1 Samueli 13 – CCL & CCB

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Samueli 13:1-23

Samueli Adzudzula Sauli

1Sauli analowa ufumu ali ndi zaka makumi atatu, ndipo analamulira Israeli kwa zaka 42.

2Nthawi ina Sauli anasankha Aisraeli 3,000. Mwa iwowa, 2,000 anali ndi Sauliyo ku Mikimasi ndi ku dziko la mapiri ku Beteli, ndipo 1,000 anali ndi Yonatani ku Gibeya ku Benjamini. Anthu ena onse otsala anawabweza kwawo.

3Yonatani anakantha mkulu wa ankhondo wa Afilisti ku Geba, ndipo Afilisti anamva kuti Aheberi awukira. Tsono Sauli anawuza amithenga kuti alize lipenga mʼdziko lonse la Israeli. 4Choncho Aisraeli onse anamva kuti Sauli wakantha mkulu wa ankhondo Wachifilisiti ndi kuti Afilisti anayipidwa nawo Aisraeli. Ndiye anthu anayitanidwa kuti abwere kwa Sauli ku Giligala.

5Tsono Afilisti anasonkhana kuti amenyane ndi Aisraeli. Iwo anali ndi magaleta 3,000, okwera pa akavalo 2,000 ndiponso asilikali kuchuluka kwake ngati mchenga wa mʼmbali mwa nyanja. Iwo anapita ndi kukamanga misasa yawo ku Mikimasi, kummawa kwa Beti-Aveni. 6Pamene Aisraeli anaona kuti anali pamavuto akulu, poti anali atapanikizidwa kwambiri, anabisala mʼmapanga, mʼmaenje, mʼmatanthwe, mʼmakwalala ndi mʼzitsime. 7Ahebri ena anawoloka Yorodani mpaka kukafika ku dziko la Gadi ndi ku Giliyadi.

Koma Sauli anakhalabe ku Giligala ndipo ankhondo onse amene anali naye anali njenjenje ndi mantha. 8Saulo anadikirira masiku asanu ndi awiri, monga mwa nthawi imene ananena Samueli. Koma Samueli sanabwere ku Giligala, ndipo anthu anayamba kumuthawa Sauli uja. 9Kotero iye anati, “Bwera nayoni nsembe yopsereza ndi nsembe ya chiyanjano.” Ndipo Sauli anapereka nsembe yopsereza. 10Atangomaliza kupereka nsembe, anangoona Samueli watulukira ndipo Sauli anapita kukamulonjera.

11Samueli anafunsa kuti, “Nʼchiyani chimene wachita?”

Sauli anayankha kuti, “Nditaona kuti anthu ayamba kundithawa, ndi kuti inu simunabwere pa nthawi munanena ija, ndiponso kuti Afilisti akusonkhana ku Mikimasi, 12ndinati, ‘Tsopano Afilisti abwera kudzandithira nkhondo ku Giligala kuno, chonsecho sindinapemphe Yehova kuti andikomere mtima.’ Motero ndinakakamizika kupereka nsembe yopsereza.”

13Samueli anati, “Mwachita zopusa. Simunatsate zimene Yehova Mulungu wanu anakulamulani kuti muchite. Mukanazitsata, Yehova akanawukhazikitsa ufumu wanu mu Israeli mpaka kalekale. 14Koma tsopano ufumu wanu sudzakhalitsa. Yehova wapeza munthu wapamtima pake ndipo wamusankha kukhala mtsogoleri wa anthu ake chifukwa inu simunasunge malamulo a Yehova.”

15Kenaka Samueli anachoka ku Giligala ndi kupita ku Gibeyati ku dziko la Benjamini. Saulo anawerenga anthu amene anali naye ndipo analipo 600.

Sauli Akonzekera Nkhondo

16Sauli ndi mwana wake Yonatani pamodzi ndi asilikali amene anali naye aja amakhala ku Geba ku dziko la Benjamini. Koma Afilisti anamanga misasa yawo ku Mikimasi. 17Ankhondo a Afilisti anatuluka mʼmisasa yawo mʼmagulu atatu. Gulu lina linapita ku Ofiri ku dziko la Suwala. 18Gulu lina linalunjika ku Beti-Horoni, ndipo gulu lachitatu linalunjika ku malire oyangʼanana ndi chigwa cha Zeboimu cha ku chipululu.

19Nthawi imeneyo nʼkuti mulibe osula zitsulo mʼdziko lonse la Israeli, pakuti Afilisti anati, “Tisawalole Aheberi kudzipangira okha malupanga kapena mikondo!” 20Kotero Aisraeli onse amapita kwa Afilisti kukanoletsa mapulawo, makasu, nkhwangwa ndi zikwakwa zawo. 21Mtengo wonolera mapulawo ndi makasu unali zigawo ziwiri za sekeli, mtengo wonolera zisonga ndi nkhwangwa unali gawo limodzi la Sekeli.

22Motero tsiku la nkhondolo panalibe lupanga kapena mkondo mʼdzanja la aliyense amene anatsatira Saulo ndi Yonatani. Koma Saulo ndi Yonatani, iwo okha ndiwo anali ndi zida.

Yonatani Athira Nkhondo Afilisti

23Tsono gulu lina lankhondo la Chifilisti linapita kukalonda mpata wa Mikimasi.

Chinese Contemporary Bible (Simplified)

撒母耳记上 13:1-23

扫罗犯罪

1扫罗四十岁13:1 希伯来文无“四十岁”,一些七十士希腊文译本有此数字。登基。他在统治以色列的第二年, 2以色列人中选出三千人,亲自带领其中的两千人到密抹伯特利山,另外一千人和约拿单留在便雅悯境内的基比亚。他把其余的人遣散回家。 3约拿单攻打迦巴非利士驻军,非利士人听到了这消息。于是,扫罗在各地吹响号角,通告希伯来人。 4以色列众人听说扫罗攻打非利士人的驻军,并听说非利士人对以色列人恨之入骨,便响应扫罗的号召,聚集在吉甲5非利士人调兵遣将,要攻打以色列。他们有三万辆战车和六千骑兵,步兵多如海边的沙。大军来到伯·亚文以东的密抹,驻扎在那里。 6以色列人看见敌军压境,情势危急,纷纷躲进山洞、丛林、石穴、地洞和坑里。 7有些希伯来人过了约旦河,逃到迦得基列。但扫罗仍然留在吉甲,跟随他的人都害怕得发抖。

8扫罗按着撒母耳所定的日期在吉甲等了七天,可是撒母耳还没有来。扫罗的军兵开始溜走。 9于是,扫罗说:“你们把燔祭和平安祭带到我这里来”。他就献上了燔祭。 10扫罗刚把燔祭献完,撒母耳就来了,扫罗出去迎接他,向他问安。 11撒母耳扫罗说:“你做的是什么事?”扫罗答道:“我看见手下的人不断离我而去,你到了约定的时候还没有来,而且非利士人就聚集在密抹12我想非利士人就要到吉甲来攻打我们了,但我们还没有向耶和华求助,我迫不得已,就献上燔祭了。” 13撒母耳说:“你真糊涂!你违背了你的上帝耶和华的命令。祂本来要使你的王位在以色列永远坚立, 14但现在你的王位不能长久了,耶和华已经找到一个合祂心意的人,要立他做百姓的君王。因为你没有遵守耶和华的命令。” 15撒母耳离开吉甲便雅悯境内的基比亚扫罗数了一下跟随他的人,约有六百人。

16扫罗及其儿子约拿单和随从留在便雅悯境内的迦巴非利士人则在密抹扎营。 17非利士人分成三队施行突袭,一队前往书亚境内的俄弗拉18一队前往伯·和仑,一队前往边境地区,那里可以俯瞰旷野附近的洗波音谷。

19那时,以色列全境找不到一个铁匠,这是因为非利士人的禁令,以免希伯来人制造刀枪。 20以色列人都要到非利士的铁匠那里去磨锄、犁、斧和铲。 21磨锄或犁要花八克银子,磨三齿叉、斧头或赶畜棒要花四克银子。 22所以在交战的日子,除了扫罗约拿单外,其他以色列人手上都没有刀枪。 23当时非利士的一队防兵前往密抹的隘口驻守。