1 Petro 5 – CCL & NSP

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Petro 5:1-14

Akulu Ampingo ndi Anyamata mu Mpingo

1Ine ndikupempha akulu a mpingo amene ali pakati panu, monga inenso mkulu mnzawo, mboni ya zowawa za Khristu ndiponso amene ndidzalandira nawo ulemerero umene uti udzaonetsedwe. 2Wetani gulu la Mulungu limene lili mʼmanja mwanu, muziliyangʼanira. Muzichita osati mowumirizidwa, koma mwakufuna kwanu, monga momwe Mulungu akufunira kuti mutero. Musachite chifukwa chadyera la ndalama, koma ndi mtima ofuna kutumikira. 3Musakhale ngati mafumu pa amene mukuwayangʼanira, koma mukhale chitsanzo kwa gululo. 4Ndipo Mʼbusa wamkulu akadzaonekera, mudzalandira chipewa cha ulemerero chosafota.

5Momwemonso, inu anyamata gonjerani amene ndi akulu. Inu nonse mukhale odzichepetsa kuti mutumikirane, chifukwa,

“Mulungu amatsutsana nawo odzikuza,

koma amapereka chisomo kwa odzichepetsa.”

6Choncho, mudzichepetse pamaso pa Mulungu wamphamvu, kuti pa nthawi yake adzakukwezeni. 7Tayani pa Iye nkhawa zanu zonse chifukwa ndiye amakusamalani.

8Khalani odziretsa ndi atcheru. Mdani wanu mdierekezi amayendayenda monga mkango wobangula kufunafuna wina kuti amumeze. 9Mukaneni iye, ndipo mukhazikike mʼchikhulupiriro, chifukwa mukudziwa kuti abale anzanu pa dziko lonse lapansi nawonso akumva zowawa zomwezi.

10Ndipo Mulungu wachisomo chonse, amene anakuyitanani ku ulemerero wake wamuyaya mwa Khristu, mutamva zowawa pa kanthawi, adzakukonzaninso ndi kukulimbitsani pa maziko olimba. 11Kwa Iye kukhale mphamvu mpaka muyaya, Ameni.

Mawu Otsiriza

12Mothandizidwa ndi Sila, amene ndi mʼbale wokhulupirika, ndakulemberani mwachidule kukulimbikitsani ndi kuchita umboni kuti ichi ndi chisomo choona cha Mulungu. 13Imani mwamphamvu mʼchisomochi. Mlongo wanu amene ali ku Babuloni, wosankhidwa pamodzi nanu akupereka moni, nayenso Marko, mwana wanga, akupereka moni. 14Mupatsane moni ndi mpsopsono wachikondi. Mtendere ukhale ndi inu nonse amene muli mwa Khristu.

New Serbian Translation

1. Петрова 5:1-14

Однос пастира према цркви

1Оне који су старешине међу вама молим ја, који сам и сам старешина и сведок Христових мука, те учесник у слави која треба да се открије, 2да напасате Божије стадо које вам је поверено. Али не чините то присилно, него драговољно, како је Богу по вољи, и не из користољубља, него из одушевљења. 3Не понашајте се деспотски према онима који су вам поверени, него будите примери стаду. 4А кад се појави врховни Пастир, примићете славни венац који не вене.

5Тако и ви, младићи, покоравајте се старешинама. А сви се заодените понизношћу, да служите једни другима, јер:

„Бог се супротставља охолима,

а понизнима исказује милост.“

6Стога се понизите под моћну руку Божију, да вас узвиси у право време. 7Пребаците сву своју бригу на њега, јер се он брине за вас.

8Будите трезвени, бдите, јер ваш непријатељ, ђаво, обилази као ричући лав и тражи кога да прождере. 9Будите чврсти у вери, те му се одуприте, знајући да и ваша браћа по вери широм света пролазе кроз исте патње.

10А Бог, милостив у свему, који вас је по Христу Исусу позвао у вечну славу, он ће вас, након ваше кратке патње усавршити, учврстити, оснажити и утемељити. 11Његова је сила довека. Амин.

Закључак и поздрав

12Написао сам вам ово кратко писмо уз помоћ Силвана, кога сматрам верним братом, да вас опоменем и потврдим да је ово права милост Божија. Ње се држите.

13Поздравља вас црква у Вавилону, која је заједно са вама изабрана од Бога, и мој син Марко. 14Поздравите једни друге пољупцем љубави.

Мир са свима вама који сте у Христу.