo ukuoneka motani?”

Mkaziyo anayankha kuti, “Amene akutuluka ndi munthu wokalamba ndipo wavala mkanjo.”

Apo Sauli anadziwa kuti anali Samueli ndipo anawerama nagunditsa nkhope yake pansi.

15Samueli anafunsa Sauli kuti, “Nʼchifukwa chiyani wandivutitsa pondiyitana kuti ndibwere kuno?”

Sauli anayankha kuti, “Ine ndavutika kwambiri mʼmaloto. Afilisti akumenyana nane, ndipo Mulungu wandifulatira. Iye sakundiyankhulanso, ngakhale kudzera mwa aneneri kapena maloto. Choncho ndakuyitanani kuti mundiwuze zoti ndichite.”

16Samueli anati, “Nʼchifukwa chiyani ukundifunsa ine, pakuti tsopano Yehova wakufulatira ndipo wasanduka mdani wako? 17Yehova wakuchita zimene ananeneratu kudzera mwa ine. Yehova wachotsa ufumu mʼmanja mwako ndipo waupereka kwa mnansi wako, kwa Davide. 18Yehova wachita zimenezi lero chifukwa sunamvere mawu ake ndipo sunawawonongeretu Aamaleki. 19Yehova adzapereka ndithu iweyo pamodzi ndi Aisraeli kwa Afilisti. Ndipo mmawa iweyo ndi ana ako mudzakhala ndi ine kuno. Ndithu Yehova adzapereka gulu lankhondo la Aisraeli kwa Afilisti.”

20Nthawi yomweyo Sauli anagwa pansi atadzazidwa ndi mantha chifukwa cha mawu a Samueli. Analibenso mphamvu, pakuti sanadye tsiku lonse.

21Mkazi uja tsono anasendera kufupi ndi Sauli, ndipo ataona kuti Sauli akuchita mantha, anamuwuza kuti, “Taonani, mdzakazi wanune ndakumverani. Ndayika moyo wanga pa chiswe ndipo ndamvera zimene munandiwuza. 22Tsono inunso mumvere mawu a mdzakazi wanune. Mundilole kuti ndikupatseni ka buledi pangʼono kuti mukhale ndi mphamvu zoyendera pa ulendo wanu.”

23Iye anakana ndipo anati, “Ayi, ine sindidya.”

Koma nduna zake pamodzi ndi mkaziyo anamuwumiriza, ndipo anawamvera. Choncho anadzuka pansi nakhala pa bedi.

24Mkaziyo anali ndi mwana wangʼombe wonenepa ndipo anamupha mwachangu. Anatenga ufa nawukanyanga ndipo anaphika buledi wopanda yisiti. 25Tsono anapereka bulediyo kwa Sauli ndi nduna zake ndipo anadya. Pambuyo pake ananyamuka kupita kwawo usiku womwewo.

Chinese Contemporary Bible (Traditional)

撒母耳記上 28:1-25

掃羅求問巫婆

1非利士人召集大軍與以色列人交戰。亞吉大衛說:「你應該明白,你和部下要隨我一起出戰。」 2大衛答道:「僕人願意效勞。」亞吉說:「很好!你就終生做我的護衛吧。」 3那時撒母耳已經死了,以色列舉國都為他哀悼,把他葬在他的家鄉拉瑪。當時,掃羅把所有占卜和行巫術的都逐出了以色列4非利士人集合起來,在書念紮營,掃羅率領以色列軍隊在基利波紮營。 5掃羅看見非利士軍隊聲勢浩大,感到膽戰心驚, 6就求問耶和華,但耶和華沒有藉著夢、烏陵或先知回答他。 7於是,掃羅命令臣僕找一個巫婆來,好求問她。臣僕在隱·多珥找到一個巫婆。

8掃羅喬裝打扮,由兩個人陪同乘夜趕到那婦人家裡,說:「請你用法術把我要求問的亡靈招上來吧。」 9婦人對他說:「你知道掃羅剷除了國內占卜的和行巫術的,你為何來陷害我,置我於死地?」 10掃羅憑耶和華向婦人起誓,說:「我憑永活的耶和華起誓,你必不會因為此事而受到懲罰。」 11婦人問道:「你想讓我招誰上來呢?」掃羅答道:「招撒母耳上來。」 12婦人看見了撒母耳,就驚叫起來,對掃羅說:「你是掃羅,你為什麼騙我呢?」 13掃羅對她說:「不用害怕,你看見什麼了?」婦人說:「我看見一個靈從地裡上來。」 14掃羅說:「他是什麼模樣?」婦人說:「是個身披長袍的老人。」掃羅知道是撒母耳,便俯伏在地,向他下拜。 15撒母耳掃羅說:「你為什麼打擾我,招我上來呢?」掃羅答道:「我深陷困境,非利士人與我們交戰,上帝也撇棄了我,不再藉著先知或夢來回答我。因此,我只好招你上來,好告訴我該怎麼辦。」 16撒母耳說:「既然耶和華已經離棄了你,與你為敵,你為什麼還來問我? 17耶和華應驗了祂藉著我所說的預言,祂已把你的國權奪去,交給了你的同胞大衛18耶和華今天這樣對待你,是因為你沒有聽從祂的吩咐,沒有把祂憎惡的亞瑪力人滅絕。 19耶和華必把你和以色列人交在非利士人手裡,明天你和你的兒子們必跟我在一起了。耶和華必把以色列的軍隊交在非利士人手裡。」

20掃羅聽了撒母耳的話,頓時嚇得渾身僵直,倒在地上,一天一夜沒有進食,毫無力氣。 21婦人到掃羅跟前,看見他驚恐萬分,就對他說:「婢女冒著生命危險服從你的命令,照你的吩咐做了。 22現在,請你聽婢女的話,讓我給你一些食物吃,你好有體力趕路。」 23掃羅不肯,說:「我不吃」。他的隨從和婦人再三勸告,他才同意了,從地上起來坐到床上。 24婦人連忙宰了家中一隻小肥牛,又和麵烤了無酵餅, 25擺在掃羅和他的隨從面前,他們吃完後,當天晚上就離開了。