1 Mbiri 24 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Mbiri 24:1-31

Magulu a Ansembe

1Magulu a ana a Aaroni anali awa:

Ana a Aaroni anali Nadabu, Abihu, Eliezara ndi Itamara. 2Koma Nadabu ndi Abihu anamwalira abambo awo asanamwalire, ndipo analibe ana aamuna. Kotero Eliezara ndi Itamara ankatumikira monga ansembe. 3Mothandizidwa ndi Zadoki chidzukulu cha Eliezara ndi Ahimeleki chidzukulu cha Itamara, Davide anawagawa mʼmagulu molingana ndi ntchito yawo yotumikira. 4Atsogoleri ambiri anapezeka pakati pa zidzukulu za Eliezara kusiyana ndi zidzukulu za Itamara ndipo anagawidwa moyenera: atsogoleri 16 a mabanja ochokera kwa Eliezara, ndipo atsogoleri asanu ndi atatu a mabanja ochokera kwa zidzukulu za Itamara. 5Anawagawa mosakondera pochita maere, pakuti iwo anali akuluakulu a ku malo opatulika ndi akuluakulu a Mulungu pakati pa zidzukulu za Eliezara ndi Itamara.

6Mlembi Semaya mwana wa Netaneli, Mlevi, analemba mayina awo pamaso pa mfumu ndi akuluakulu ake: wansembe Zadoki, Ahimeleki mwana wa Abiatara ndi atsogoleri a mabanja a ansembe ndiponso Alevi, banja limodzi kuchokera kwa Eliezara kenaka limodzi kuchokera kwa Itamara.

7Maere woyamba anagwera Yehoyaribu,

achiwiri anagwera Yedaya,

8achitatu anagwera Harimu,

achinayi anagwera Seorimu,

9achisanu anagwera Malikiya,

achisanu ndi chimodzi anagwera Miyamini,

10achisanu ndi chiwiri anagwera Hakozi,

achisanu ndi chitatu anagwera Abiya,

11achisanu ndi chinayi anagwera Yesuwa,

a khumi anagwera Sekaniya,

12a 11 anagwera Eliyasibu,

a 12 anagwera Yakimu,

13a 13 anagwera Hupa,

a 14 anagwera Yesebeabu,

14a 15 anagwera Biliga,

a 16 anagwera Imeri,

15a 17 anagwera Heziri,

a 18 anagwera Hapizezi,

16a 19 anagwera Petahiya,

a 20 anagwera Ezekieli,

17a 21 anagwera Yakini,

a 22 anagwera Gamuli,

18a 23 anagwera Delaya,

ndipo a 24 anagwera Maaziya.

19Umu ndi mmene anasankhidwira kuti azigwira ntchito yotumikira pamene alowa mʼNyumba ya Yehova, motsatira dongosolo limene anapatsidwa ndi kholo lawo Aaroni, monga momwe Yehova Mulungu wa Israeli anamulamulira.

Alevi Ena Onse

20Za zidzukulu zina zonse za Levi:

Kuchokera kwa ana a Amramu: Subaeli;

kuchokera kwa ana a Subaeli: Yehideya.

21Kwa Rehabiya, kuchokera kwa ana ake:

Mtsogoleri anali Isiya.

22Kuchokera ku banja la Izihari: Selomoti;

kuchokera kwa ana a Selomoti: Yahati.

23Ana a Hebroni: woyamba anali Yeriya, wachiwiri anali Amariya, wachitatu anali Yahazieli ndipo Yekameamu anali wachinayi.

24Mwana wa Uzieli: Mika;

kuchokera kwa ana a Mika: Samiri.

25Mʼbale wa Mika: Isiya;

kuchokera kwa ana a Isiya: Zekariya.

26Ana a Merari: Mahili ndi Musi.

Mwana wa Yaaziya: Beno.

27Ana a Merari:

Kuchokera kwa Yaaziya: Beno, Sohamu, Zakuri ndi Ibiri.

28Kuchokera kwa Mahili: Eliezara, amene analibe ana aamuna.

29Kuchokera kwa Kisi:

Mwana wa Kisi: Yerahimeeli.

30Ndipo ana a Musi: Mahili, Ederi ndi Yerimoti.

Awa anali Alevi potsata mabanja a makolo awo. 31Iwonso anachita maere, monga anachitira abale awo, zidzukulu za Aaroni, pamaso pa mfumu Davide, ndi Zadoki ndi Ahimeleki, atsogoleri a mabanja a ansembe ndi Alevi. Mabanja a mwana wamkulu anachita nawo mofanana ndi a mwana wamngʼono.