1 Petro 4 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Petro 4:1-19

Moyo Watsopano

1Popeza kuti Khristu anamva zowawa mʼthupi lake, mukhale nawonso mtima omwewo, chifukwa iye amene wamva zowawa mʼthupi lake walekana nawo uchimo. 2Chifukwa cha ichi, iwo sakhalanso moyo wawo akuchita zofuna za matupi awo, koma amachita chifuniro cha Mulungu. 3Pakuti mwataya kale nthawi yambiri mʼmbuyomu pochita zimene anthu osapembedza amachita, moyo wokhumba zonyansa, zilakolako zoyipa kuledzera, zochitika zoyipa za pa phwando, mapokoso ndi kupembedza mafano onyansa. 4Anthu osapembedza amadabwa pamene simuthamangira nawo kuchita zoyipitsitsazi, nʼchifukwa chake amakuchitani chipongwe. 5Koma adzafotokoza okha mlandu wawo kwa Mulungu amene wakonzeka kuweruza amoyo ndi akufa. 6Pa chifukwa chimenechi, Uthenga Wabwino unalalikidwa ngakhale kwa iwo amene tsopano ndi akufa, kuti adzaweruzidwe monga anthu ku thupi, koma adzakhale ndi moyo monga mwa Mulungu mu mzimu.

7Chimaliziro cha zinthu zonse chili pafupi. Choncho khalani maso ndi odziletsa kuti muthe kupemphera. 8Koposa zonse muzikondana wina ndi mnzake kwambiri, chifukwa chikondi chimaphimba machimo ambiri. 9Muzisamalirana wina ndi mnzake osamanyinyirika. 10Aliyense agwiritse ntchito mokhulupirika mphatso iliyonse imene anayilandira potumikira ena ngati adindo ogwiritsa bwino ntchito mphatso za Mulungu za mitundumitundu. 11Ngati wina ayankhula, ayankhuledi mawu enieni a Mulungu. Ngati wina atumikira, atumikire ndi mphamvu imene Mulungu amapereka, kuti pa zonse Mulungu alemekezedwe mwa Yesu Khristu. Kwa Iye kukhale ulemerero ndi mphamvu mpaka muyaya, Ameni.

Kumva Zowawa Chifukwa cha Chikhristu

12Abale okondedwa musadabwe ndi mayesero owawa amene mukukumana nawo ngati kuti china chake chachilendo chakuchitikirani. 13Koma kondwerani popeza mukumva zowawa pamodzi ndi Khristu, kuti mudzakondwere kwakukulu pamene ulemerero wake udzaonekera. 14Ngati akuchitani chipongwe chifukwa cha dzina la Khristu, ndinu odala, ndiye kuti Mzimu waulemerero wa Mulungu uli pa inu. 15Ngati mumva zowawa, zisakhale chifukwa cha kupha munthu, kapena kuba, kapena kuchita choyipa, kapena kulowerera za anthu ena, 16koma ngati mumva zowawa chifukwa ndinu Mkhristu, musachite manyazi, koma muyamike Mulungu chifukwa cha dzinalo. 17Pakuti nthawi yafika kuti chiweruzo chiyambe mʼnyumba ya Mulungu, ndipo ngati chiyamba ndi ife nanga podzafika kwa osamvera Uthenga Wabwino wa Mulungu, chidzakhala chotani? 18Monga Malemba akuti,

“Ngati kuli kovuta kuti olungama apulumuke,

nanga munthu wochimwa, wosasamala za Mulungu adzatani?”

19Nʼchifukwa chake, iwo amene akumva zowawa monga mwa chifuniro cha Mulungu, adzipereke okha mʼmanja mwa Mlengi wawo wokhulupirika ndi kumapitiriza kuchita zabwino.