1 Mbiri 17 – CCL & CCB

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Mbiri 17:1-27

Lonjezo la Mulungu kwa Davide

1Davide atakhazikika mʼnyumba yake yaufumu, anawuza mneneri Natani kuti, “Ine pano ndikukhala mʼnyumba yaufumu yomanga ndi mitengo ya mkungudza, pomwe Bokosi la Chipangano la Yehova lili mu tenti.”

2Natani anayankha Davide kuti, “Chitani chilichonse chimene chili mu mtima mwanu, chifukwa Mulungu ali nanu.”

3Usiku umenewo mawu a Mulungu anafika kwa Natani, ndipo anati,

4“Pita kamuwuze mtumiki wanga Davide kuti, ‘Yehova akunena kuti, sudzandimangira ndiwe nyumba yokhalamo.’ 5Ine sindinakhalepo mʼnyumba kuyambira tsiku limene ndinatulutsa Israeli mʼdziko la Igupto mpaka lero lino. Ndakhala ndikuyenda kuchoka mʼtenti ina kupita mʼtenti ina, kuchoka malo ena kupita malo ena. 6Konse ndakhala ndikuyenda ndi Aisraeli onse, kodi ndinanenapo kwa wina aliyense wa atsogoleri awo amene ndinamulamula kuweta anthu anga kuti, ‘Kodi nʼchifukwa chiyani simunandimangire nyumba ya mitengo ya mkungudza?’ ”

7Ndipo tsopano umuwuze mtumiki wanga Davide kuti, “Yehova Wamphamvuzonse akuti, Ine ndinakutenga ku busa ukuweta nkhosa, kuti ukhale mtsogoleri wa anthu anga, Aisraeli. 8Ineyo ndinali nawe kulikonse kumene unkapita, ndipo ndachotsa adani ako onse pamaso pako. Tsopano ndidzakuza dzina lako kuti likhale mʼgulu la mayina a anthu otchuka kwambiri pa dziko lapansi. 9Ndipo ndidzawapatsa malo anthu anga, Aisraeli ndipo ndidzawadzala pamalo awoawo kuti asadzavutitsidwenso. Anthu oyipa sadzawazunzanso monga ankachitira poyamba paja; 10monga akhala akuchitira kuchokera nthawi imene ndinasankha atsogoleri a anthu anga Aisraeli. Ine ndidzagonjetsanso adani anu onse.

“ ‘Ine ndikulengeza kwa iwe kuti Yehova adzakhazikitsa banja lako. 11Masiku ako akadzatha ndipo ukadzatsatira makolo ako, Ine ndidzawutsa mphukira yako imene idzalowa mʼmalo mwako, mmodzi mwa ana ako, ndipo ndidzakhazikitsa ufumu wake. 12Iye ndiye amene adzandimangira nyumba, ndipo ndidzakhazikitsa ufumu wake kwamuyaya. 13Ine ndidzakhala abambo ake, ndipo iye adzakhala mwana wanga. Ine sindidzasiya kumukonda monga ndinachitira ndi amene unalowa mʼmalo mwawo. 14Ndidzamuyika kukhala wolamulira nyumba yanga ndi ufumu wanga kwamuyaya. Mpando wake waufumu udzakhazikika kwamuyaya.’ ”

15Natani anafotokozera Davide mawu onse avumbulutso limene analandira.

Pemphero la Davide

16Choncho Mfumu Davide analowa mu tenti nakhala pamaso pa Yehova, ndipo anati,

“Ine ndine yani, Inu Yehova Mulungu, ndipo banja langa nʼchiyani kuti mundifikitse pamene ndafikapa? 17Inu Mulungu, kukhala ngati izi ndi zosakwanira pamaso panu, Inuyo mwayankhula zatsogolo la banja la mtumiki wanu. Mwandiyangʼana ndipo mwandiyesa ngati munthu wolemekezeka kwambiri pakati pa anthu, Inu Yehova Mulungu.”

18“Kodi Davide anenenso chiyani kwa Inu, pakuti mwachitira ulemu wotere mtumiki wanu? Pakuti Inu mukumudziwa mtumiki wanu. 19Inu Yehova, chifukwa cha mtumiki wanu komanso mwa chifuniro chanu, mwachita chinthu chachikulu ichi ndipo mwawulula malonjezo anu aakulu onse.

20“Palibe wina wofanana nanu, Inu Yehova, ndipo palibe Mulungu wina koma Inu nokha monga tamvera ndi makutu athu. 21Ndipo ndi ndani wofanana ndi anthu anu Aisraeli, mtundu wokhawo pa dziko lapansi umene Mulungu wake anapita kukawuwombola, monga anthu akeake ndi kukadzitchukitsa yekha pochita zinthu zodabwitsa zazikulu, pothamangitsa mitundu ina pamaso pa anthu ake, amene Inu munawawombola ku Igupto? 22Inu munawapanga anthu anu Aisraeli kukhala anuanu kwamuyaya, ndipo Inu, Inu Yehova ndinu Mulungu wawo.

23“Ndipo tsopano Yehova, sungani kwamuyaya lonjezo limene mwachita ndi mtumiki wanu ndi banja lake, likhazikitseni kwamuyaya. Chitani monga mwalonjezera, 24kotero dzina lanu likhazikike ndi kukhala lotchuka mpaka muyaya. Ndipo anthu adzanena kuti, ‘Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa woyangʼanira Israeli, ndi Mulungu wa Israeli!’ Ndipo banja la mtumiki wanu Davide lidzakhazikika pamaso panu.

25“Inu Mulungu wanga, mwaululira mtumiki wanu kuti mudzamumangira nyumba. Nʼchifukwa chake ine mtumiki wanu ndalimba mtima kupemphera motere. 26Inu Yehova, ndinu Mulungu! Mwalonjeza zinthu zabwinozi kwa mtumiki wanu. 27Ndipo chakukomerani kudalitsa banja la mtumiki wanu kuti likhale pamaso panu mpaka muyaya. Pakuti Inu Yehova mwalidalitsa, lidzakhala lodalitsika mpaka muyaya.”

Chinese Contemporary Bible (Simplified)

历代志上 17:1-27

上帝对大卫的应许

1大卫住进宫殿后,对拿单先知说:“你看,我住在香柏木建的王宫中,耶和华的约柜却在帐篷里。” 2拿单大卫说:“你有什么想法,就去做吧!因为上帝与你同在。”

3当晚,上帝对拿单说: 4“你去告诉我的仆人大卫,‘耶和华说,你不是为我建造殿宇的人。’ 5从我把以色列人带出埃及那天起直到今天,我从未住过殿宇,都住在四处迁移的帐篷里。 6在我与以色列人同行的日子,我从未责问任何我委派牧养我子民的士师,‘你为何不为我建造香柏木的殿宇呢?’

7“现在你要告诉我的仆人大卫,‘万军之耶和华说,你原本在草场牧羊,我召你来做我以色列子民的首领。 8无论你去哪里,我都与你同在,为你铲除所有仇敌。现在我要使你声名远播,与世上的伟人齐名。 9-10我必为我的以色列子民预备一个地方,栽培他们,使他们住在自己的家园,不再受惊扰,不会像从前我设立士师治理他们的时候那样受恶人压迫。我必制服你所有的仇敌,我耶和华向你宣告,我必建立你的王朝。 11你离世归到祖先那里的时候,我必使你的一位后裔继承你的王位,使他的国坚立。 12他要为我建造殿宇,我必使他王位永固。 13我要做他的父亲,他要做我的儿子。我的慈爱曾离开在你之前的扫罗王,但我的慈爱必不离开他。 14我要使他永远治理我的家和我的国。他的王位必永远稳固。’” 15拿单就把所听到的启示全部告诉大卫

大卫的祷告

16于是,大卫王走进会幕,在耶和华面前坐下,说:“耶和华上帝啊,我是谁?我的家算什么?你竟如此厚待我。 17上帝啊,不止如此,你还应许将来要恩待仆人的后裔。耶和华上帝啊,你视我为尊贵的人。 18你将尊荣加于仆人,我还能说什么?因为你了解仆人。 19耶和华啊,你按照自己的心意为仆人成就这大事,并显明出来。 20耶和华啊,我们从未听过有谁能与你相比,你是独一无二的上帝。 21世上有谁能与你的以色列子民相比?你从埃及救赎他们,让他们做你的子民,为他们驱逐外族人、行伟大奇妙的事,使自己声名远播。 22你让以色列人永远做你的子民,你耶和华做他们的上帝。

23“耶和华啊,愿你永远信守你对仆人和仆人家的应许,愿你成就自己的应许。 24这样,你的名必永远坚立,被尊崇,人们必说,‘以色列的上帝——万军之耶和华是以色列的上帝’,你仆人大卫的家必在你面前坚立。 25我的上帝啊,因为你曾启示仆人,说要为仆人建立王朝,仆人才敢这样向你祈求。 26耶和华啊,唯独你是上帝,你应许要将这福气赐给仆人。 27愿你赐福仆人的王朝,使它在你面前永远坚立。耶和华啊,你已赐下祝福,你的祝福是永远的!”