1 Samueli 11 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Samueli 11:1-15

Sauli Apulumutsa Mzinda wa Yabesi

1Nahasi, Mwamoni anapita ndi kuzungulira mzinda wa Yabesi Giliyadi. Tsono anthu onse a ku Yabesi anapempha Nahasiyo kuti, “Muchite nafe pangano, ndipo tidzakutumikirani.”

2Koma Nahasi Mwamoni uja anayankha kuti, “Ndidzachita nanu pangano pokhapokha nditakolowola diso lakumanja la aliyense wa inu kuti ndichititse manyazi Aisraeli onse.”

3Akuluakulu a mzinda wa Yabesi anati kwa iye, “Utipatse masiku asanu ndi awiri kuti titumize uthenga mu Israeli monse. Ngati sipapezeka wodzatipulumutsa, ndiye ife tidzadzipereka kwa iwe.”

4Amithenga aja atafika kwawo kwa Sauli ku Gibeya ndi kufotokoza nkhaniyi kwa anthu onse, iwo analira motaya mtima. 5Pa nthawiyo nʼkuti Sauli akubwera kuchokera ku munda, ali pambuyo pa ngʼombe zake za ntchito ndipo anafunsa. “Nʼchiyani chawavuta anthuwa kuti azilira motere?” Ndipo anamufotokozera zomwe anthu a mu mzinda wa Yabesi ananena.

6Sauli atamva mawu awo, Mzimu wa Mulungu unabwera pa iye mwa mphamvu ndipo anakwiya kwambiri. 7Tsono anatenga ngʼombe ziwiri za ntchito, nazidula nthulinthuli. Ndipo anatumiza amithenga ndi nthulizo dziko lonse la Israeli ndi mawu akuti, “Umo ndi mmene adzachite ndi ngʼombe ya aliyense amene satsata Sauli ndi Samueli.” Ndipo anthu anachita mantha aakulu motero kuti onse ananyamuka ndi mtima umodzi. 8Pamenepo Sauli anawasonkhanitsa ku Bezeki nawawerenga, ndipo Aisraeli analipo 300,000, Ayuda analipo 30,000.

9Tsono Sauli anawuza amithenga ochokera ku Yabesi aja kuti, “Mukawawuze anthu a ku Yabesi Giliyadi kuti mawa nthawi ya masana adzapulumutsidwa.” Pamene amithengawo anapita ndi kukafotokoza nkhani imeneyi kwa anthu a ku Yabesi, iwo anasangalala kwambiri. 10Choncho anthu a ku Yabesi anawuza Nahasi kuti, “Mawa tidzadzipereka kwa inu ndipo inu mudzachite nafe chilichonse chokukomerani.”

11Tsono mmawa mwake Sauli anagawa anthuwo mʼmagulu atatu. Mmamawa kusanache iwo analowa mʼmisasa ya Aamoni ndi kuwapha mpaka masana. Amene anapulumuka anabalalika, aliyense kwakekwake.

Sauli Avomerezedwa kukhala mfumu

12Kenaka anthu anafunsa Samueli kuti, “Kodi ndani aja ankanena kuti, ‘Kodi Sauli nʼkutilamulira ife?’ Bwera nawoni kuno kuti tidzawaphe.”

13Koma Sauli anati, “Palibe amene ati aphedwe lero, pakuti lero lino Yehova wagwira ntchito yopulumutsa Israeli.”

14Ndipo Samueli anati kwa anthuwo, “Tiyeni tipite ku Giligala kuti tikatsimikizenso kuti Sauli ndi mfumu yathu.” 15Choncho anthu onse anapita ku Giligala ndipo kumeneko Samueli anakalonga Sauli ufumu pamaso pa Yehova. Pambuyo pake anthu anapereka nsembe zachiyanjano pamaso pa Yehova, ndipo Sauli ndi Aisraeli onse anachita chikondwerero chachikulu.