1 Samueli 21 – CCL & CARST

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Samueli 21:1-15

Davide Apita ku Nobi

1Davide anapita ku Nobi kwa wansembe Ahimeleki. Ahimelekiyo ankanjenjemera pamene ankamuchingamira, ndipo anafunsa kuti, “Muli nokha chifukwa chiyani? Chifukwa chiyani mulibe wokuperekezani?”

2Davide anayankha Ahimeleki kuti, “Mfumu yandituma zinthu zina ndipo yandiwuza kuti, ‘Munthu aliyense asadziwe za zimene ndakutumazo.’ Kunena za anthu anga, ndawawuza kuti tikakumane pamalo pena pake. 3Kodi muli ndi chakudya? Patseniko malofu a buledi asanu, kapena chilichonse muli nacho.”

4Koma wansembeyo anamuyankha Davide kuti, “Ine ndilibe buledi wamba woti ndikupatseni. Koma pali buledi wachipembedzo yekha. Ngati anthu amene muli nawo sanagone ndi akazi awo mukhoza kudya.”

5Davide anayankha kuti, “Kunena zoona sitinakhudzane ndi mkazi monga timachitira nthawi zonse tikakhala pa ulendo. Anthu anga salola kudziyipitsa ndi mkazi ngakhale pa ulendo wamba. Nanji lero tili pa ulendo woterewu!” 6Choncho wansembe uja anamupatsa buledi wachipembedzo popeza kunalibeko buledi wina aliyense koma yekhayo amene amaperekedwa kwa Yehova. Uyu ndi amene anachotsedwa tsiku limenelo kuti ayikepo wina wotentha.

7Koma tsiku limenelo mmodzi wa antchito a Sauli anali pomwepo kudikirira kuti achite mwambo wa chipembedzo mʼnyumba ya Mulungu. Munthuyu dzina lake anali Doegi Mwedomu, munthu wamphamvu pakati pa abusa a Sauli.

8Davide anafunsa Ahimeleki kuti, “Kodi muli ndi mkondo kapena lupanga pano? Ine sindinatenge lupanga langa kapena chida china chilichonse chifukwa zimene andituma amfumu ndi zamsangamsanga.”

9Wansembeyo anayankha kuti, “Kuno kuli lupanga la Goliati Mfilisiti uja amene unamupha mʼchigwa cha Ela, lakulungidwa mʼnsalu paseli pa Efodi. Ngati mufuna kulitenga, tengani popeza kuno kulibe lina koma lokhalo.”

Davide anati, “Palibe lina lofanana nalo. Ndipatseni lomwelo.”

Davide ku Gati

10Tsiku lomwelo Davide ananyamuka kuthawa Sauli ndipo anapita kwa Akisi, mfumu wa ku Gati. 11Koma nduna za Akisi zinafunsa mfumuyo kuti, “Kodi uyu si Davide mfumu ya dzikoli? Kodi iyeyu si uja pomuvinira ankayimba kuti,

“Sauli wapha 1,000,

koma Davide wapha miyandamiyanda?”

12Mawu amenewa anamulowa kwambiri Davide mu mtima ndipo anayamba kuopa kwambiri Akisi mfumu ya ku Gati. 13Choncho anasintha makhalidwe ake pamaso pawo, nʼkudzisandutsa ngati wamisala. Iye ankangolembalemba pa zitseko za chipata ndi kumangotuluka dovi, nʼkumayenderera mʼndevu zake.

14Akisi anawuza nduna zake kuti, “Mukumuona munthu uyu kuti ndi wamisala! Nʼchifukwa chiyani mukubwera naye kwa ine? 15Kodi ine ndikusowa anthu amisala kuti muzibwera naye munthuyu kwa ine kuti azidzachita zamisala zake pamaso panga? Kodi munthu ameneyu nʼkulowa mʼnyumba mwanga?”

Священное Писание (Восточный перевод), версия для Таджикистана

1 Царств 21:1-15

Довуд у священнослужителя в Нове

1Довуд пришёл в город Нов к священнослужителю Ахи-Малику. Встретив его, Ахи-Малик заволновался и спросил:

– Почему ты один? Почему с тобой никого нет?

2Довуд ответил священнослужителю Ахи-Малику:

– Царь поручил мне одно дело и сказал: «Никто не должен ничего знать о порученном тебе деле, с которым я тебя посылаю». А своим людям я велел встретить меня в условленном месте. 3Что у тебя тут есть под рукой? Дай мне пять лепёшек или что найдётся у тебя.

4Но священнослужитель ответил Довуду:

– У меня нет под рукой обычного хлеба, здесь есть священный хлеб21:4 Священный хлеб – двенадцать хлебов, которые выставлялись каждую субботу в священном шатре, а позже и в храме Всевышнего, а старые хлебы доставались священнослужителям (см. Исх. 25:30; Лев. 24:5-9). – но я дам его только при условии, что твои люди воздерживались от женщин.

5Довуд ответил:

– Поистине, женщин при нас не было – как обычно, когда я отправляюсь с поручением. Тела моих людей чисты, даже когда мы спешим по обычным поручениям. Насколько же чище они должны быть сегодня!

6И священнослужитель дал ему священный хлеб, потому что там не было другого хлеба, кроме того, который в тот день был взят с места, где он лежал перед Вечным и заменён свежим.

7(В тот день там был один из слуг Шаула, который задержался перед Вечным, это был эдомитянин Доэг, глава пастухов Шаула.)

8Довуд спросил Ахи-Малика:

– Нет ли у тебя здесь копья или меча? Я не захватил ни своего меча, ни иного оружия, потому что дело царя было срочным.

9Священнослужитель ответил:

– Здесь есть меч филистимлянина Голиафа, которого ты убил в долине Ела. Меч за ефодом, завёрнутый в одежду, если хочешь, возьми его. Кроме этого, здесь нет никакого другого меча.

Довуд сказал:

– Нет ему равного, дай его мне.

Довуд у филистимлян в Гате

10В тот день Довуд убежал от Шаула и пришёл к Ахишу, царю Гата. 11Но слуги Ахиша сказали ему:

– Разве это не Довуд, царь той страны? Разве это не тот, о ком они пели друг другу во время танцев: «Шаул сразил тысячи, а Довуд – десятки тысяч»?

12Довуд обратил внимание на эти слова и очень испугался Ахиша, царя Гата. 13Он притворился перед ними сумасшедшим и, пока был у них, вёл себя как безумный, царапал знаки на дверях и пускал слюни по бороде.

14Ахиш сказал своим слугам:

– Гляньте на этого человека! Он сумасшедший! Зачем вы привели его ко мне? 15Разве у меня мало помешанных, что вы привели ко мне и этого, чтобы он безумствовал передо мной? Для чего этому человеку входить в мой дом?