Fuko la Isakara
1Ana a Isakara anali awa:
Tola, Puwa, Yasubu ndi Simironi ndipo onse analipo anayi.
2Ana a Tola ndi awa:
Uzi, Refaya, Yerieli, Yahimai, Ibisamu ndi Samueli. Awa anali atsogoleri a mabanja awo. Pa nthawi ya ulamuliro wa Davide zidzukulu za Tola zomwe zinali anthu odziwa kumenya nkhondo zinalipo 22,600.
3Mwana wa Uzi anali
Izirahiya.
Ana a Izirahiya anali:
Mikayeli, Obadiya, Yoweli ndi Isiya. Onse asanu anali atsogoleri a mabanja. 4Monga mwa chiwerengero cha mabanja awo, panali anthu 36,000 odziwa kumenya nkhondo, pakuti iwo anali ndi akazi ndi ana ambiri.
5Abale awo onse a mʼbanja la Isakara amene anali odziwa kumenya nkhondo analipo 87,000, olembedwa potsata mibado yawo.
Fuko la Benjamini
6Ana atatu a Benjamini anali awa:
Bela, Bekeri ndi Yediaeli.
7Ana a Bela anali awa:
Eziboni, Uzi, Uzieli, Yerimoti ndi Iri. Iwowa anali atsogoleri a mabanja awo ndipo onse pamodzi analipo asanu. Pa mndandanda wa mʼbado wawo panali anthu 22,034 odziwa kumenya nkhondo.
8Ana a Bekeri anali awa:
Zemira, Yowasi, Eliezara, Eliyoenai, Omiri, Yeremoti, Abiya, Anatoti ndi Alemeti. Onsewa anali ana a Bekeri. 9Pa mndandanda wa mʼbado wawo panali atsogoleri a mabanja ndi anthu 20,200 odziwa kumenya nkhondo.
10Mwana wa Yediaeli anali
Bilihani.
Ana a Bilihani anali awa:
Yeusi, Benjamini, Ehudi, Kenaana, Zetani, Tarisisi ndi Ahisahara. 11Ana onsewa a Yediaeli anali atsogoleri a mabanja. Analipo anthu 17,200 amene anali okonzeka kupita ku nkhondo.
12Asupi ndi Ahupi anali zidzukulu za Iri, ndipo Ahusimu anali zidzukulu za Aheri.
Fuko la Nafutali
13Ana a Nafutali anali awa:
Yahazieli, Guni, Yezeri ndi Salumu, zidzukulu za Biliha.
Fuko la Manase
14Ana a Manase anali awa:
Asirieli ndi mwana amene anabereka kwa mzikazi wake wa ku Aramu. Mzikazi yemweyo anaberekanso Makiri abambo ake a Giliyadi. 15Makiri anatenga mkazi wa banja la Ahupi ndi Asupi. Mlongo wake anali Maaka.
Mwana wake wina anali Zelofehadi, amene anabereka ana aakazi okhaokha.
16Maaka mkazi wa Makiri anabereka mwana wamwamuna ndipo anamutcha Perezi. Mʼbale wake anamutcha Seresi, ndipo ana ake anali Ulamu ndi Rakemu.
17Mwana wa Ulamu anali
Bedani.
Awa anali ana a Giliyadi mwana wa Makiri, mwana wa Manase. 18Mlongo wake Hamoleketi anabereka Isihodi, Abiezeri ndi Mahila.
19Ana a Semida anali:
Ahiyani, Sekemu, Likihi ndi Aniyamu.
Fuko la Efereimu
20Ana a Efereimu anali awa:
Sutela, Beredi,
Tahati, Eliada,
Tahati, 21Zabadi,
Sutela.
Ezeri ndi Eladi anaphedwa ndi anthu a ku Gati, pamene anabwera kudzalanda zoweta zawo. 22Efereimu, abambo awo, anawalira masiku ambiri, ndipo abale ake anabwera kudzamutonthoza. 23Kenaka anagona ndi mkazi wake, ndipo anakhala woyembekezera nabala mwana wamwamuna. Anamutcha dzina lake Beriya, chifukwa tsoka linagwera banja lake. 24Mwana wake wamkazi anali Seera, amene anamanga mzinda wa Beti-Horoni Wakumunsi, Wakumtunda kudzanso Uzeni-Seera.
25Mwana wina wa Efereimu anali Refa amene zidzukulu zake zinali Resefu,
Tela, Tahani,
26Ladani, Amihudi,
Elisama, 27Nuni
ndi Yoswa.
28Malo amene ankakhala anali Beteli ndi midzi yozungulira, cha kummawa kunali Naarani, Gezeri ndi midzi yake ya kumadzulo ndi Sekemu ndi midzi yake mpaka ku Aya ndi midzi yake. 29Mʼmbali mwa malire a Manase munali Beti-Seani, Taanaki, Megido ndi Dori, pamodzi ndi midzi yake. Zidzukulu za Yosefe mwana wa Israeli zimakhala mʼmizinda imeneyi.
Fuko la Aseri
30Ana a Aseri anali awa:
Imuna, Isiva, Isivi ndi Beriya. Mlongo wawo anali Sera.
31Ana a Beriya anali awa:
Heberi ndi Malikieli amene anabereka Birizaiti.
32Heberi anabereka Yafuleti, Someri, Hotamu ndi Suwa, mlongo wawo.
33Ana a Yafuleti anali awa:
Pasaki, Bimuhali ndi Asivati.
Awa anali ana a Yafuleti.
34Ana a Someri anali awa:
Ahi, Rohiga, Yehuba ndi Aramu.
35Ana a mʼbale wake Helemu anali awa:
Zofa, Imuna, Selesi ndi Amali.
36Ana a Zofa anali awa:
Suwa, Harineferi, Suwali, Beri, Imula, 37Bezeri, Hodi, Sama, Silisa, Itirani ndi Bera.
38Ana a Yeteri anali awa:
Yefune, Pisipa ndi Ara.
39Ana a Ula anali awa:
Ara, Hanieli ndi Riziya.
40Onsewa anali zidzukulu za Aseri, atsogoleri a mabanja, anthu omveka, ankhondo olimba mtima, ndi akuluakulu pakati pa atsogoleri anzawo. Chiwerengero cha anthu odziwa kumenya nkhondo chomwe chinalembedwa chinali 26,000.
以萨迦的后裔
1以萨迦的四个儿子是陀拉、普瓦、雅述和伸仑。 2陀拉的儿子是乌西、利法雅、耶勒、雅买、易伯散和示姆利,他们都是陀拉宗族的族长。在大卫执政年间,陀拉家共有两万二千六百个英勇的战士。 3乌西的儿子是伊斯拉希。伊斯拉希的儿子是米迦勒、俄巴底亚、约珥、伊示雅,他们五人都是族长。 4他们妻儿众多,因此各宗族中可以出征作战的共有三万六千人。 5按家谱的记载,以萨迦支派的各族中共有八万七千个英勇的战士。
便雅悯的后裔
6便雅悯的三个儿子是比拉、比结和耶叠。 7比拉的五个儿子是以斯本、乌西、乌薛、耶利摩和以利,他们都是族长,是英勇的战士。按家谱记载,他们宗族共有两万二千零三十四个战士。 8比结的儿子是细米拉、约阿施、以利以谢、以利约乃、暗利、耶利摩、亚比雅、亚拿突和亚拉篾。 9比结的儿子都是族长。按家谱的记载,他们宗族共有两万零二百个英勇的战士。 10耶叠的儿子是比勒罕,比勒罕的儿子是耶乌斯、便雅悯、以忽、基拿拿、细坦、他施和亚希沙哈。 11这些耶叠的儿子都是族长,宗族中可以英勇作战的共一万七千二百人。 12以珥的儿子是书品和户品,亚黑的儿子是户伸。
拿弗他利的后裔
13拿弗他利的儿子是雅薛、沽尼、耶色和沙龙。他们都是辟拉的后代。
玛拿西的后裔
14玛拿西的妾是亚兰人,她给玛拿西生的儿子是亚斯列,另外还生了基列的父亲玛吉。 15玛吉娶了户品和书品的妹妹玛迦。玛拿西的次子名叫西罗非哈,西罗非哈只有几个女儿。 16玛吉的妻子玛迦生了一个儿子,给他取名叫毗利施。毗利施的兄弟名叫示利施,示利施的儿子是乌兰和利金。 17乌兰的儿子是比但。这些都是基列的子孙。基列是玛吉的儿子,玛吉是玛拿西的儿子。 18基列的妹妹哈摩利吉生了伊施何、亚比以谢和玛拉。 19示米大的儿子是亚现、示剑、利克希和阿尼安。
以法莲的后裔
20以法莲的后代有书提拉,书提拉的儿子是比列,比列的儿子是他哈,他哈的儿子是以拉大,以拉大的儿子是他哈, 21他哈的儿子是撒拔,撒拔的儿子是书提拉。以法莲的另外两个儿子以谢和以列因为偷迦特人的牲畜而被当地人杀死了。 22他们的父亲以法莲为他们悲伤了多日,亲戚都来安慰他。 23后来,以法莲与妻子同房,妻子怀孕,生了一个儿子。以法莲因家里遭遇不幸,就给孩子取名叫比利亚7:23 “比利亚”意思是“不幸”。。 24以法莲有一个女儿叫舍伊拉,她建了上伯·和仑、下伯·和仑和乌羡·舍伊拉。 25比利亚的儿子是利法和利悉,利悉的儿子是他拉,他拉的儿子是他罕, 26他罕的儿子是拉但,拉但的儿子是亚米忽,亚米忽的儿子是以利沙玛, 27以利沙玛的儿子是嫩,嫩的儿子是约书亚。 28以法莲人的地业和住处包括伯特利及其四围的村庄、东部的拿兰、西部的基色及其四围的村庄、示剑及其四围的村庄,远至迦萨及其四围的村庄。 29玛拿西人的地业包括伯·善、他纳、米吉多、多珥以及它们四围的村庄。这些是以色列之子约瑟的后代居住的地方。
亚设的后裔
30亚设的儿子是音拿、亦施瓦、亦施韦、比利亚,女儿是西拉。 31比利亚的儿子是希别和玛结,玛结的儿子是比撒威。 32希别的儿子是雅弗勒、朔默、何坦,女儿是书雅。 33雅弗勒的儿子是巴萨、宾哈和亚施法。这三人是雅弗勒的儿子。 34朔默的儿子是亚希、罗迦、耶户巴和亚兰。 35朔默的兄弟希连的儿子是琐法、音那、示利斯和亚抹。 36琐法的儿子是书亚、哈尼弗、书阿勒、比利、音拉、 37比悉、河得、珊玛、施沙、益兰、比拉。 38益帖的儿子是耶孚尼、毗斯巴、亚拉。 39乌拉的儿子是亚拉,汉尼业和利谢。 40这些都是亚设的后代。他们都是族长,是英勇的战士和杰出的首领。按照家谱的记载,他们宗族中可以出征作战的共有两万六千人。