1 Mbiri 26 – CCL & CCB

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Mbiri 26:1-32

Alonda a pa Zipata

1Magulu a alonda a pa zipata:

Kuchokera ku banja la Kora: Meselemiya mwana wa Kore, mmodzi mwa ana a Asafu.

2Meselemiya anali ndi ana awa:

woyamba Zekariya,

wachiwiri Yediaeli,

wachitatu Zebadiya,

wachinayi Yatinieli,

3wachisanu Elamu,

wachisanu ndi chimodzi Yehohanani,

ndipo wachisanu ndi chiwiri Elihunai.

4Obedi-Edomu analinso ndi ana awa:

woyamba Semaya,

wachiwiri Yehozabadi,

wachitatu Yowa,

wachinayi Sakara,

wachisanu Netaneli,

5wachisanu ndi chimodzi Amieli,

wachisanu ndi chiwiri Isakara

ndipo wachisanu ndi chitatu Peuletayi.

(Pakuti Mulungu anadalitsa Obedi-Edomu).

6Mwana wake Semaya analinso ndi ana amene anali atsogoleri mʼbanja la abambo awo chifukwa anali anthu amphamvu. 7Ana a Semaya anali: Otini, Refaeli, Obedi ndi Elizabadi; abale ake, Elihu ndi Semakiya, analinso anthu amphamvu. 8Onsewa anali adzukulu a Obedi-Edomu. Iwo ndi ana awo ndiponso abale awo anali anthu aluso ndi amphamvu pogwira ntchito. Zidzukulu zonse za Obedi-Edomu zinalipo 62.

9Meselemiya anali ndi ana ndi abale ake amene anali aluso ndipo onse analipo 18.

10Hosa Mmerari anali ndi ana awa: woyamba anali Simiri (ngakhale kuti iye sanali woyamba kubadwa, abambo ake anamusankha kuti akhale mtsogoleri), 11wachiwiri Hilikiya, wachitatu Tebaliya ndipo wachinayi Zekariya. Ana ndi abale onse a Hosa analipo 13.

12Magulu amenewa a alonda a pa zipata, motsogozedwa ndi atsogoleri awo, anali ndi ntchito yotumikira mʼNyumba ya Yehova, monga momwe amachitira abale awo. 13Iwo anachita maere mwa mabanja awo aangʼono ndi aakulu omwe kuti apeze mlonda pa chipata chilichonse.

14Maere a chipata chakummwa anagwera Selemiya. Maere anachitikanso chifukwa cha mwana wake Zekariya, phungu wanzeru ndipo maere a chipata chakumpoto anagwera iye. 15Maere a chipata chakummwera anagwera Obedi-Edomu, ndipo maere a nyumba yosungiramo katundu anagwera ana ake. 16Maere a chipata chakumadzulo ndi chipata cha Saleketi ku msewu wa ku mtunda anagwera Supimu ndi Hosa.

Mlonda ankayangʼanana ndi mlonda mnzake: 17Mbali ya kummawa kunkakhala Alevi 6 pa tsiku, kumpoto anayi pa tsiku, kummwera anayi pa tsiku ndipo awiri ankakhala pa nyumba yosungiramo katundu. 18Ndipo ku bwalo cha kumadzulo, anayi amakhala mu msewu ndi awiri pabwalo penipeni.

19Awa anali magulu a alonda a pa zipata amene anali zidzukulu za Kora ndi Merari.

Asungichuma ndi Akuluakulu Ena

20Abale awo Alevi, motsogozedwa ndi Ahiya, anali oyangʼanira chuma cha nyumba ya Mulungu ndi zinthu zoperekedwa kwa Mulungu.

21Adzukulu a Ladani, mmodzi mwa ana a Geresoni, amene anali atsogoleri a mabanja a Ageresoni, anali awa: Yehieli, 22ana a Yehieli, Zetamu ndi mʼbale wake Yoweli. Iwo amayangʼanira chuma cha ku Nyumba ya Mulungu wa Yehova.

23Kuchokera ku banja la Amramu, banja la Aizihara, banja la Ahebroni ndi banja la Auzieli:

24Subaeli, chidzukulu cha Geresomu, mwana wa Mose, anali mkulu woyangʼanira chuma. 25Abale ake obadwa mwa Eliezara, anali Rekabiya mwana wake, Yesaya mwana wake, Yoramu mwana wake, Zikiri mwana wake ndi Selomiti mwana wake. 26Selomiti ndi abale ake amayangʼanira zinthu zonse zoperekedwa kwa Mulungu ndi mfumu Davide, atsogoleri a mabanja amene anali olamulira ankhondo 1,000, olamulira ankhondo 100, ndi olamulira ankhondo ena. 27Zina zofunkha ku nkhondo anazipereka kuti zikhale zokonzera Nyumba ya Yehova. 28Ndipo zonse zimene zinaperekedwa ndi Mlosi Samueli, Sauli mwana wa Kisi, Abineri mwana wa Neri ndiponso Yowabu mwana wa Zeruya ndi zinthu zonse zimene zinkaperekedwa zimasungidwa ndi Selomiti ndi abale ake.

29Kuchokera ku banja la Izihari: Kenaniya ndi ana ake anapatsidwa ntchito kutali ndi Nyumba ya Mulungu ngati akuluakulu ndi oweruza Israeli.

30Kuchokera ku banja la Ahebroni: Hasabiya ndi abale ake, anthu anzeru 1,700. Iwo ankayangʼanira ntchito zonse za Yehova ndi ntchito yonse ya mfumu cha kumadzulo kwa Yorodani. 31Pa banja la Ahebroni, Yeriya anali mtsogoleri monga mwa mbiri ya mibado ya mabanja awo. Mʼchaka cha 40 cha ufumu wa Davide, panachitika kafukufuku ndipo ena mwa anthu aluso a banja la Hebroni anapezeka kuti anali ku Yazeri ku Giliyadi. 32Yeriya anali ndi abale 2,700 amene anali aluso ndiponso atsogoleri a mabanja. Mfumu Davide anawayika iwowa kuti aziyangʼanira fuko la Rubeni, fuko la Gadi ndi theka la fuko la Manase pa zinthu zonse za Mulungu ndi za mfumu.

Chinese Contemporary Bible (Simplified)

历代志上 26:1-32

圣殿的守卫

1以下是殿门守卫的班次:

可拉亚萨的后代有可利的儿子米施利米雅2米施利米雅的长子是撒迦利亚,次子是耶叠,三子是西巴第雅,四子是耶提聂3五子是以拦,六子是约哈难,七子是以利约乃4俄别·以东的长子是示玛雅,次子是约萨拔,三子是约亚,四子是沙甲,五子是拿坦业5六子是亚米利,七子是以萨迦,八子是毗乌利太。上帝特别赐福俄别·以东6他儿子示玛雅有几个儿子都很能干,在各自的家族中做首领。 7他们是俄得尼利法益俄备得以利萨巴。他们的亲族以利户西玛迦也很能干。 8这些都是俄别·以东的子孙,他们和他们的儿子及亲族共有六十二人,都是能干称职的人。 9米施利米雅的儿子及亲族共十八人,都很能干。 10米拉利的后代何萨的长子是申利,他本来不是长子,是被他父亲立为长子的。 11次子是希勒迦,三子是底巴利雅,四子是撒迦利亚何萨的儿子及亲族共十三人。

12这些按族长分成小组的殿门守卫在耶和华的殿里按班次供职,与他们的亲族一样。 13他们无论大小,都按照族系抽签,以决定看守哪个门。 14示利米雅抽中东门,他儿子撒迦利亚是个精明的谋士,抽中北门。 15俄别·以东抽中南门,他儿子抽中库房。 16书聘何萨抽中西门和上行之路的沙利基门,两班相对而立。 17每天有六个利未人守东门,四人守北门,四人守南门,守库房的二人一组。 18守卫西面街道的有四人,守卫走廊的有二人。 19以上是可拉的子孙和米拉利的子孙守门的班次。

圣殿里的其他职务

20利未亚希雅负责掌管上帝殿里的库房和放奉献之物的库房。 21革顺拉但的子孙中做族长的有耶希伊利22耶希伊利的两个儿子西坦约珥负责管理耶和华殿里的库房。 23暗兰族、以斯哈族、希伯仑族、乌歇族也各有其职。 24摩西的孙子——革舜的儿子细布业是库房的主管。 25细布业的亲族有以利以谢以利以谢的儿子是利哈比雅利哈比雅的儿子是耶筛亚耶筛亚的儿子是约兰约兰的儿子是细基利细基利的儿子是示罗密26示罗密及其亲族负责管理库房中的奉献之物,这些物品是大卫王、众族长、千夫长、百夫长和将领献给上帝的圣物。 27他们把战争中掳掠的财物献出来,以备建造耶和华的殿。 28撒母耳先见、基士的儿子扫罗尼珥的儿子押尼珥洗鲁雅的儿子约押及其他人奉献的圣物都由示罗密及其亲族管理。

29以斯哈族的基拿尼雅及其众子做官长和士师,为以色列管理圣殿以外的事务。 30希伯仑族的哈沙比雅及其亲族一千七百人都很能干,他们在以色列约旦河以西办理耶和华和王的事务。 31按家谱记载,希伯仑宗族的族长是耶利雅大卫执政第四十年,经过调查,在基列雅谢希伯仑族中找到一些能干的人。 32耶利雅的亲族有两千七百人,都是能干的族长。大卫王派他们在吕便支派、迦得支派和玛拿西半个支派中办理一切有关上帝和王的事务。