1 Mbiri 21 – CCL & CCBT

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Mbiri 21:1-30

Davide Awerenga Ankhondo Ake

1Satana anafuna kuvutitsa Aisraeli choncho anawutsa mtima wa Davide kuti awerenge Aisraeli. 2Choncho Davide anati kwa Yowabu pamodzi ndi atsogoleri a ankhondo, “Pitani mukawerenge Aisraeli kuyambira ku Beeriseba mpaka ku Dani. Ndipo mudzandiwuze kuti ndidziwe chiwerengero chawo.”

3Yowabu anayankha kuti, “Yehova achulukitse ankhondo ake kukhala miyandamiyanda. Mbuye wanga mfumu, kodi anthu onsewa sali pansi panu? Nʼchifukwa chiyani mbuye wanga mukufuna kuchita zimenezi? Nʼchifukwa chiyani mukufuna kuchimwitsa Israeli?”

4Komabe mawu a mfumu anapambana mawu a Yowabu, kotero Yowabu anapita mu Israeli monse ndipo kenaka anabwera ku Yerusalemu. 5Yowabu anapereka chiwerengero cha anthu ankhondo kwa Davide: Mu Israeli monse munali anthu ankhondo 1,100,000 amene amadziwa kugwiritsa ntchito lupanga, kuphatikizapo anthu 470,000 a fuko la Yuda.

6Koma Yowabu sanaphatikizepo fuko la Levi ndi fuko la Benjamini pa chiwerengerochi, pakuti lamulo la mfumu linamuyipira. 7Lamulo limeneli silinakomerenso Mulungu. Kotero Iye analanga Israeli.

8Choncho Davide anati kwa Mulungu, “Ine ndachimwa kwambiri pa zimene ndachita. Tsono ndikupempha kuti mukhululuke kulakwa kwa mtumiki wanu. Ine ndachita zopusa kwambiri.”

9Yehova anati kwa Gadi, mlosi wa Davide, 10“Pita ukamuwuze Davide kuti, ‘Yehova akuti, Ine ndikukupatsa zinthu zitatu izi. Usankhepo chimodzi pa zimenezi choti ndikuchitire.’ ”

11Choncho Gadi anapita kwa Davide ndipo anati kwa Iye, “Yehova akuti, ‘Musankhepo chimene mungakonde kuti chichitike: 12mʼdziko mukhale njala zaka zitatu, mukhale mukuthawa adani anu kwa miyezi itatu, akukukanthani ndi lupanga la Yehova, kapena mʼdziko mukhale mliri kwa masiku atatu, mngelo wa Yehova akuwononga Israeli yense.’ Ndipo tsono ganizirani bwino chomwe ndikamuyankhe amene wandituma.”

13Davide anati kwa Gadi, “Ine ndavutika kwambiri mu mtima mwanga. Ine andilange ndi Yehova, pakuti chifundo chake ndi chachikulu kwambiri; koma ndisalangidwe ndi anthu.”

14Choncho Yehova anabweretsa mliri pa Aisraeli, ndipo unapha Aisraeli 70,000. 15Ndipo Mulungu anatumiza mngelo kuti awononge Yerusalemu. Koma pamene mngeloyo amachita zimenezi, Yehova anaona ndipo anavutika mu mtima chifukwa cha zowawazo ndipo anati kwa mngelo amene ankawononga anthu uja, “Basi kwakwanira! Leka kuwononga.” Nthawi imeneyo mngelo wa Yehova anali atayima pamalo opunthira tirigu a Arauna Myebusi.

16Davide anakweza maso ake ndipo anaona mngelo wa Yehova atayima pakati pa dziko lapansi ndi kumwamba, mʼdzanja lake muli lupanga lotambalitsa kuloza ku Yerusalemu. Ndipo Davide ndi akuluakulu, atavala ziguduli, anadzigwetsa pansi chafufumimba.

17Davide anati kwa Mulungu, “Kodi si ine amene ndinalamula kuti ankhondo awerengedwe? Ine mʼbusa ndi amene ndachimwa, ndiye ndachita zoyipa. Anthuwa ali ngati nkhosa zosalakwa. Kodi iwowa achita chiyani? Inu Yehova Mulungu wanga, langani ineyo pamodzi ndi banja langa, koma musalole kuti mliriwu ukhale pa anthu anuwa.”

18Pamenepo mngelo wa Yehova analamula Gadi kuti awuze Davide kuti akamange guwa lansembe la Yehova pamalo opunthira tirigu a Arauna Myebusi. 19Ndipo Davide anapita pomvera mawu amene Gadi ananena mʼdzina la Yehova.

20Pamene Arauna ankapuntha tirigu, anatembenuka ndipo anaona mngelo ndipo ana ake anayi aamuna amene anali naye anabisala. 21Davide anayandikira, ndipo Arauna atayangʼana ndi kumuona, anachoka popunthira tirigupo ndipo anawerama nagunditsa nkhope yake pansi pamaso pa Davide.

22Davide anati kwa Arauna, “Undipatse malo ako opunthira tirigu kuti ndimangire Yehova guwa lansembe, kuti mliri uli pa anthuwa usiye. Undigulitse ine pa mtengo woyenera ndithu.”

23Arauna anati kwa Davide, “Tengani! Mbuye wanga mfumu achite chomukomera. Taonani ine ndidzapereka ngʼombe zazimuna za nsembe yopsereza, zopunthira tirigu zidzakhala nkhuni ndipo tiriguyu adzakhala chopereka chachakudya. Ndidzapereka zonsezi.”

24Koma mfumu Davide inayankha Arauna kuti, “Ayi, ine ndikuti ndipereka mtengo wathunthu. Sindingatenge chinthu chako ndi kuchipereka kwa Yehova, kapena kupereka nsembe imene sindinayigule.”

25Choncho Davide analipira Arauna masekeli agolide 600 chifukwa cha malowo. 26Davide anamangira Yehova guwa lansembe pamenepo ndipo anaperekapo nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano. Iye anapemphera kwa Yehova, ndipo Yehova anayankha potumiza moto pa guwa lansembe zopsereza kuchokera kumwamba.

27Tsono Yehova anayankhula kwa mngelo, ndipo analowetsa lupanga lake mʼchimake. 28Pa nthawi imeneyo, Davide ataona kuti Yehova wamuyankha pa malo opunthira tirigu a Arauna Myebusi, anapereka nsembe pamenepo. 29Tenti ya Yehova imene Mose anapanga mʼchipululu, ndi guwa lansembe zopsereza pa nthawi imeneyi zinali pa phiri ku Gibiyoni. 30Koma Davide sanathe kupita kumeneko kuti akapemphere pamaso pa Yehova, chifukwa amaopa lupanga la mngelo wa Yehova.

Chinese Contemporary Bible (Traditional)

歷代志上 21:1-30

大衛統計人口

1撒旦為了攻擊以色列,就挑動大衛統計以色列人的數目。 2大衛約押和其他軍中的首領說:「你們要走遍以色列,從別示巴一直到,統計以色列的人口,然後回來稟告我,我好知道他們的數目。」 3約押說:「願耶和華使祂子民的人數比現在增加百倍。但我主我王啊,他們不都是你的僕人嗎?我主為什麼要這樣做,使以色列人陷於罪中呢?」 4大衛不聽約押的規勸。約押只好出去,走遍以色列,然後回到耶路撒冷5將人數呈報大衛:全以色列有一百一十萬刀兵,猶大有四十七萬。 6約押沒有把利未人和便雅憫人算在其中,因為他厭惡王的這個命令。 7上帝也不喜悅這事,便降災給以色列人。 8大衛對上帝說:「我做這事犯了大罪。求你赦免僕人的罪,我做了極其愚昧的事。」 9耶和華對大衛的先見迦得說: 10「你去告訴大衛,我有三樣災禍,他可以選擇讓我降哪一樣給他。」

11迦得就來見大衛,把耶和華的話告訴他,說:「你可以任選一樣, 12或三年的饑荒,或被敵人追殺三個月,或國中遭三天的瘟疫,讓耶和華的天使在以色列全境施行毀滅。請你考慮好後告訴我,我好回覆那差我來的。」 13大衛說:「我實在為難!不過我寧願落在耶和華的手中,也不願落在人的手中,因為耶和華有無限的憐憫。」

14於是,耶和華在以色列降下瘟疫,有七萬人死亡。 15上帝差遣天使去毀滅耶路撒冷。天使正要毀滅的時候,耶和華見了就心生憐憫,對施行毀滅的天使說:「夠了,住手吧!」當時,耶和華的天使正站在耶布斯阿珥楠的麥場上。 16大衛舉目看見耶和華的天使站在天地之間,手握著已出鞘的刀,指向耶路撒冷大衛和眾長老都身披麻衣,臉伏於地。 17大衛對上帝說:「吩咐統計人民數目的不是我嗎?是我犯了罪,做了惡事,這些百姓有什麼過錯呢?我的上帝耶和華啊,願你的手懲罰我和我的家族,不要把瘟疫降在你的子民身上。」

18耶和華的天使吩咐迦得去告訴大衛耶布斯阿珥楠的麥場上為耶和華建一座祭壇。 19大衛照耶和華藉迦得所說的話去了麥場。 20那時,阿珥楠正在打麥子,他轉身看見了天使,跟他在一起的四個兒子都躲了起來。 21阿珥楠看見大衛來了,就從麥場出來,俯伏叩拜大衛22大衛對他說:「請你將這塊麥場賣給我,我要在這裡為耶和華築一座祭壇,好止住民間的瘟疫。你全價賣給我吧。」 23阿珥楠說:「我主我王只管用我的麥場!我願獻出牛作燔祭,打麥的器具作柴,麥子作素祭,我願獻出這一切。」

24大衛王說:「不可,我一定要付你全價,我不能拿你的東西獻給耶和華,不能把白白得來的獻作燔祭。」 25於是,大衛就用七公斤金子買了阿珥楠的麥場。 26大衛在那裡為耶和華建了一座壇,獻上燔祭和平安祭,並求告耶和華。耶和華垂聽了他的禱告,從天上降火在祭壇上, 27又命令天使收刀入鞘。

28大衛見耶和華在耶布斯阿珥楠的麥場上應允了他的禱告,就在那裡獻祭。 29那時候,摩西在曠野為耶和華所造的聖幕和燔祭壇都在基遍的高地。 30大衛因為懼怕耶和華天使的刀,不敢去那裡求問上帝。