1 Mbiri 19 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Mbiri 19:1-19

Davide Achita Nkhondo ndi Aamoni

1Patapita nthawi Nahasi mfumu ya Aamoni inamwalira, ndipo mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake. 2Davide anaganiza kuti, “Ine ndidzachitira chifundo Hanuni mwana wa Nahasi chifukwa abambo ake anandichitira zabwino.” Choncho Davide anatumiza anthu kuti akamupepesere kwa Hanuni chifukwa cha imfa ya abambo ake.

Anthu amene Davide anawatuma atafika kwa Hanuni mʼdziko la Aamoni kudzamupepesa, 3atsogoleri a ankhondo a Aamoni anawuza Hanuni kuti, “Kodi mukuganiza kuti Davide akupereka ulemu kwa abambo anu potumiza anthuwa kwa inu kudzapepesa? Kodi anthuwa sanawatumize kuti adzaone dziko lathu ndi kuchita ukazitape ndi cholinga chofuna kuwulanda?” 4Choncho Hanuni anagwira anthu amene Davide anawatuma aja ndipo anawameta ndi kudula zovala zawo pakati mʼchiwuno mpaka matako kuonekera ndipo anawabweza kwawo.

5Munthu wina atafika ndi kufotokozera Davide za anthuwo, iye anatuma amithenga kukakumana nawo, chifukwa anali ndi manyazi kwambiri. Mfumu inati, “Mukhale ku Yeriko mpaka ndevu zanu zitakula, ndipo kenaka mubwere kuno.”

6Aamoni atazindikira kuti amukwiyitsa kwambiri Davide, Hanuni ndi Aamoni anatumiza siliva wolemera makilogalamu 34,000 kuti akalipirire magaleta ndi okwerapo ake a ku Mesopotamiya; Aramu-Maaka ndi Zoba. 7Iwo analipira magaleta okwanira 32,000, pamodzi ndi mfumu ya ku Maaka ndi ankhondo ake. Amenewa anabwera ndi kudzamanga misasa yawo pafupi ndi Medeba. Nawonso Aamoni anabwera kuchokera ku mizinda yawo ndipo anapita kukachita nkhondo.

8Davide atamva zimenezi, anatumiza Yowabu ndi gulu lonse la ankhondo amphamvu. 9Aamoni anatuluka ndi kukhala mʼmizere ya nkhondo pa chipata cha mzinda wawo, pamene mafumu amene anabwera nawo anali kwa wokha, ku malo wopanda mitengo.

10Yowabu ataona kuti kunali mizere ya ankhondo kutsogolo kwake ndi kumbuyo kwake; iye anasankha ena mwa ankhondo a Israeli odziwa kuchita bwino nkhondo ndipo anawayika kuti amenyane ndi Aaramu. 11Iye anayika ankhondo ena otsalawo mʼmanja mwa Abisai mʼbale wake ndipo anawayika kuti amenyane ndi Aamoni. 12Yowabu anati, “Ngati Aaramu andipose mphamvu, iwe ubwere udzandipulumutse; koma ngati Aamoni akupose mphamvu, ine ndidzabwera kudzakupulumutsa. 13Limba mtima ndipo timenyane nawo mopanda mantha chifukwa cha anthu athu ndi mizinda ya Mulungu wathu. Yehova achite chomukomera pamaso pake.”

14Choncho Yowabu ndi ankhondo amene anali naye anapita kukamenyana ndi Aaramu, ndipo iwo anathawa pamaso pake. 15Aamoni atazindikira kuti Aaramu akuthawa, iwo anathawanso pamaso pa Abisai mʼbale wake ndi kulowa mu mzinda. Motero Yowabu anabwerera ku Yerusalemu.

16Aaramu ataona kuti agonjetsedwa ndi Aisraeli, anatumiza amithenga kukayitana Aaramu amene anali ku tsidya la Mtsinje, pamodzi ndi mtsogoleri wa ankhondo wa Hadadezeri, Sofaki akuwatsogolera.

17Davide atawuzidwa zimenezi, iye anasonkhanitsa Aisraeli onse ndi kuwoloka Yorodani. Iyeyo anapita kukakumana nawo ndipo anakhala mʼmizere yankhondo moyangʼanana ndipo iwo anamenyana naye. 18Koma iwo anathawa pamaso pa Aisraeli, ndipo Davide anapha anthu okwera pa magaleta 7,000 ndi ankhondo oyenda pansi 40,000. Iye anaphanso Sofaki, mtsogoleri wawo wankhondo.

19Mafumu amene ali pansi pa Hadadezeri ataona kuti agonjetsedwa ndi Aisraeli, anachita mtendere ndi Davide ndipo anakhala pansi pa ulamuliro wake.

Motero Aaramu anaopa kuthandizanso Aamoni.