1 Mbiri 27 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Mbiri 27:1-34

Magulu a Anthu Ankhondo

1Uwu ndi mndandanda wa Aisraeli, atsogoleri a mabanja, olamulira asilikali 1,000, olamulira asilikali 100 ndi akuluakulu awo, amene ankatumikira mfumu mʼzonse zokhudza magulu a ankhondo, amene amagwira ntchito mwezi ndi mwezi chaka chonse. Gulu lililonse linali ndi anthu 24,000.

2Amene amalamulira gulu loyamba pa mwezi woyamba anali Yasobeamu mwana wa Zabidieli. Pa gulu lake panali asilikali 24,000. 3Iyeyu anali chidzukulu cha Perezi ndipo anali mkulu wa atsogoleri onse a ankhondo mwezi woyamba.

4Amene amalamulira gulu lachiwiri pa mwezi wachiwiri anali Dodai Mwahohi; Mikiloti ndiye anali mtsogoleri wa gulu lake. Pa gulu lake panali asilikali 24,000.

5Wolamulira ankhondo wachitatu, pa mwezi wachitatu anali Benaya, mwana wa wansembe Yehoyada. Iye anali mtsogoleri ndipo pa gulu lake panali ankhondo 24,000. 6Uyu ndi Benaya uja amene anali wamphamvu pa gulu la anthu makumi atatu ndipo ndiye amatsogolera anthu makumi atatu aja. Mwana wake Amizabadi ndiye amatsogolera gulu lake.

7Wachinayi pa mwezi wachinayi anali Asaheli mʼbale wake wa Yowabu; ndipo mwana wake Zebadiya ndiye analowa mʼmalo mwake. Pa gulu lake panali asilikali 24,000.

8Wachisanu pa mwezi wachisanu anali Samihuti, mdzukulu wa Izira. Pa gulu lake panali asilikali 24,000.

9Wa 6 pa mwezi wa 6 anali Ira mwana wa Ikesi wa ku Tekowa. Pa gulu lake panali asilikali 24,000.

10Wa 7 pa mwezi wa 7 anali Helezi Mpeloni wa fuko la Efereimu. Pa gulu lake panali asilikali 24,000.

11Wa 8 pa mwezi wa 8 anali Sibekai Mhusati, wa mbumba ya Zera. Pa gulu lake panali asilikali 24,000

12Wa 9 pa mwezi wa 9 anali Abiezeri wa banja la Anatoti, wa fuko la Benjamini. Pa gulu lake panali asilikali 24,000.

13Wa khumi pa mwezi wa khumi anali Mahazayi wa ku Netofa, wa mbumba ya Zera. Pa gulu lake panali asilikali 24,000.

14Mtsogoleri wa 11, pa mwezi wa 11 anali Benaya wa ku Piratoni, wa fuko la Efereimu. Pa gulu lake panali asilikali 24,000.

15Mtsogoleri wa 12, pa mwezi wa 12 anali Helidai Mnetofa, wa banja la Otanieli. Pa gulu lake panali asilikali 24,000.

Akuluakulu a Mafuko a Israeli

16Akuluakulu amene amatsogolera mafuko a Israeli ndi awa:

Mtsogoleri wa fuko la Rubeni: Eliezara mwana wa Zikiri;

mtsogoleri wa fuko la Simeoni: Sefatiya mwana wa Maaka;

17mtsogoleri wa fuko la Levi: Hasabiya mwana wa Kemueli,

mtsogoleri wa banja la Aaroni: Zadoki;

18mtsogoleri wa fuko la Yuda: Elihu, mʼbale wake wa Davide;

mtsogoleri wa fuko la Isakara: Omuri mwana wa Mikayeli;

19mtsogoleri wa fuko la Zebuloni: Isimaiya mwana wa Obadiya;

mtsogoleri wa fuko la Nafutali: Yerimoti mwana wa Azirieli;

20mtsogoleri wa fuko la Efereimu: Hoseya mwana wa Azaziya;

mtsogoleri wa fuko la theka la Manase: Yoweli mwana wa Pedaya;

21mtsogoleri wa fuko la theka la Manase limene linali ku Giliyadi: Ido mwana wa Zekariya;

mtsogoleri wa fuko la Benjamini: Yaasieli mwana wa Abineri;

22mtsogoleri wa fuko la Dani: Azareli mwana wa Yerohamu.

Awa anali akuluakulu a mafuko a Israeli.

23Davide sanawerenge amuna amene anali ndi zaka makumi awiri kapena kucheperapo, chifukwa Yehova analonjeza kuti adzachulukitsa Aisraeli ngati nyenyezi zamumlengalenga. 24Yowabu mwana wa Zeruya anayamba kuwerenga amuna koma sanamalize. Mkwiyo unagwera Aisraeli chifukwa cha zimenezi ndipo chiwerengerochi sanachilowetse mʼbuku la mbiri ya mfumu Davide.

Anthu Oyangʼanira Chuma cha Mfumu

25Azimaveti mwana wa Adieli ankayangʼanira nyumba zosungiramo katundu wa mfumu.

Yonatani mwana wa Uziya ankayangʼanira nyumba zosungiramo katundu wa maboma ozungulira, mizinda, midzi ndi malo olondera.

26Eziri mwana wa Kelubi ankayangʼanira anthu ogwira ntchito yolima ku munda.

27Simei wa ku Rama ankayangʼanira minda ya mpesa.

Zabidi wa ku Sifamu ankayangʼanira mphesa ndi mosungiramo mwake.

28Baala-Hanani wa ku Gederi ankayangʼanira mitengo ya olivi ndi ya mikuyu ya ku Sefela.

Yowasi ankayangʼanira mafuta a Olivi.

29Sitirayi wa ku Saroni ankayangʼanira ziweto zimene amaweta ku Saroni.

Safati mwana wa Adilayi ankayangʼanira ngʼombe zakuzigwa.

30Obili Mwismaeli ankayangʼanira ngamira.

Yehideya Mmerenoti ankayangʼanira abulu.

31Yazizi Mhagiri akayangʼanira nkhosa ndi mbuzi.

Onsewa anali akuluakulu oyangʼanira chuma cha mfumu Davide.

32Yonatani, malume wake wa Davide, anali phungu wake ndipo anali munthu wanzeru komanso analinso mlembi. Yehieli mwana wa Hakimoni ankasamalira ana a mfumu.

33Ahitofele anali phungu wa mfumu.

Husai Mwariki anali bwenzi la mfumu. 34Ahitofele atamwalira mʼmalo mwake munalowa Yehoyada mwana wa Benaya ndi Abiatara.

Yowabu anali mtsogoleri wa gulu lankhondo la mfumu.