1 Samueli 23 – CCL & CCBT

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Samueli 23:1-29

Davide Apulumutsa Mzinda wa Keila

1Davide atawuzidwa kuti “Onani, Afilisti akuthira nkhondo mzinda wa Keila ndi kulanda zokolola zawo za mʼnkhokwe,” 2anafunsa Yehova kuti, “Kodi ndipite ndikamenyane nawo Afilistiwa?”

Yehova anamuyankha kuti, “Pita, kamenyane nawo Afilisti ndi kupulumutsa mzinda wa Keila.”

3Koma anthu amene anali ndi Davide anati, “Ngati tikuchita mantha ku Yuda konkuno, nanji kupita ku Keila kukamenyana ndi ankhondo a Afilisti!”

4Davide anafunsanso Yehova, ndipo Yehova anamuyankha kuti, “Pita ku Keila pakuti ndapereka Afilisti mʼdzanja lako.” 5Choncho Davide ndi anthu ake anapita ku Keila kukamenyana ndi Afilisti. Anapha Afilisti ambiri ndi kutenga ziweto zawo. Choncho anapulumutsa anthu a ku Keila. 6(Pamene Abiatara mwana wa Ahimeleki anathawira kwa Davide anabwera ndi efodi mʼmanja mwake).

Sauli Atsatira Davide

7Sauli atamva kuti Davide wapita ku Keila anati, “Mulungu wamupereka kwa ine, pakuti Davide wadzitsekera yekha mʼndende polowa mu mzinda umene uli ndi zipata ndi zotsekera zake.” 8Choncho Sauli anasonkhanitsa ankhondo ake nawatuma ku Keila kuti akamuzungulire Davide ndi anthu ake.

9Davide atadziwa kuti Sauli akufuna kumuchita chiwembu, anawuza Abiatara wansembe uja kuti, “Bwera nayo efodiyo.” 10Tsono Davide anayankhula ndi Yehova kuti, “Inu Yehova Mulungu wa Israeli, ine mtumiki wanu ndamva ndithu kuti Sauli akufuna kubwera ku Keila ndi kudzawononga mzindawu chifukwa cha ine. 11Kodi anthu a Keila adzandipereka mʼmanja mwa Sauli? Kodi Sauli abweradi monga ndamvera ine mtumiki wanu? Inu Yehova Mulungu wa Israeli, chonde, ndiwuzeni ine mtumiki wanu.”

Ndipo Yehova anati, “Sauli abweradi.”

12Davide anafunsanso, “Kodi anthu a ku Keila adzapereka ine ndi anthu angawa kwa Sauli?”

Ndipo Yehova anayankha, “Iwo adzakuperekanidi.”

13Choncho Davide ndi anthu ake, omwe analipo 600, anachoka ku Keila namayenda mothawathawa. Sauli atamva kuti Davide wathawa ku Keila, sanatumizeko ankhondo ake aja.

14Davide ankakhala mʼmapanga mʼdziko lamapiri ku chipululu cha Zifi. Sauli ankamufufuza tsiku ndi tsiku, koma Mulungu sanapereke Davide mʼmanja mwake.

15Davide anaona kuti Sauli akufunafuna kuti amuphe. Nthawiyi nʼkuti Davide ali mʼchipululu cha Zifi ku Horesi. 16Ndipo Yonatani mwana wa Sauli anapita kwa Davide ku Horesi ndipo anamulimbitsa mtima pomuwuza kuti Yehova ali naye. 17Iye anamuwuza kuti, “Usaope, abambo anga sadzakupha. Iwe udzakhala mfumu ya Israeli ndipo ine ndidzakhala wachiwiri wako. Ngakhale abambo anga Sauli akudziwa zimenezi.” 18Awiriwa anachita pangano pamaso pa Yehova. Ndipo Yonatani anabwerera kwawo, koma Davide anakhalabe ku Horesi.

19Anthu a ku Zifi anapita kwa Sauli ku Gibeya ndipo anamuwuza kuti, “Davide akubisala kwathu, mʼmapanga a ku Horesi, mʼphiri la Hakila, kummwera kwa Yesimoni. 20Tsopano inu, mubwere nthawi iliyonse imene mukufuna, ndipo ife tidzamupereka kwa mfumu.”

21Sauli anayankha kuti, “Yehova akudalitseni pakuti mwandichitira chifundo. 22Pitani mukatsimikizire. Mukaone kumene amakhala ndiponso mupeze munthu amene wamuona. Anthu amandiwuza kuti ndi wochenjera kwambiri. 23Kafufuzeni ndithu malo onse kumene amabisalako, ndipo mubwerenso kuno mudzandiwuze chenicheni. Pambuyo pake ine ndidzapita nanu. Ngatidi ali mʼderalo ndidzamusaka pakati pa mabanja onse a Yuda.”

24Kotero iwo ananyamuka ndi kupita ku Zifi, koma Sauli asananyamuke. Nthawi imeneyi Davide ndi anthu ake anali ku chipululu cha Maoni, ku Araba kummwera kwa Yesimoni. 25Sauli ndi anthu ake anapita kukamufufuza Davide. Koma Davide atamva izi anathawa ndi kukabisala ku thanthwe la chipululu cha Maoni. Sauli atamva kuti Davide anathawira ku Maoni anamutsatira ku chipululu komweko.

26Sauli amayenda mbali ina ya phirilo, ndipo Davide ndi anthu ake nawonso anali mbali ina ya phirilo. Koma Davide ndi anthu ake anafulumira kumuthawa Sauli pamene Sauliyo ndi anthu ake ali pafupi kuwagwira. 27Nthawi yomweyo munthu wina wamthenga anabwera kudzamuwuza Sauli kuti, “Bwerani msanga! Afilisti akuthira nkhondo dzikoli.” 28Choncho Sauli analeka kuthamangitsa Davide ndipo anapita kukamenyana ndi Afilisti. Nʼchifukwa chake malowa amatchedwa Mwala wa Malekano. 29Ndipo Davide anachoka kumeneko ndi kukakhala ku mapanga a ku Eni Gedi.

Chinese Contemporary Bible (Traditional)

撒母耳記上 23:1-29

大衛營救基伊拉

1一天,大衛得知非利士人正在攻打基伊拉,搶掠麥場, 2便求問耶和華:「我可以去攻打非利士人嗎?」耶和華答道:「你可以去攻打非利士人,營救基伊拉。」 3大衛的部下卻對他說:「我們在猶大這裡尚且膽戰心驚,何況去基伊拉攻打非利士軍隊呢!」 4大衛再求問耶和華,耶和華答道:「到基伊拉去吧,我一定把非利士人交在你手裡。」 5於是,大衛和部下到基伊拉去攻打非利士人,大敗敵人,奪取了他們的牲畜,救出基伊拉人。

6亞希米勒的兒子祭司亞比亞他基伊拉投奔大衛時,把以弗得也帶了去。 7掃羅得知大衛基伊拉,就說:「這一次是上帝把他交在我手中了,因為他竟然自投網羅,進入有門有閂的城。」 8掃羅召集全軍準備攻打基伊拉,圍困大衛和他的部下。 9大衛知道了掃羅的計謀,便吩咐祭司亞比亞他把以弗得帶來, 10然後說:「耶和華,以色列的上帝啊,僕人聽說掃羅要來毀滅基伊拉,因為我在這裡。 11基伊拉的人會不會把我交給掃羅呢?掃羅是不是像我聽說的那樣要來這裡呢?耶和華,以色列的上帝啊,求你告訴我。」耶和華說:「掃羅一定會來。」 12大衛又問耶和華:「基伊拉的人會不會把我和我的部下交給掃羅呢?」耶和華說:「他們一定會。」 13於是,大衛率領自己的六百部下離開基伊拉,到處流浪。掃羅得知大衛已經離開基伊拉,就不去了。

14大衛住在曠野的堡壘或西弗曠野的山區。掃羅天天搜捕大衛,但上帝沒有把大衛交在他的手中。 15大衛西弗曠野的何利沙得知掃羅要來殺他。 16掃羅的兒子約拿單何利沙大衛,鼓勵大衛堅定地信靠上帝。 17他對大衛說:「不要害怕,我父親害不了你。你將做以色列的王,我將做你的宰相。我父親也明白這一點。」 18二人在耶和華面前立了約。之後,大衛仍留在何利沙約拿單則回家去了。

19西弗人去基比亞掃羅,說:「大衛就躲在我們那裡,在曠野南面哈基拉山上何利沙的堡壘裡。 20王啊,你隨時都可以下來,我們一定把他交在王的手裡。」 21掃羅說:「願耶和華賜福給你們!因為你們體恤我。 22我聽說他非常狡猾,你們再回去弄清楚他的行蹤,誰在那裡見過他, 23查明他的藏身之處,回來如實告訴我,然後我會與你們同去。如果他在猶大境內,我要搜遍千家萬戶,找到他。」 24於是,西弗人先回去了。當時大衛和他的部下在曠野南面的亞拉巴,即瑪雲曠野。 25大衛聽說掃羅和手下正在搜尋他,便率領部下前往瑪雲曠野的磐石,住在那裡。掃羅得知後,便去瑪雲曠野追趕大衛26掃羅在山這邊走,大衛和他的部下在山那邊走,急急忙忙地躲避掃羅掃羅和他的手下四面包圍過來,眼看就要抓住他們了。 27這時,掃羅的信使前來稟報,說非利士人前來犯境,請王速回。 28掃羅只好放棄追趕大衛,回師迎戰非利士人。因此,那地方叫「脫險岩」。 29後來,大衛從那裡轉移到隱·基底的堡壘裡。